1Naomi anali ndi wachibale wake wachuma kwambiri, wa m'banja la malemu mwamuna wake uja Elimeleki, dzina lake Bowazi.
2Lev. 19.9, 10; Deut. 24.19 Tsiku lina Rute adauza Naomi kuti, “Mundilole kuti ndikakunkhe barele ku munda wa munthu aliyense amene akandikomere mtima.” Naomi adamuuza kuti, “Pita mwana wanga.”
3Choncho Rute adanyamuka napita kukakunkha ku minda, anthu atakolola kale. Kudangochitika kuti adakafika ku munda wa Bowazi amene anali wa m'banja la Elimeleki.
4Posachedwa Bowazi adafika kuchokera ku Betelehemu, ndipo adalonjera anthu okolola aja kuti, “Chauta akhale nanu.” Iwo adayankha kuti, “Chauta akudalitseni.”
5Tsono Bowazi adafunsa kapitao wake amene ankayang'anira anthu okolola aja kuti, “Kodi mai uyu ndani?”
6Kapitao wakeyo adayankha kuti, “Maiyu ndi Mmowabu amene adabwera ndi Naomi kuchokera ku dziko la Mowabu.
7Iyeyu wandipempha kuti, ‘Chonde mundilole kuti ndikunkheko barele m'munda m'mene anthu akolola kale!’ Choncho wakhala akukunkha kuyambira m'mamaŵa mpaka tsopano lino, osapuma ndi pang'ono pomwe.”
8Apo Bowazi adauza Rute kuti, “Tamvera, mwana wanga, usapite kukakunkha ku munda wina, usasiye munda uno, koma uzitsata adzakazi angaŵa.
9Uziyang'ana munda akukololawu, ndipo uziŵatsata pambuyo. Ndaŵauza anyamatawo kuti asakuvute. Tsono ukamamva ludzu, uzipita ku mitsuko ndi kukamwa madzi amene anyamatawo atunga.”
10Rute adaŵerama, nazyolikitsa nkhope pansi, ndipo adafunsa kuti, “Chifukwa chiyani ndapeza kukoma mtima kotereku mwa inu, kuti mulabadeko za ine mlendo?”
11Koma Bowazi adayankha kuti, “Zonse zimene wakhala ukuchitira mpongozi wako, kuyambira nthaŵi imene mwamuna wako adamwalira, ndazimva zonsezo. Ndamvanso kuti udasiya bambo wako, mai wako ndi dziko lako, ndipo wabwera kwa anthu amene sudaŵadziŵe ndi kale lonse.
12Chauta akubwezere zabwino zimene wachitazi. Akupatse mphotho yaikulu Chauta, Mulungu wa Aisraele, poti wabwera kwa Iye kuti akuteteze.”
13Apo Rute adati, “Mwandikomera mtima kwambiri mbuyanga, mwandisangalatsa ndipo mwandilankhula mwachifundo, ngakhale sindine mmodzi mwa adzakazi anu.”
14Nthaŵi yakudya Bowazi adauza Rute kuti, “Bwera kuno, udzadyeko buledi ndi kusunsa nthongo yako m'vinyo.” Choncho adakhala pansi pafupi ndi anthu okolola aja, ndipo adampatsa barele wokazinga. Adadya mpaka kukhuta ndipo barele wina adatsalako.
15Pamene adanyamuka mkaziyo kuti akakunkhe, Bowazi adaŵalangiza antchito ake aja kuti, “Muzimulola mkaziyu kuti azikunkha ngakhale pakati pa mitolo, osamchititsa manyazi.
16Muzimusololerako ngala zina zam'mitolo ndi kumlekera kuti azikunkha, osamdzudzula.”
17Choncho Rute adakunkha m'mundamo mpaka madzulo. Pambuyo pake adapuntha barele amene adakunkha uja, ndipo adakwanira pafupi makilogramu khumi.
18Adatenga bareleyo kupita naye ku mudzi, nakaonetsa mpongozi wake. Atatero, adatulutsa chakudya chimene chidatsalira atakhuta chija, napatsa mpongozi wakeyo.
19Naomi adamufunsa kuti, “Unakakunkha kuti lero? Unakagwira ntchitoyi m'munda mwa yani? Ngwodala munthu amene anakukomera mtimayo.” Rute adauza mpongozi wake za munthu amene adagwirako ntchito, adati, “Munthuyo dzina lake ndi Bowazi.”
20Lev. 25.25 Apo Naomi adauza Rute kuti, “Munthu ameneyo amdalitse Chauta, amene amasunga malonjezo ake kwa anthu amoyo, ngakhalenso kwa anthu akufa.” Ndipo adatinso, “Munthuyo ndi mnansi wathu, mmodzi mwa achibale athu, amene ali ndi udindo wotisamala.”
21Tsono Rute Mmowabuyo adati, “Kuwonjezera pamenepo, munthuyo anandiwuza kuti, ‘Uzitsata antchito angaŵa mpaka atamaliza munda wanga kukolola.’ ”
22Naomi adauza Rute kuti, “Kuli bwino mwana wanga kuti uzipita ndi adzakazi ake, kuwopa kuti ukapita m'munda wina, angakuvute.”
23Motero Rute ankatsatira adzakazi a Bowaziwo, namakunkha, mpaka anthu atamaliza kudula barele ndi tirigu. Monsemo Rute ankakhala ndi mpongozi wakeyo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.