1Lizani lipenga ku Ziyoni.
Fuulani mochenjeza pa phiri langa loyera.
Onse okhala m'dziko anjenjemere,
pakuti tsiku la Chauta likufika, layandikira.
2Ndi tsiku lamdima ndi lachisoni,
tsiku lamitambo ndi la mdima wandiweyani.
Gulu la ankhondo amphamvu ochuluka
langoti bii ngati mdima wokuta mapiri.
Gulu lotere silinaonekepo nkale lonse,
ngakhale kutsogolo kuno silidzaonekanso.
3Kutsogolo kwake moto ukupsereza,
kumbuyo kwake malaŵi a moto akutentha zinthu.
Iwo asanafike, dziko linali ngati munda wa Edeni,
koma atachoka, lidasanduka chipululu!
Palibe kanthu kotsalapo.
4 Chiv. 9.7-9 Maonekedwe ake ali ngati a akavalo,
liŵiro lake ngati la akavalo ankhondo.
5Akulumpha pamwamba pa mapiri
ndi phokoso longa la magaleta.
Akumveka ngati malaŵi a moto otentha ziputu,
ngati gulu lamphamvu lankhondo
litakonzekera kumenya nkhondo.
6Anthu a mitundu ina amachita mantha akaŵaona,
nkhope zonse zimatumbuluka.
7Akududuka ngati ankhondo.
Akukwera malinga ngati asilikali.
Aliyense akuyenda pa mzere,
osasempha njira yake.
8Sakukankhanakankhana,
aliyense akuyenda molunjika.
Akupyola pakati pa zida zankhondo, osaŵaimitsa.
9Akuulumphira mzindawo,
akukwera pamwamba pa malinga.
Akuloŵa m'nyumba,
akuloŵera pa windo ngati mbala.
10 Chiv. 8.12 Dziko lapansi likugwedezeka
pamene iwo akuyandikira.
Mlengalenga ukunjenjemera.
Dzuŵa ndi mwezi zikuchita mdima,
ndipo nyenyezi zikuleka kuŵala.
11 Chiv. 6.17 Chauta akumveketsa liwu lake
kutsogolo kwa gulu lake lankhondo.
Gulu lake lankhondolo ndi lalikulu kwambiri.
Wochitadi zimene Chauta akulamula, ngwamphamvu.
Tsiku la Chauta ndi lalikulu ndi loopsa.
Ndani angathe kupirira tsikulo?
Mulungu aitana anthu kuti abwerere12Koma Chauta akunena kuti,
“Ngakhale tsopano bwererani kwa Ine
ndi mtima wanu wonse,
mukusala zakudya, mukukhetsa misozi
ndi kulira mwachisoni.
13Ng'ambani mitima yanu, osati zovala zanu chabe.”
Bwererani kwa Chauta, Mulungu wanu,
poti Iye ngwokoma mtima ndi wachifundo,
wosakwiya msanga ndi wa chikondi chosasinthika.
Nthaŵi zonse ndi wokonzeka kukhululuka.
14Mwina mwake adzasintha mtima ndi kuleka,
ndipo adzatisiyira madalitso.
Madalitsowo adzakhala a chopereka cha chakudya
ndi chakumwa
zopereka kwa Chauta,
Mulungu wanu.
15Lizani lipenga ku Ziyoni.
Lengezani mwambo wa kusala zakudya.
Muitanitse msonkhano waukulu.
16Sonkhanitsani anthu pamodzi,
muŵauze kuti adziyeretse.
Sonkhanitsani akuluakulu,
sonkhanitsani ana,
sonkhanitsani ndi oyamwa omwe.
Lamulani kuti nawonso akwati achoke
m'chipinda mwao, abwere.
17 1Am. 7.36-38 Ansembe, amene ali atumiki a Chauta,
azilira pakati pa guwa lansembe ndi khonde.
Azinena kuti,
“Inu Chauta, achitireni chifundo anthu anu.
