Eza. 10 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kuthetsa maukwati okwatirana ndi akunja

1Pamene Ezara ankapemphera ndi kulapa, alikulira ndipo atadzigwetsa pansi ku Nyumba ya Mulungu, chinamtindi cha anthu chidabwera kwa iye kudzasonkhana. Panali amuna, akazi ndi ana, kuchokera m'dziko lonse la Israele, ndipo ankalira koopsa.

2Tsono Sekaniya, mwana wa Yehiyele, wa fuko la Elamu, adauza Ezara kuti, “Ife takhala osakhulupirika kwa Mulungu wathu, ndipo takhala tikukwatira akazi achilendo a mitundu ya m'maiko akunoŵa. Koma ngakhale zili choncho, chikhulupiriro chilipobe pakati pa Aisraele.

3Tiyeni tsono tichite naye chipangano Mulungu wathu, kuti ifeyo tilekane nawo akazi ameneŵa pamodzi ndi ana ao, potsata uphungu wa inu mbuyanga ndi wa anthu amene amaopa malamulo a Mulungu wathu. Ndipo tidzazichitadi potsata malamulowo.

4Ndiye inu dzukani, imeneyi ndi ntchito yanu, ndipo ife tili nanu. Valani dzilimbe ndipo muigwire ntchitoyo.”

5Choncho Ezara adanyamuka ndipo adalumbiritsa akulu a ansembe, Alevi ndi Aisraele onse, kuti adzachitedi monga m'mene Sekaniya adaanenera. Tsono onsewo adalumbira.

6Pambuyo pake Ezara adachokako ku Nyumba ya Mulungu napita ku chipinda cha Yehohanani, mwana wa Eliyasibu, kumene adakachezera usikuwo. Sadadye buledi kapena kumwa madzi. Nthaŵi yonseyo adakhalira kulira chifukwa cha kusakhulupirika kwa anthu obwerako ku ukapolo aja.

7Tsono anthu adalengeza m'dziko lonse la Yuda ndi mu mzinda wa Yerusalemu, kwa onse ochokera ku ukapolo aja, kuti asonkhane ku Yerusalemu.

8Adanena kuti, “Wina aliyense akapanda kufika asanathe masiku atatu, ndiye kuti potsata lamulo la atsogoleri ndi la akulu, adzayenera kumlanda katundu wake yense, ndipo adzachotsedwe m'gulu la anthu obwerako ku ukapolo aja.”

9Choncho anthu onse a m'dziko la Yuda ndi a m'dziko la Benjamini adasonkhana ku Yerusalemu asanathe masiku atatu. Limeneli linali tsiku la 20 la mwezi wachisanu ndi chinai. Ndipo anthu onse adakhala pansi pa bwalo la Nyumba ya Mulungu, ali njenjenje chifukwa cha nkhani imeneyi ndiponso chifukwa cha mvula yambiri imene inkagwa.

10Tsono wansembe Ezara adaimirira nati, “Mudachimwa pomakwatira akazi achikunja, ndipo mudaonjezera tchimo la Israele.

11Lapani tsopano kwa Chauta, Mulungu wa makolo anu, ndipo muchite zimene Iye akufuna. Dzichotseni pakati pa mitundu ya anthu a m'maiko enaŵa, ndi pa akazi achilendowo.”

12Chitamva mau amenewo, chinantindi chonse chapamsonkhanopo chidayankha mokweza mau kuti, “Ndi chonchodi, tiyenera kuchitadi monga mwaneneramo.

13Koma anthu ali panoŵa ngambiri, ndipo mvula ikugwa kwamphamvu, sitingathe kukaima pa mtetete. Chinanso nchakuti ntchitoyi si ya tsiku limodzi kapena masiku aŵiri, pakuti tidachimwa kwambiri pa nkhani imeneyi.

