1Nthaŵi yoti Davide amwalire itayandikira, adauza mwana wake Solomoni kuti,
2“Ine ndi ulendo uno, nchifukwa chake tsono khala wamphamvu ndipo ulimbike mtima.
3Uzichita zimene Chauta Mulungu wako akulamula. Uziyenda m'njira za Chauta, uzimvera mau, malangizo ndi malamulo a Mulungu, monga momwe adalembedwera m'malamulo a Mose, kuti zonse zizikuyendera bwino kulikonse kumene ungapite.
4Uzitero kuti Chauta achitedi zimene adalankhula za ine kuti, ‘Ana ako aamuna akamasamala makhalidwe ao ndi kukhala okhulupirika kwa Ine ndi mtima wao wonse ndi mzimu wao wonse, sipadzasoŵa munthu pa banja lako wolamulira Israele.’
5 2Sam. 3.27; 2Sam. 20.10 “Kuwonjezera pamenepo, ukudziŵanso zoipa zimene Yowabu mwana wa Zeruya adandichita, pakupha atsogoleri aŵiri a ankhondo a Aisraele aja, Abinere mwana wa Nere, ndi Amasa mwana wa Yetere. Kuteroko kunali kulipsira pa nthaŵi yamtendere magazi amene anthuwo adaakhetsa pa nthaŵi yankhondo. Koma tsopano ine pokhala mfumu, ndikusenza kuchimwa kwake ndi kuvala mlandu chifukwa cha magazi osachimwawo.
6Tsono iwe uchite potsata nzeru zako, koma ndithu usalole kuti afe ndi ukalamba ndi kupita ku manda mwamtendere.
7 2Sam. 17.27-29 “Koma ana a Barizilai wa ku Giliyadi, uŵachitire zabwino ndi kuŵalola kuti azidya pamodzi nawe, poti adandichitira chifundo pamene adakumana nane nthaŵi imene ndinkathaŵa Abisalomu mbale wako.
8 2Sam. 16.5-13; 19.16-23 “Palinso Simei, mwana wa Gera, Mbenjamini wa ku Bahurimu, amene adaanditukwana momvetsa chisoni, tsiku limene ndinkapita ku Mahanaimu. Koma pamene adadza kudzakumana nane ku Yordani, ndidalumbira m'dzina la Chauta kuti sindidzamupha.
9Nchifukwa chake tsono usamuyese wosalakwa, poti iwe ndiwe munthu wanzeru. Udzadziŵa wekha choyenera kumchita. Ngakhale ndi nkhalamba, aphedwe ndithu.”
10Tsono Davide adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wake wa Davideyo.
112Sam. 5.4, 5; 1Mbi. 3.4 Apo nkuti atalamulira Israele zaka makumi anai. Ku Hebroni adalamulira zaka zisanu ndi ziŵiri, ndipo ku Yerusalemu zaka 33.
121Mbi. 29.23 Choncho Solomoni adakhala pa mpando waufumu wa Davide atate ake. Ndipo ufumu wake unali wokhazikika kwambiri.
Kufa kwa Adoniya13Tsiku lina Adoniya, mwana wa Hagiti, adafika kwa Bateseba, mai wake wa Solomoni. Bateseba adamufunsa kuti, “Kodi wadzera mtendere?” Iye adati, “Ai, ndi zamtendere ndithu.”
14Tsono adati, “Koma ndili ndi mau oti ndilankhule nanu.” Bateseba adati, “Lankhula.”
15Adoniya adati, “Mukudziŵa kuti ufumuwu udaali wanga, ndipo Aisraele onse ankayembekeza kuti ndidzalamulira ndine. Koma zinthu zatembenuka, ufumuwo wapita kwa mbale wanga, popeza kuti adampatsa ndi Chauta.
16Tsopano ndikukupemphani chinthu chimodzi. Musandikanize ai.” Bateseba adati, “Nena.”
171Maf. 1.3, 4 Iyeyo adati, “Inuyo mfumu Solomoni sakukanizani, ndiye chonde ndimati mumpemphe kuti andipatse Abisagi, mtsikana wa ku Sunamu uja, kuti akhale mkazi wanga.”
18Bateseba adati, “Chabwino. Ndikulankhulira kwa mfumu.”
19Choncho Bateseba adapita kwa mfumu Solomoni kukalankhula naye m'malo mwa Adoniya. Solomoni adanyamuka kuti akumane naye, ndipo adaŵeramira mai wakeyo. Adakhala pa mpando wake waufumu, ndipo adaitanitsa mpando wina kuti mai wake akhalepo. Tsono mai uja adakhala ku dzanja lamanja la mfumuyo.
20Ndipo maiyo adati, “Ndikufuna kukupemphani kanthu kakang'ono. Chonde musandikanize.” Tsono mfumu idauza mai wakeyo kuti, “Pemphani chimene mukufuna, mai wanga, sindikukanizani.”
21Maiyo adati, “Mulole kuti Abisagi Msunamu uja apatsidwe kwa Adoniya mbale wanu, kuti akhale mkazi wake.”
22Mfumu Solomoni adafunsa mai wakeyo kuti, “Chifukwa chiyani mukumpemphera Abisagi Msunamu Adoniyayu? Mpemphereninso ndi ufumu womwe, poti iyeyu ndi mkulu wanga, ndipo akugwirizana ndi wansembe Abiyatara ndiponso Yowabu mwana wa Zeruya.”
23Pomwepo mfumu Solomoni adalumbira m'dzina la Chauta kuti, “Mulungu andilange koopsa ngati Adoniya saphedwa chifukwa cha zimenezi.
