1Inu Mulungu, chifukwa chiyani mukutitaya mpaka muyaya?
Chifukwa chiyani mkwiyo wanu ukutukutirira
nkhosa za busa lanu ngati moto?
2Kumbukirani mpingo wanu
umene mudaupatula kuyambira kale,
mtundu umene Inu mudauwombola kuti ukhale wanuwanu.
Kumbukirani phiri la Ziyoni kumene Inu mudadzakhala.
3Dzayendereni mabwinja oonongeka kwathunthuŵa.
Adani aononga zinthu zonse za m'Nyumba yanu.
4Adani anu abangula m'malo anu opatulika,
adaikamo mbendera zao kusonyeza kuti agonjetsa.
5Adadulamo zonse,
monga momwe anthu amadulira mitengo m'nkhalango.
6Pambuyo pake, ndi nsompho ndi nyundo,
adakadzula zosemasema zonse.
7Nyumba yanu adaitentha,
malo amene Inu mumakhalako
adaŵaipitsa poŵagwetsera pansi.
8Mumtima mwao ankati,
“Tiyeni tiŵagonjetse kotheratu.”
Adatentha malo opatulika onse a Mulungu m'dzikomo.
9Zizindikiro zonse za fuko lathu zaonongeka,
kulibenso mneneri ndi mmodzi yemwe,
palibe ndi mmodzi yemwe pakati pathu
amene akudziŵa nthaŵi yodzatha zimenezi.
10Inu Mulungu, adani athuŵa adzanyodolabe mpaka liti?
Amaliwongowo adzanyozabe dzina lanu mpaka muyaya?
11Chifukwa chiyani mukubisa dzanja lanu lotithandiza?
Bwanji dzanja lanu lamanja likungokhala pachifuwa panu?
12Komabe Inu Mulungu,
ndinu mfumu yanga kuyambira kalekale.
Ndinu amene mumagwira ntchito yopulumutsa
pa dziko lonse lapansi.
13 Eks. 14.21 Mudagaŵa Nyanja Yofiira ndi mphamvu zanu.
Mudaphwanya mitu ya zilombo zam'madzi.
14 Yob. 41.1; Mas. 104.26; Yes. 27.1 Mudatswanya mitu ya Leviyatani,
chilombo cham'madzi chija,
nkuitaya kuti ikhale chakudya cha zilombo zam'chipululu.
15Mudatumphutsa akasupe ndi mifuleni,
mudaumitsa mitsinje imene siiphwa.
16Mudalenga usana ndi usiku.
Mudaika mwezi ndi dzuŵa m'malo mwake.
17Mudalemba malire a dziko lapansi,
mudakhazikitsa chilimwe ndi dzinja.
18Kumbukirani, Inu Chauta,
kuti adani amakunyodolani,
kuti anthu achipongwe amanyoza dzina lanu.
19Musati mupereke moyo wa nkhunda yanu Israele
ku zilombo zakuthengo.
Musaiŵale mpaka muyaya moyo wa anthu anu osauka.
20Kumbukirani chipangano chanu,
pakuti malo obisika am'dziko
asanduka mochitira zankhanza zambirimbiri.
21Musalole kuti anthu oponderezedwa achite manyazi.
Osauka ndi osoŵa akutamandeni.
22Dzambatukani, Inu Mulungu,
tiyeni mudziteteze pa mlandu wanuwo,
kumbukirani kuti anthu amwano
amakunyodolani tsiku lonse.
23Musalekerere chiwawa cha amaliwongo anu,
phokoso la adani anu
limene likungokulirakulira nthaŵi zonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.