14Tsono atsogoleri athu aimirire m'malo mwa msonkhano wonse. Anthu onse a m'mizinda yathu amene adakwatira akazi achilendo abwere pa nthaŵi imene inu munene, ndipo abwere pamodzi ndi akulu ndi aweruzi a mzinda uliwonse. Motero mkwiyo woopsa wa Mulungu wathu pa nkhani imeneyi udzachoka.”

15Yonatani yekha, mwana wa Asahele, ndiponso Yahazeiya, mwana wa Tikiwa, ndi amene adatsutsapo pa zimenezi, ndipo Mesulamu pamodzi ndi Mlevi Sabetai, adaŵavomereza.

16Choncho anthu obwerako ku ukapolo aja, adachitadi momwemo. Wansembe Ezara adasankha anthu, akulu a mabanja potsata mafuko ao, aliyense kuchita kumlemba dzina. Pa tsiku loyamba la mwezi wakhumi, adayambapo kuifufuza nkhani imeneyi.

17Ndipo pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, anali atathana nawo anthu amene adaakwatira akazi achilendo aja.

Anthu amene adaakwatira akazi achilendo

18Nawu mndandanda wa ansembe amene adaakwatira akazi achilendo: Pa banja la Yesuwa ndi abale ake, ana a Yozadaki, panali aŵa: Maaseiya, Eliyezere, Yaribu ndi Gedaliya.

19Iwo adatsimikiza zochotsa akazi ao, ndipo adapereka nkhosa yamphongo yopepesera machimo ao.

20Pa banja la Imara panali Hanani ndi Zebadiya.

21Pa banja la Harimu panali Maaseiya, Eliya, Semaya, Yehiyele ndi Uziya.

22Pa banja la Pasuri panali Eliyoenai, Maaseiya, Ismaele, Netanele, Yozabadi ndi Elasa.

23Pakati pa Alevi panali aŵa: Yosabadi, Simei, Kelaya (amene ankatchedwanso Kelita), Petahiya, Yuda ndi Eliyezere.

24Pakati pa oimba nyimbo, panali Eliyasibu. Pakati pa alonda a ku Nyumba ya Mulungu panali Salumu, Telemu ndi Uri.

25Pakati pa Israele: a fuko la Parosi anali Ramiya, Iziya, Malikiya, Miyamini, Eleazara, Hasabiya ndi Benaya.

26A fuko la Elamu anali Mataniya, Zekariya, Yehiyele, Abidi, Yeremoti ndi Eliya.

27A fuko la Zatu anali Eliyoenai, Eliyasibu, Mataniya, Yeremoti, Zabadi, ndi Aziza.

28A fuko la Bebai anali Yehohanani, Hananiya, Zabibai ndi Atilai.

29A fuko la Bani anali Mesulamu, Malaki, Adaya, Yasubu, Seyala ndi Yeremoti.

30A fuko la Pahatimowabu anali Adina, Kelali, Benaya, Maaseiya, Mataniya, Bezalele, Binuyi ndi Manase.

31A fuko la Harimu anali Eliyezere, Isiya, Malikiya, Semaya, Simeoni

32Benjamini, Maluki ndi Semariya.

33A fuko la Hasumu anali Matenai, Matata, Zebadi, Elifeleti, Yeremai, Manase ndi Simei.

34A fuko la Bani anali Maadai, Amuramu, Uwele,

35Benaya, Bedeiya, Keluhu,

36Vaniya, Meremoti, Eliyasibu,

37Mataniya, Metenai, ndi Yasu.

38A fuko la Binuyi anali Simei,

39Selemiya, Natani, Adaya,

40Makinadebai, Sasai, Sarai,

41Azarele, Seremiya, Semariya,

42Salumu, Amariya ndi Yosefe.

43A fuko la Nebo anali Yeiyele, Matitiya, Zabadi, Zebina, Yadai, Yowele ndi Benaya.

44Onseŵa adaakwatira akazi achilendo. Tsono adaŵasudzula akaziwo pamodzi ndi ana ao omwe.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help