24Nchifukwa chake, pali Chauta wamoyo, amene adandisankhula ndi kundikhazika pa mpando waufumu wa Davide bambo wanga, nandipatsa ufumuwu monga momwe adalonjezera, Adoniya aphedwa ndithu lero lomwe lino.”
25Choncho mfumu Solomoni adatuma Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo iye adakamkantha Adoniyayo, naafa.
Abiyatara ndi Yowabu zinthu ziŵaipira26 2Sam. 15.24; 1Sam. 22.20-23 Tsono mfumu idauza wansembe Abiyatara kuti, “Pita ku Anatoti ku minda yako. Uyenera kufa ndithu, koma sindikupha tsopano lino ai, chifukwa udasunga Bokosi lachipangano la Chauta pamaso pa Davide bambo wanga, ndiponso poti udazunzika naye limodzi bambo wanga.”
271Sam. 2.27-36 Choncho Solomoni adachotsa Abiyatara pa ntchito yokhala wansembe wa Chauta. Motero zidachitikadi zija adaanena Chautazi za banja la Eli ku Silo.
28Pamene Yowabu adamva zimenezi, adathaŵira ku hema lopatulika la Chauta nakagwira nsonga za guwa lansembe. Yowabu ndiye uja ankathandiza Adoniya koma osati Abisalomu.
29Tsono Mfumu Solomoni atamva kuti Yowabu wathaŵira ku hema la Chauta, ndipo kuti wakhala pambali pa guwa lansembe, adatuma Benaya mwana wa Yehoyada namuuza kuti, “Pita, ukamuphe.”
30Choncho Benaya adapita ku hema la Chauta lija, ndipo adauza Yowabuyo kuti, “Mfumu ikukulamula kuti utuluke.” Koma Yowabuyo adati, “Iyai, ine ndifera pompano.” Apo Benaya adakauzanso mfumu zimene Yowabu adaanena.
31Mfumu idamuyankha kuti, “Kachite monga momwe iye waneneramo. Ukamuphe, ndipo ukamuike m'manda. Motero udzandichotsera ine pamodzi ndi banja la bambo wanga mlandu wa imfa ya anthu amene Yowabu adaŵapha popanda chifukwa.
32Chauta adzambwezera ntchito zake zokhetsa magazi chifukwa choti iye adapha ndi lupanga anthu abwino aŵiri aja amene anali osalakwa kupambana iyeyo, bambo wanga Davide osadziŵa. Anthu aŵiriwo ndiwo Abinere mwana wa Nere ndi mtsogoleri wa ankhondo a ku Israele, ndiponso Amasa mwana wa Yetere mtsogoleri wa ankhondo a ku Yuda.
33Choncho chilango cha magazi omwe adakhetsa aja chibwerere pa Yowabu ndiponso pa zidzukulu zake mpaka muyaya. Koma mtendere wochokera kwa Chauta ukhale pa Davide ndi zidzukulu zake, pa banja lake ndi pa mpando wake waufumu, mpaka muyaya.”
34Pamenepo Benaya mwana wa Yehoyada adapita nakamkantha Yowabu, nkumupha, ndipo adamuika m'manda ku nyumba yake ku chipululu.
35Tsono mfumu idaika Benaya mwana wa Yehoyada kuti aziyang'anira gulu lankhondo m'malo mwa Yowabu, ndipo idaika wansembe Zadoki m'malo mwa Abiyatara.
Kuphedwa kwa Simei36Pambuyo pake mfumu idatuma anthu kukaitana Simei, ndipo atabwera, idamuuza kuti, “Umange nyumba yako muno mu Yerusalemu, ndipo uzikhala mommuno, osamatuluka kukayenda kwina kulikonse.
37Ukadzatuluka ndi kuwoloka mtsinje wa Kidroni, mosapeneka konse udzaphedwa. Magazi ako adzakhala pamutu pako.”
38Simei adauza mfumu kuti, “Zimene mukunenazi nzabwino. Ine kapolo wanu ndidzachita monga momwe mwaneneramu, mbuyanga mfumu.” Choncho Simei adakhala mu Yerusalemu masiku ambiri.
39Koma zidangotere kuti patapita zaka zitatu, akapolo aŵiri a Simei adaathaŵira kwa Akisi, mwana wa Maaka, mfumu ya ku Gati. Simei atamva kuti akapolo ake ali ku Gati,
40adanyamuka pa bulu, napita ku Gati kwa Akisi, kukafunafuna akapolo ake. Simeiyo adapita, ndipo adakaŵatenga akapolo ake aja ku Gati.
41Tsono Solomoni atamva kuti Simei adaapita ku Gati kuchoka ku Yerusalemu, ndipo kuti adabwerako,
42adamuitanitsa Simeiyo namufunsa kuti, “Kodi sindidakulumbiritse iwe m'dzina la Chauta ndi kukuchenjeza kwathunthu kuti tsiku limene udzatuluke ndi kupita kwina kulikonse, udzaphedwa? Ndipo iwe udaandiwuza kuti, ‘Zimene mwanenazi nzabwino, ndimvera.’
43Nanga chifukwa chiyani tsono sudasunge zimene udalumbira kwa Chauta, ndiponso sudasunge lamulo limene ndidakulamula?”
44Mfumu idauzanso Simei kuti, “Ukudziŵa mumtima mwakomo zoipa zonse zimene udamchita Davide, bambo wanga. Tsopano Chauta akubwezera zoipa zako pa iwe.
45Koma Chauta adzandidalitsa ine mfumu Solomoni, ndipo mpando waufumu wa Davide adzaukhazikitsa mpaka muyaya.”
46Pamenepo mfumuyo idalamula Benaya mwana wa Yehoyada. Ndipo iye adatuluka nakamupha Simeiyo. Motero ufumu wa Solomoni udakhazikikadi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.