1Kwezani mau kuimbira Mulungu
amene ali mphamvu zathu.
Fuulani ndi chimwemwe kwa Mulungu wa Yakobe.
2Yambani nyimbo, imbani ng'oma,
pamodzi ndi pangwe wolira bwino ndi zeze.
3 Num. 10.10 Imbani lipenga mwezi ukaoneka chatsopano,
ukaoneka kwathunthu,
pa tsiku lathu lachikondwerero.
4Pakuti ndilo lamulo lokhalira Israele,
lochokera kwa Mulungu wa Yakobe,
5Adalipereka lamulolo kwa zidzukulu za Yosefe
pamene zinkatuluka m'dziko la Ejipito.
Ndikumva liwu
limene sindidalimve ndi kale lonse, lakuti,
6“Ndidakutulani katundu wa pamapeŵa panu.
Manja anu ndidaŵachotsera ntchito yonyamula madengu.
7 Eks. 17.7; Num. 20.13 Pamene munali m'mavuto mudandiitana,
Ine nkukupulumutsani.
Ndidakuyankhani ndili wobisika m'bingu.
Ndidakuyesani ku madzi a Meriba aja.
8Imvani inu anthu anga, ndikulangizeni.
Inu Aisraele, chonde mukadandimvera!
9 Eks. 20.2, 3; Deut. 5.6, 7 “Pasadzakhale mulungu wachilendo pakati panu.
Musadzapembedze mulungu wina ai.
10Ine ndine Chauta, Mulungu wanu,
amene ndidakutulutsani m'dziko la Ejipito.
Yasamani kukamwa, Ine ndidzakudyetsani.
11“Koma anthu anga sadamvere mau anga.
Israele adandinyoza.
12Choncho ndidaŵasiya ndi mitima yao yosamverayo,
kuti atsate zimene ankafuna.
13“Anthu anga akadandimvera,
Aisraele akadayenda m'njira zanga,
14bwenzi posachedwa nditagonjetsa adani ao,
ndipo dzanja langa likadakantha amaliwongo ao.
15“Anthu amene amadana ndi Chauta,
akadakhwinyata pamaso pake,
ndipo tsoka lao likadakhala mpaka muyaya.
16Ndikadakudyetsani ndi ufa wosalala watirigu,
ndipo ndikadakukhutitsani ndi uchi wam'thanthwe.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.