Mas. 117 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
Kutamanda Chauta
1 Aro. 15.11 Tamandani Chauta, inu mitundu yonse ya anthu.
Mlemekezeni kwambiri, inu anthu a m'maiko onse.
2Pakuti chikondi chake kwa ife nchachikulu,
kukhulupirika kwa Chauta nkwamuyaya.
Tamandani Chauta!