1Inu Chauta, ndidzaimba mosalekeza
nyimbo yotamanda chikondi chanu chosasinthika.
Ndidzalalika ndi pakamwa panga
za kukhulupirika kwanu ku mibadwo yonse.
2Chikondi chanu chosasinthika chakhazikika
kuti chikhale mpaka muyaya,
kukhulupirika kwanu nkwachikhalire ngati mlengalenga.
3Inu mwanena kuti,
“Ndachita chipangano ndi wosankhidwa wanga,
ndalumbira kwa Davide mtumiki wanga kuti,
4 2Sam. 7.12-16; 1Mbi. 17.11-14; Mas. 132.11; Ntc. 2.30 ‘Ndidzakhazikitsa zidzukulu zako mpaka muyaya,
ndidzasungira mibadwo yonse mpando wako waufumu.’ ”
5Zakumwamba zimatamanda zodabwitsa zanu, Inu Chauta,
zimatamanda kukhulupirika kwanu
mu msonkhano wa oyera mtima.
6Kodi ndani mu mlengalenga angathe kulingana ndi Chauta?
Ndani pakati pa akumwamba amafanafana naye?
7Mulungu ndiye amene amamuwopa
mu msonkhano wa anthu oyera mtima,
ndiye wamkulu ndi wolemekezeka
pakati pa onse omzungulira.
8Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse,
kodi ndani ali wamphamvu ngati Inu Chauta,
amene muli okhulupirika pa zonse?
9Mumalamulira nyanja yaukali.
Mafunde ake akakwera, Inu mumaŵakhalitsa bata.
10Mudatswanya chilombo cha m'nyanja
ndi kuchisandutsa mtembo.
Mudabalalitsa adani anu ndi mkono wanu wamphamvu.
11Zakumwamba ndi zanu, dziko lapansi nalonso ndi lanu.
Mudapanga dziko lonse ndi zonse zam'menemo.
12Mudalenga kumpoto ndi kumwera.
Mapiri a Tabori ndi Heremoni
akukutamandani ndi chimwemwe.
13Inu muli ndi mphamvu zonse.
Dzanja lanu ndi lamphamvu kwambiri,
dzanja lanu lamanja ndi lopambana.
14Maziko a ufumu wanu
ndiwo kulungama ndi kuweruza mosakondera.
Mumaonetsa chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika
pa zonse zimene mumachita.
15Ngodala anthu
amene mumaŵaphunzitsa kuimba nyimbo zachikondwerero,
amene amayenda m'chikondi chanu, Inu Chauta.
16Iwowo amakondwa masiku onse chifukwa cha Inu,
ndipo amatamanda kulungama kwanu.
17Amanyadira ulemerero wanu ndi mphamvu zanu.
Mphamvu zathu zalimba chifukwa mwatikomera mtima.
18Chauta ndiye chishango chathu,
Woyera wa Israele ndiye mfumu yathu.
19Kale mudalankhula m'masomphenya
kwa anthu anu okhulupirika, mudati,
“Ndamuveka chisoti chaufumu
munthu amene ali wamphamvu,
ndamukweza amene ali wosankhidwa pakati pa anthu.
20 1Sam. 13.14; Ntc. 13.22; 1Sam. 16.12 “Ndampeza Davide mtumiki wanga,
ndamdzoza ndi mafuta anga oyera,
21“Kotero kuti dzanja langa
lidzamchirikiza mpaka muyaya,
mkono wanganso udzamulimbitsa.
22“Adani sadzampambana,
anthu oipa sadzamtsitsa.
23Ndidzatswanya adani ake pamaso pake,
ndi kukantha odana naye.
24“Kukhulupirika ndiponso chikondi changa chosasinthika
zidzakhala naye,
ndidzalimbitsa mphamvu zake, kuti mbiri yanga isungike.
25Ndidzakuza ufumu wake kuchokera ku Nyanja Yaikulu
mpaka kukafika ku mtsinje wa Yufurate.
26“Iye adzandiwuza kuti,
‘Inu ndinu Atate anga, Mulungu wanga,
Thanthwe londipulumutsa.’
27 Chiv. 1.5 Ndithu ndidzamsandutsa mwana wanga wachisamba,
adzakhala wopambana mafumu a dziko lapansi.
28“Ndidzamkonda nthaŵi zonse
ndi chikondi changa chosasinthika,
chipangano changa ndi iye sichidzaphwanyika.
29Ndidzakhazikitsa zidzukulu zake pa mpando wachifumu,
mpaka muyaya,
ndipo ufumu wake udzakhala waukulu ngati mlengalenga.
30“Koma ngati ana ake asiya lamulo langa,
ndipo satsata malangizo anga,
31ngati aphwanya malamulo anga,
ndipo sasunga malangizo anga,
32“ndidzaŵalanga ndi ndodo,
chifukwa cha zolakwa zao,
ndidzaŵakwapula ndi zikoti
chifukwa cha machimo ao.
33Koma Davide sindidzamchotsera
chikondi changa chosasinthika,
sindidzakhala wosakhulupirika kwa iye.
34“Sindidzaswa chipangano changa,
kapena kusintha mau otuluka pakamwa panga.
35Ndidalumbira kamodzinkamodzi kuti,
‘Pali dzina langa loyera!
Sindidzamnamiza Davide.’
36“Zidzukulu zake sizidzatha mpaka muyaya,
mpando wake wachifumu udzakhalapo nthaŵi zonse,
monga m'mene likhalira dzuŵa pamaso panga.
37Ufumu wake udzakhazikika mpaka muyaya ngati mwezi,
mboni yanga yokhulupirika mu mlengalenga.”
Kulira chifukwa cha kugonjetsedwa kwa mfumu38Koma tsopano Inu mwamtaya ndi kumkana wodzozedwa wanu,
mwamkwiyira kwambiri.
39Mwakana chipangano chanu ndi mtumiki wanu,
mwadetsa m'fumbi chisoti chake chaufumu.
40Mwagumula makoma ake onse,
mwasandutsa malinga ake mabwinja.
41Onse odutsa amamlanda zinthu zake,
anzake amamunyodola.
42Mwalimbikitsa amaliwongo ake,
mwakondwetsa adani ake onse.
43Inde, mwabunthitsa lupanga lake,
ndipo simudamlimbitse pa nkhondo.
44Mwamchotsera ndodo yachifumu m'manja,
ndipo mwataya pansi mpando wake wachifumu.
45Mwamkalambitsa msanga,
mwamkuta ndi manyazi.
Pemphero lopempha chipulumutso46Kodi mpaka liti, Inu Chauta?
Kodi mudzandibisalira mpaka muyaya?
47Kumbukirani kuti masiku a moyo wanga ndi ochepa.
Zoonadi, mudalenga anthu onse
kuti akhale a moyo waufupi kwambiri.
48Kodi ndani angathe kukhala moyo osaona imfa?
Ndani angathe kupulumutsa moyo wake
polewa mphamvu za malo a anthu akufa?
49Ambuye, chili kuti
chikondi chanu chosasinthika chakale chija,
chimene mudachilumbirira Davide
kuti mudzakhala wokhulupirika?
50Ambuye, kumbukirani kunyozedwa kwa mtumiki wanune,
ndakhala ndikupirira chamumtima chipongwe cha anthu.
51Kumbukirani kuti amene akundinyozawo
ndi adani anu, Inu Chauta,
iwo akunyoza Wodzozedwa wanu paliponse pamene waponda.
52Chauta atamandike mpaka muyaya.
Inde momwemo. Inde momwemo.
BUKU LACHINAI(Mas. 90—106)Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.