Mas. 35 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero lopempha chithandizoSalmo la Davide.

1Inu Chauta, mulimbane nawo anthu olimbana nane,

Mumenyane nawo omenyana nane.

2Gwirani chishango ndi lihawo,

ndipo fulumirani mundithandize.

3Tengani mkondo ndi nthungo,

kuti mulimbane nawo anthu ondilondola.

Uzani mtima wanga kuti,

“Mpulumutsi wako ndine.”

4Anyozeke ndi kuchita manyazi

onse ofunafuna moyo wanga.

Abwezeni m'mbuyo ndipo athaŵe chinambalala

amene apangana kuti andichite choipa.

5Akhale ngati mankhusu ouluka ndi mphepo,

pamene mngelo wa Chauta akuŵapirikitsa.

6Njira yao ikhale yamdima ndi yoterera,

pamene mngelo wa Chauta akuŵalondola.

7Adaniwo adanditchera ukonde popanda chifukwa,

adandikumbira mbuna ine munthu wosachimwa.

8Aonongeke pamene iwo sakuyembekeza.

Akodwe mu ukonde wotcha okha,

agwere m'mbuna yokumba iwo omwe.

9Motero mtima wanga udzakondwa motamanda Chauta,

kukondwerera kuti wandipulumutsa.

10Ndidzasangalala ndi mtima wonse

ndi kunena kuti.

“Ndani angafanefane ndi Inu Chauta,

Inu amene mumapulumutsa munthu wofooka

kwa munthu wopambana pa mphamvu,

Inu amene mumapulumutsa munthu wofooka ndi wosoŵa

kwa munthu wolanda zinthu zake?”

11Mboni zoipa zikundiwukira,

zikundifunsa zinthu zimene sindikuzidziŵa.

12Zikundibwezera zoipa pa zabwino,

ndipo mtima wanga uli ndi chisoni chokhachokha.

13Koma ine pamene adani anga analikudwala,

ndidavala chiguduli kuwonetsa chisoni.

Ndidadzilanga posala zakudya.

Ndidapemphera nditaŵeramitsa mutu wanga pa chifuŵa,

14monga ngati ndikuchitira chisoni bwenzi langa

kapena mbale wanga.

Ndinkayenda khumakhuma

ngati munthu wolira maliro a mai wake,

nditaŵerama ndi kumalira.

15Koma ine nditagwa m'mavuto,

iwo aja adasonkhana akusangalala.

Adandisonkhanira onse pamodzi,

anthu achabechabe amene sindidaŵadziŵe nkomwe,

ndipo ankangondisinjirira.

16Anthuwo ankapitirira kundinyodola mwachipongwe,

namandikukutira mano ao.

17Inu Chauta, mudzakhala mpaka liti mukungoyang'ana?

Landitseni kwa anthu ofuna kundiwononga,

mupulumutse moyo wanga ku mikangoyi.

18Tsono ndidzakuthokozani pa msonkhano waukulu,

ndidzakutamandani pa chinamtindi cha anthu anu.

19 Mas. 69.4; Yoh. 15.25 Musalole kuti adani anga onyenga akondwere

chifukwa cha mavuto anga,

musalole kuti amene amandida popanda chifukwa,

andiyang'ane cham'mbali mondinyoza.

20Iwo salankhula za mtendere,

koma amangoganiza zonamizira okonda za mtendere pa dziko.

21Amandiseka mofuula namanena kuti,

“Ha! Maso athu apenyadi zimene zidachitikazo.”

22Inu Chauta, amene mwaona zimenezi,

musakhale chete.

Musakhale kutali ndi ine, Inu Ambuye.

23Tiyeni, Inu Chauta, dzukani

kuti munditchinjirize pa mlandu wanga,

Inu Mulungu wanga ndi Ambuye anga.

24Chauta, Mulungu wanga, chifukwa cha kulungama kwanu,

onetsani kuti ine ndine wosalakwa,

ndipo musalole kuti adani anga akondwere

chifukwa cha mavuto anga.

25Musalole kuti mumtima mwao anene kuti,

“Inde, ndizo zimene timafuna.”

Asanene kuti, “Tamgonjetsa.”

26Amene amakondwera poona kuti ndili pa mavuto,

muŵachititse manyazi,

muŵasokoneze kwathunthu.

Amene amayesa kuti akupambana ine,

achite manyazi ndipo anyozeke.

27Koma amene amafunitsitsa kuti ndipezeke wosalakwa,

afuule ndi chimwemwe ndipo asangalale.

Anene nthaŵi zonse kuti,

“Chauta ndi wamkulu.

Amakondwera akaona mtumiki wake zamuyendera bwino.”

28Tsono nanenso ndidzalalika za kulungama kwanu.

Ndidzakutamandani masiku onse, Inu Chauta.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help