1Zimene Ambuye Chauta akunena ndi izi, akuti, “Chipata chakuvuma cha bwalo lam'kati chizikhala chotseka masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito. Azitsekula pa tsiku la Sabata lokha ndi tsiku limene mwezi wakhala.
2Mfumu poloŵa izidzera m'khonde lam'kati la chipata kuchokera kunja, nkudzaima pafupi ndi nsanamira yapakhomo. Ansembe apereke nsembe yake yopsereza ndi nsembe yachiyanjano. Mfumuyo ipembedze pachiwundopo, kenaka nkutuluka. Koma chipatacho asachitseke mpaka madzulo.
3Anthu nawonso azipembedza pamaso pa Chauta pa khomo la chipata chimenecho pa masiku a Sabata ndiponso pa tsiku limene mwezi wakhala.
4Nsembe yopsereza imene mfumu iyenera kupereka kwa Chauta ikhale motere: pa tsiku la Sabata azipereka anaankhosa asanu ndi mmodzi opanda chilema ndiponso nkhosa yamphongo yopanda chilema.
5Pamodzi ndi nkhosa yamphongo iliyonse, mfumu izipereka ufa wokwanira efa imodzi. Pamodzi ndi anaankhosa aja mfumu iziperekanso ufa monga ingathere. Iperekenso hini imodzi ya mafuta pa efa iliyonse ya ufa.
6Pa tsiku limene mwezi wakhala mfumu ipereke mwanawang'ombe wamphongo wopanda chilema, anaankhosa asanu ndi mmodzi, ndi nkhosa yamphongo, zonsezo zopanda chilema.
7Ipereke efa imodzi ya ufa pa ng'ombe yamphongo iliyonse, ndiponso efa ina pa nkhosa yamphongo iliyonse. Pa anaankhosa iperekenso ufa monga m'mene ingathere. Pamodzi ndi efa iliyonse ya ufa, ipereke hini imodzi ya mafuta.
8Mfumu poloŵa, izidzera m'khonde lam'kati la chipata chakuvuma, nkutulukiranso pomwepo.
9“Pa masiku achikondwerero, anthu am'dzikomo akabwera kudzapembedza Chauta, munthu woloŵera pa chipata chakumpoto azidzatulukira pa chipata chakumwera. Munthu woloŵera pa chipata chakumwera, azidzatulukira pa chipata chakumpoto. Munthu aliyense asadzatulukire pomwe waloŵera, koma azipita chakutsogolo.
10Tsono mfumu izidzakhala pakati pao. Izidzaloŵa nthaŵi imene iwowo akuloŵa, nkutuluka nthaŵi imene iwowo akutuluka.
11“Pa masiku achikondwerero ndi pa masiku ena osankhidwa, zopereka za ufa zikhale zokwanira efa imodzi pamodzi ndi ng'ombe yamphongo iliyonse, efa imodzinso pamodzi ndi nkhosa yamphongo iliyonse, koma pa mwanawankhosa azipereka monga m'mene angathere. Iperekenso hini imodzi ya mafuta pamodzi ndi efa iliyonse ya ufa.
12Pamene mfumu ikufuna kupereka zaufulu kwa Chauta, monga nsembe yopsereza kapena nsembe zachiyanjano, aitsekulire chipata chakuvuma. Ipereke nsembe yake yopsereza ndi nsembe yake yachiyanjano, monga m'mene imachitira pa tsiku la Sabata. Itamaliza, ituluke. Itatuluka, chipata chitsekedwe.
Zopereka za tsiku lililonse13“Tsiku lililonse, nthaŵi yam'maŵa, azipereka kwa Chauta mwanawankhosa wa chaka chimodzi wopanda chilema.
14Pamodzi ndi nyamayo aziperekanso m'maŵa mulimonse ufa wokwanira chimodzi mwa zigawo zisanu ndi chimodzi za efa. Aziperekanso chimodzi mwa zigawo zitatu za hini ya mafuta okandira ufa wosalala. Nsembe imeneyi yopereka kwa Chautayi iziperekedwa nthaŵi zonse.
15Motero azipereka mwanawankhosa, ufa ndi mafuta m'maŵa mulimonse, kuti zikhale zopsereza tsiku ndi tsiku.”
16Zimene Ambuye Chauta akunena ndi izi, akuti, “Kalonga akapereka chigawo cha chuma chake kwa mmodzi mwa ana ake, mphatsoyo ndi ya ana akewodi, popeza kuti ndi chigawo cha choloŵa cha makolo.
17 Pamenepo mphatsoyo idzabwerera kwa kalonga uja, chifukwa chuma chake chonse ncha ana okha.
18Tsono kalonga asalande anthu gawo la chuma chaochao pakuŵachotsa m'dera lao la dziko. Ana ake kalonga aŵapatse choloŵa chao pa dziko limene lili lakelake, kuti choncho asalande ndi mmodzi yemwe mwa ana anga choloŵa chake.”
Zipinda zophikiramo za ku Nyumba ya Mulungu19Pambuyo pake munthu uja adandidzeretsa pa khomo la pambali pa chipata nandiloŵetsa ku zipinda zopatulika za ansembe zoyang'ana kumpoto. Ndipo adandilozera malo chakuzambwe kwa zipindazo, nandiwuza kuti,
20“Aŵa ndi malo m'mene ansembe azidzaphikiramo nyama za nsembe zopepesera kupalamula ndiponso nsembe zopepesera machimo. Kumenekonso ndiko kumene azidzaotcherako chopereka cha chakudya. Sadzatuluka nazo zoyerazi m'bwalo lakunja kuwopa kuti angapatsireko kuyera anthu enawo.”
21Atatero adandiloŵetsa m'bwalo lakunja napita nane ku ngodya zinai za bwalolo. Tsono m'kati mwa ngodya iliyonse munali bwalo lina.
22Motero pa ngodya zinai za bwalo lalikululo panali mabwalo ena ang'onoang'ono. Mabwalo amenewo anali ofanana, m'litali mwake mamita makumi aŵiri, muufupi mwake mamita khumi ndi asanu.
23Kuzungulira mabwalo anai ang'onoang'onowo panali mpanda wamiyala, ndiponso malo osonkhapo moto, omangidwa m'munsi mwa mpandawo.
24Tsono adandiwuza kuti, “Zimenezi ndizo zipinda zophikiramo, kumene anthu otumikira m'Nyumba ya Mulungu aziphikiramo nyama za nsembe za anthu.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.