1Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2“Iwe mwana wa munthu, ulengeze mau oimba mlandu abusa a Israele. Ulengeze, uŵauze kuti ‘Zimene akunena Ambuye Chauta ndi izi: Tsoka kwa inu abusa a ku Israele, amene mumangodzisamala inu nokha. Kodi suja abusa amayenera kusamala nkhosa?
3Chambiko mumadya, zaubweya mumavala, ndipo nyama zonenepa mumapha, koma nkhosa osasamala konse.
4Nkhosa zofooka simudazilimbikitse, zodwala simudazichiritse, zopweteka simudazimange mabala ake, zosokera simudazibweze, ndipo zotayika simudazifunefune. Koma munkaziŵeta mozunza ndi mwankhalwe.
5Num. 27.17; 1Maf. 22.17; Mt. 9.36; Mk. 6.34 Ndiye zinkangoti balalabalala, poti panalibe mbusa. Motero zidasanduka chakudya cha zilombo zonse zakuthengo.
6Nkhosa zanga zidamwazikana nkumangoyendayenda ku mapiri ndi ku magomo ataliatali. Zidabalalikira m'dziko lonse popanda wina wozilondola kapena kuzifunafuna.’
7“Tsono abusa inu, tamverani zimene Ine Chauta ndikukuuzani:
8Pali ine ndemwe, nkhosa zanga zidajiwa ndi zilombo zakuthengo, zidasanduka chakudya cha zilombo chifukwa chosoŵa abusa. Abusa anga sadalondole nkhosa zanga, ankangosamala za iwo okha, osasamala nkhosa.
9Nchifukwa chake abusa inu, imvani mau a Ine Chauta.
10Ndikuti, Ndaipidwa nanu abusanu. Ndidzakulandani nkhosa zanga, simudzazidyetsanso. Ndidzakuchotsani pa ntchito yaubusa, kuti musadzasamalenso za inu nokha. Ndidzapulumutsa nkhosa zanga kukamwa kwanu, ndipo simudzazidyanso.
Mbusa wabwino11“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi, Tsopano nkhosa zangazo ndidzazifunafuna ndekha mwiniwakene, ndipo ndidzazisamala.
12Monga mbusa amanka nafunafuna nkhosa zake, pamene zina zabalalikira kutali, Inenso ndidzatero, kunka ndikufunafuna nkhosa zanga. Ndidzazipulumutsa konse kumene zidamwazikira pa nthaŵi yamdima ndi yankhungu.
13Ndidzazitulutsa pakati pa mitundu yonse ya anthu, ndidzazisonkhanitsa kuchokera ku maiko ena, ndipo ndidzazibwezera ku dziko lakwao. Ndidzaziŵetera ku mapiri a ku Israele, pafupi ndi mitsinje yake, ndi ku malo onse abwino kumene anthu amakhalako.
14Ndidzaziŵetera ku mabusa abwino, ndipo zizidzadya msipu wonenepetsa ku mapiri okwera a Israele. Kumeneko zidzapumula ku mabusa abwino amsipu. Zidzapezadi mabusa abwino ku mapiri a Israele.
15Ineyo mwiniwake ndidzakhala mbusa wa nkhosa zanga. Ndipo Ine ndemwe ndizidzazipumulitsa. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
16Zotayika ndidzazifunafuna, zosokera ndidzazibweza, zopweteka ndidzazimanga mabala ake. Zofooka ndidzazilimbikitsa, koma zonenepa ndi zamphamvu ndidzaziwononga. Ndidzaŵeta nkhosa zanga mwachilungamo.”
17“Tsono kunena za inu, nkhosa zanganu, Ine Ambuye Chauta ndikukuuzani kuti, Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ndi nkhosa, pakati pa nkhosa zamphongo ndi atonde.
18Kodi inu simukhutira kudya pa busa labwino? Nanga mumaponderezeranji zimene simudya? Kodi simukhutira kumwa madzi abwino? Nanga madzi amene simumwa mumaŵadetsereranji ndi mapazi anu?
19Kodi mukufuna kuti nkhosa zanga zizidya udzu umene mudaponderezawo, ndi kumamwa madzi amene mudadetserera?
20“Tsono Ine Ambuye Chauta ndikukuuzani kuti, Ineyo mwiniwake ndidzaweruza ndekha pakati pa inu nkhosa zonenepanu ndi zinzanu zoondazo.
21Zofooka mumaziwomba ndi kuzikankhira kumbali, ndipo mumazigunda ndi nyanga zanu nkuzimwazira kutali.
22Koma ndidzazipulumutsa nkhosa zangazo, ndipo sindidzalolanso kuti zijiwe. Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ina ndi nkhosa inanso.
23Chiv. 7.17Ndidzaziikira mbusa mmodzi, mtumiki wanga Davide. Iyeyo ndiye azidzazisamala, ndipo adzakhala mbusa wake.
24Ezek. 37.24Pamenepo Ine Chauta ndidzakhala Mulungu wake, ndipo mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yake. Ndatero Ineyo Chauta.”
25“Ndidzapangana nazo chipangano chamtendere. Zilombo zonse zolusa ndidzazichotsa m'dziko, kuti nkhosa zanga zizidzakhala mwamtendere, ngakhale m'chipululu kapena m'thengo.
26Ndidzakhazika anthu anga kufupi ndi phiri langa, ndipo ndidzaŵagwetsera mvula pa nthaŵi yake, mvula yake ya madalitso.
27Mitengo ya m'minda idzabereka zipatso, ndipo minda idzakhala ndi zokolola zake, tsono anthu adzakhala mwamtendere m'dziko lao. Adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, pamene ndidzathyole magoli ao ndi kuŵapulumutsa kwa amene adaŵagwira ukapolo.
28Anthu a mitundu ina sadzaŵafunkhanso, ndipo zilombo zakuthengo sizidzaŵadya. Adzakhala mwamtendere popanda wina woŵaopsa.
29Ndidzachulukitsa zolima zao, mwakuti sadzafanso ndi njala m'dzikomo, ndipo choncho anthu a mitundu ina sadzaŵanyozanso.
30Motero adzadziŵa kuti Ine Chauta Mulungu wao ndili nawo, ndipo kuti iwowo, Aisraelewo, ndi anthu anga. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
31‘Inu ndinu nkhosa zanga, nkhosa zimene ndimadyetsa, ndipo Ine ndine Mulungu wanu. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.’ ”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.