Hos. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chauta aimba mlandu Israele

1Inu Aisraele, imvani mau a Chauta,

chifukwa Iye akukuimbani mlandu,

inu anthu okhala m'dziko.

Mlandu wake ndi wakuti,

m'dziko mulibe kukhulupirika kapena kukoma mtima,

ndipo Mulungu samulabadira.

2Akulumbira monama, kunena zabodza,

kupha, kuba ndi kuchita chigololo.

Machimo achita kunyanya,

ndipo akungophanaphana.

3Nchifukwa chake mudzagwa chilala m'dziko,

ndipo onse okhalamo adzavutika

pamodzi ndi nyama zakuthengo zomwe,

ndi mbalame zamumlengalenga.

Ngakhale nsomba zam'nyanja zidzafa.

Chauta aimba mlandu ansembe.

4Chauta akuti, “Wina aliyense asatsutsepo kanthu,

wina aliyense asaimbe mnzake mlandu,

pakuti mlandu uli pakati pa Ine

ndi inu ansembe onyenganu.

5Mumakhumudwa usana ndi usiku,

ndipo aneneri nawonso amachita chimodzimodzi,

motero ndidzaononga Israele mai wanu.

6Anthu anga akuwonongeka chifukwa Ine sandidziŵa.

Ndidzakukanani kuti musanditumikire ngati ansembe,

chifukwa choti mwakana kuphunzitsa za Ine.

Mwaiŵala malamulo a Mulungu wanu,

tsono Inenso Mulungu wanu ndidzaiŵala ana anu.

7“Ansembe ankati akamachulukirachulukira,

ndi m'menenso ankanyanyira kundichimwira.

Ndidzasandutsa ulemu wao kuti ukhale manyazi.

8Amalemererapo pa kuchimwa kwa anthu anga,

ndipo amafunitsitsa kuti anthuwo azichimwirachimwira.

9Tsono ansembewo ndidzaŵachita

zomwe ndidzaŵachite anthu.

Ndidzaŵalanga chifukwa cha makhalidwe ao oipa

ndi kuŵalipsira pa ntchito zaozo.

10Azidzadya koma sadzakhuta.

Azidzachita zachiwerewere, koma sadzachulukana,

poti adasiya Chauta,

kuti adzipereke ku zachiwerewere.”

Chauta adzudzula chipembedzo chachikunja

11Chauta akuti,

“Vinyo, kaya ndi wakale kaya ndi watsopano,

amaononga nzeru.

12Anthu anga amapempha nzeru ku fano lamtengo,

ndipo amaombeza ndi ndodo yao.

Mzimu wonyansa waasokeretsa,

motero posiya Mulungu wao, akhala osakhulupirika.

13Amapereka nsembe pa mapiri,

amafukiza lubani pa zitunda,

patsinde pa mitengo yogudira monga thundu,

mnjale ndi mkundi,

chifukwa amati mithunzi yake njabwino.

“Nchifukwa chake ana anu aakazi

akuchita zachiwerewere,

ndipo akamwana anu akuchita zigololo.

14Koma sindidzaŵalanga ana anu aakazi

chifukwa chochita zachiwerewere,

sindidzaŵalanga akamwana anu

chifukwa cha zigololo zao.

Paja inu nomwe amunanu mumayenda ndi akazi achiwerewere,

ndipo mumapereka nsembe

pamodzi ndi akazi adama akuchipembedzo.

Anthu opanda nzeru chitere adzaonongeka.

15“Ngakhale Aisraele amachita zosakhulupirika,

anthu a ku Yuda asapezeke ndi mlandu wotere.

Asapite kukapembedza ku Giligala kapena ku Betehaveni.

Asakalumbirenso kumeneko kuti, ‘Pali Chauta wamoyo!’

16Aisraele ndi okanika ngati anaang'ombe.

Kodi Chauta angathe kuŵadyetsa tsopano

ngati anaankhosa pa busa lokoma?

17“Anthu a ku Efuremu aphathana ndi mafano, izo nzao.

18Amati akamwa kwambiri,

amangochita zigololo.

Amakonda zamanyazi kupambana ulemu wao.

19Adzachotsedwa ngati chinthu chotengedwa ndi mphepo,

ndipo adzachititsidwa manyazi

chifukwa cha nsembe zao zachikunja.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help