1Zoonadi, Mulungu ndi wabwino kwa olungama,
kwa anthu oyera mtima.
2Koma ine ndinali pafupi kuphunthwa,
mapazi anga anali pafupi kuterereka.
3Pakuti ndinkachita nsanje ndi anthu odzikuza,
pamene ndidaona anthu oipa akulemera.
4Iwowo samva kupweteka konse.
Matupi ao ndi onenepa ndi athanzi.
5Saona mavuto monga anthu ena,
sazunzika ngati anzao.
6Nchifukwa chake amavala kunyada ngati mkanda wam'khosi.
Amavala nkhanza ngati malaya.
7Maso ao ndi otupa ndi kunenepa.
Mitima yao ndi yodzaza ndi maganizo ofuna kuchita zoipa.
8Amanyodola ndi kumalankhula zoipa,
amadzikuza ndi kumaopseza ena kuti,
“Tikupsinjani.”
9Pakamwa pao pamalankhula monyoza Mulungu kumwamba,
ndipo lilime lao ndi losamangika pa dziko lapansi.
10Nchifukwa chake ngakhale anthu a Mulungu
amabwera kwa iwo,
ndipo amakhuta zonena zao ngati madzi akumwa.
11Amati,
“Kodi Mulungu angadziŵe bwanji?
Kodi Wopambanazonseyo angadziŵe kanthu kalikonse?”
12Onani, umu ndimo m'mene aliri anthu oipa.
Nthaŵi zonse ali pabwino,
ndipo amangolemera kosalekeza.
13Ine ndasunga mtima wanga woyera,
ndasamba m'manja kuwonetsa kuti ndine wosalakwa,
koma zonsezi popanda phindu konse.
14Pakuti ndapeza mavuto tsiku lonse,
ndipo ndalangidwa m'maŵa mulimonse.
15Ndikadati, “Ndilankhula monga amachitira iwowo,”
ndikadakhala wosakhulupirika kwa zidzukulu zanu,
16Koma pamene ndidalingalira zimenezi
kuti ndizimvetse bwino,
zidandiwonekera ngati nkhani yovuta,
17mpaka nditakaloŵa m'malo opatulika a Mulungu,
apo mpamene ndidaona mathero ake a anthuwo.
18Zoonadi, Inu mumapondetsa anthu oipa pa malo oterera.
Mumaŵagwetsa mpaka aonongeke.
19Adzangoferatu ndi mantha,
ndi kuwonongeka pa kamphindi kochepa.
20Inu Ambuye, pamene mudzadzuka mudzaŵanyoza kotheratu,
monga momwe munthu amanyozera maloto atadzuka m'maŵa.
21Pamene paja ndinkavutika ndi maganizo,
ndi kumamva cholasa mumtimamu,
22ndinali wopusa wosamvetsa kanthu,
ndinali ngati chilombo kwa Inu.
23Koma chonsecho ndili ndi Inu nthaŵi zonse.
Inu mumandigwira dzanja lamanja.
24Mumandiwongolera ndi malangizo anu,
pambuyo pake mudzandilandira ku ulemerero.
25Nanga ndili ndi yani kumwamba kupatula Inu?
Pansi pano palibe kanthu kena kamene ndimafuna,
koma Inu nokha.
26Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani,
Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga
ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.
27Onse amene ali kutali ndi Inu adzaonongeka,
Inu mumaŵaononga amene ali osakhulupirika kwa Inu.
28Koma ine kukhala pafupi ndi Mulungu kumandikomera.
Ndatsimikiza zoti Ambuye ndiwo kothaŵira kwanga
ndipo ndidzalalika ntchito zao zonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.