Gen. 49 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yakobe adalitsa ana ake

1Pambuyo pake Yakobe adaitana ana ake naŵauza kuti, “Sonkhanani pamodzi, kuti ndikuuzeni zimene zidzakuchitikireni m'tsogolo muno.

2“Bwerani kuno, ndipo mumve, inu ana a Yakobe,

mverani bambo wanu Israele.

3“Rubeni mwana wanga wachisamba,

ndiwe nkhongono zanga,

ndiwe mphatso yoyamba ya mphamvu zanga.

Mwa ana anga onse,

wopambana ndiwe pa ulemerero ndi mphamvu.

4Uli ngati chigumula cha madzi oopsa,

koma sudzakhalanso wopambana,

chifukwa chakuti sudaope kugona pa bedi la ine bambo wako.

Udaloŵa m'bedi langa, nuliipitsa!

5“Simeoni ndi Levi mpachibale pao,

amagwiritsa ntchito zida zankhondo pochita chiwawa.

6Ine sindidzakhala nao pa zokambirana zao zam'seri,

sindifuna kukhala nao m'misonkhano yao,

chifukwa choti adapha anthu mokalipa,

ndipo adapundula ng'ombe zamphongo mwankhanza,

naziyesa choseketsa.

7Matemberero aŵagwere,

chifukwa mkwiyo wao ndi woopsa kwambiri,

ukali wao utembereredwenso,

chifukwa imeneyo ndi nkhalwe.

Ndidzaŵamwaza iwowo m'dziko lonse la Yakobe.

Ndidzaŵabalalitsa pakati pa Israele.

8“Iwe Yuda, abale ako adzakutamanda.

Adani ako udzaŵagwira pa khosi,

abale ako adzakugwadira iwe.

9 Num. 24.9; Chiv. 5.5 Yuda ali ngati msona wa mkango.

Ukapha, umabwereranso kumalo kumene umabisala.

Yuda ali ngati mkango,

amatambasuka nagona pansi.

Iye ndi mkangodi,

ndipo palibe amene angalimbe mtima kuti amdzutse.

10Ndodo yaufumu siidzachoka mwa Yuda,

adzachita kuupanira ufumu umenewo,

adzasunga mphamvu zake,

mpaka mwiniwake weniweni atabwera,

wodzalamulira anthu onse.

11Bulu wake amamumangirira ku mtengo wamphesa,

mwanawabulu ku mpesa wabwino.

Zovala zake amazichapa mu vinyo,

mu vinyo wofiira ngati magazi.

12Maso ake ndi ofiira ndi vinyo

mano ake ndi oyera ndi mkaka.

13“Zebuloni adzakhala m'mbali mwa nyanja,

madooko ake adzakhala malo a zombo,

dziko lake lidzafika mpaka ku Sidoni.

14“Isakara ali ngati bulu wamphamvu,

amagona chotambasuka pakati pa makola.

15Ataona kukoma kwa malo ousirapowo,

ndi kukongola kwa dzikolo.

Adaŵeramitsa msana kuti anyamule katundu wake,

ndipo adasanduka womagwira ntchito yaukapolo.

16“Dani adzalamulira anthu ake.

Anthuwo adzalingana ndi mafuko ena a Israele.

17Dani adzakhala ngati njoka pambali pa mseu,

njoka yaululu ndithu m'mbali mwa njira,

yoluma ku chidendene cha kavalo,

kotero kuti wokwerapo wake adzagwa chagada.

18“Ndikuyembekeza chipulumutso chanu, Inu Chauta.

19“Gadi anthu achifwamba adzamthira nkhondo,

koma iyeyo adzaŵatembenukira nkuŵapirikitsa.

20“Dziko la Asere lidzabala chakudya chokoma,

choyenera kudya mafumu.

21“Nafutali ali ngati insa yongoyenda mwaufulu,

imene imabala ana okongola.

22“Yosefe ali ngati nthambi yobala zipatso,

nthambi yobala zipatso pafupi ndi kasupe,

nthambi yotambasuka pa khoma.

23Adani ake adalimbana naye mwankhalwe,

namthamangitsa ndi mauta ao.

24Koma iyeyo uta wake sudagwedezeke,

mikono yake idalimbika,

ndi mphamvu za Mulungu Wamphamvuzonse wa Yakobe,

amene ali Mbusa ndi Thanthwe la Israele.

25Ndi Mulungu wa atate ako amene amakuthandiza,

ndi Mulungu Mphambe amene amakudalitsa.

Amakudalitsa ndi mvula yochokera mu mlengalenga,

ndi madzi otumphuka pansi pa nthaka,

ndipo adzakudalitsa pakukupatsa ana ambiri

ndi ng'ombe zambiri.

26Madalitso a bambo wako ndi amphamvu

kupambana madalitso a mapiri amuyaya,

kupambananso zabwino za ku zitunda zamuyaya.

Zimenezi zidzakhala pamutu pa Yosefe,

pamphumi pa kalonga amene adampatula

pakati pa abale ake.

27“Benjamini ali ngati mmbulu wolusa

umene m'maŵa umapha ndi kudya zimene udagwira,

ndipo madzulo umagaŵa zimene udagwirazo.”

28Aŵa ndiwo akulu a mafuko khumi ndi aŵiri a Aisraele, ndipo zimenezi nzimene bambo wao Yakobe adaŵauza, pamene ankadalitsa aliyense mwa iwo potsazikana nawo.

Yakobe amwalira naikidwa m'manda

29Tsono Yakobe adaŵalamula ana akewo kuti, “Popeza kuti tsopano ndilikufa, mukandiike m'phanga limene lili m'munda wa Efuroni Muhiti, ku Makipera.

30Gen. 23.3-20 Lili kuvuma kwa Mamure m'dziko la Kanani. Abrahamu adaagula phangalo pamodzi ndi munda womwe kwa Efuroni Muhiti, kuti pakhale manda.

31Gen. 25.9, 10; Gen. 35.29 Kumeneko ndiko kumene adaika Abrahamu pamodzi ndi Sara mkazi wake. Isaki pamodzi ndi mkazi wake Rebeka, adaŵaikanso komweko, ndipo Leya ndidamuika komwekonso.

32Mundawo pamodzi ndi phangalo adagula kwa Ahiti.”

33Ntc. 7.15 Tsono Yakobe atamaliza kulangiza ana ake, adabwezeranso mapazi ake m'bedi ndipo adamwalira.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help