Musalole kuti ena aŵanyoze
anthu anu osankhidwa.
Anthu achikunja asaŵaseke
pomafunsana kuti,
‘Ha, ali kuti Mulungu waoyo?’ ”
Mulungu akhululukira Israele18Apo chikondi cha Chauta chidayaka
ngati moto chifukwa cha dziko lake,
ndipo adaŵachitira chifundo anthu ake.
19Chauta adaŵayankha anthu ake kuti,
“Ndikutumizirani tirigu, vinyo ndi mafuta,
ndipo mudzakhuta ndithu.
Sindidzalolanso kuti akunja akunyozeni.
20Ndidzachotsa adani akumpoto
kuti akhale kutali ndi inu,
ndipo ndidzaŵapirikitsira ku dziko
louma ndi lachipululu.
Akutsogolo ndidzaŵathamangitsira
ku nyanja yakuvuma,
akumbuyo ndidzaŵathamangitsira
ku nyanja yakuzambwe.
Tsono mitembo yao idzatulutsa
chivundi ndi fungo lonunkha.
Zoonadi Chauta adachita zazikulu.
21“Iwe dziko, usachite mantha.
Kondwa ndipo usangalale,
pakuti Chauta mwini wake adachita zazikulu.
22Inu nyama zakuthengo, musaope,
pakuti msipu wakuchipululu akuphukira.
Mitengo ikubala zipatso.
Mkuyu ndi mpesa zikubereka kwamphamvu.
23“Inu anthu a ku Ziyoni, kondwani ndi
kusangalala chifukwa cha zimene Chauta,
Mulungu wanu, wakuchitirani.
Wakukomerani mtima pokupatsani mvula mofulumira.
Wakupatsani mvula yochuluka,
kumayambiriro ndi kumathero,
monga pa masiku amekedzana.
24“Pa malo opunthira padzadzaza tirigu.
Mopondera mphesa mudzasefukira vinyo watsopano,
mafutanso adzachuluka.
25Motero ndidzakubwezerani zonse
zimene zidaonongedwa ndi dzombe,
mandowa, mphutsi ndi ziwala.
Limenelitu ndiye gulu lankhondo lija
limene ndidatuma kudzakukanthani.
26“Mudzadya zambiri ndi kukhuta,
ndipo mudzatamanda dzina la Chauta,
Mulungu wanu,
amene wakuchitirani zodabwitsa.
Choncho anthu anga sadzaŵanyozanso ai.
27Mudzadziŵa kuti Ine ndili naye Israele,
ndipo kuti Ine ndekha, osati wina,
ndine Chauta, Mulungu wanu.
Anthu anga sadzaŵanyozanso ai.
Za kubwera kwa Tsiku la Chauta28“Patapita nthaŵi, tsiku lidzafika
pamene ndidzatsitsa mzimu wanga
pa mtundu uliwonse wa anthu.
Ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzalosa.
Nkhalamba zanu zidzalota maloto,
ndipo achinyamata anu adzaona zinthu m'masomphenya.
29Masiku amenewo, ndidzatsitsa mzimu wanga
ngakhale pa akapolo ndi pa adzakazi omwe.
30“Mu mlengalenga ndi pa dziko lapansi ndidzaonetsa zodabwitsa izi: magazi, moto ndi utsi watoloo.
31Mt. 24.29; Mk. 13.24, 25; Lk. 21.25; Chiv. 6.12, 13 Dzuŵa lidzasanduka mdima, ndipo mwezi udzasanduka magazi, tsiku lalikulu ndi loopsa la Chauta lisanafike.
32Ntc. 2.17-21
Aro. 10.13 Ndipo aliyense amene adzatama dzina la Chauta mopemba, adzapulumuka. Monga Iye adanenera, kudzakhala ena opulumuka ku phiri la Ziyoni ndi ku Yerusalemu, ndipo mwa otsalawo padzapezeka ena amene Chauta adzaŵaitana.Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.