1Ngwodala mwamuna amene ali ndi mkazi wabwino,
mkazi wotere amaŵirikiza masiku
a moyo wa mwamuna wake.
2Mkazi wokhulupirika amasangalatsa mwamuna wake,
ndipo mwamunayo adzakhala ndi mtendere
pa moyo wake wonse.
3Mkazi wabwino ndi dalitso lalikulu,
ndi imodzi mwa mphatso zamtengowapatali,
zimene Ambuye amasungira anthu oŵaopa.
4Ngakhale alemere kapena asauke,
anthu ameneŵa adzakhala okondwa,
nthaŵi zonse adzaoneka osangalala.
5Pali zinthu zitatu izi
zimene mtima wanga umaopa,
ndi china chachinai
chimene ndimachita nacho mantha:
ukazitape womveka mumzinda monse,
kusonkhana kwa gulu la anthu okwiya, ndi kusinjirira.
Zonsezi ndi nzoipa koposa imfa.
6Mkazi wansanje amaŵaŵitsa mtima
ndi kumvetsa chisoni,
aliyense amamva mau ake olasa.
7Mkazi woipa ali ngati goli lang'ombe lolasa m'khosi,
kuyesa kumugonjetsa
ndiye ngati ukugwira chinkhanira.
8Mkazi wauchidakwa amaŵaŵitsa mtima,
sangathe kubisa manyazi ake.
9Mkazi wachimasomaso amadziŵika ndi kapenyedwe kake,
ungathe kumzindikira pakungoyang'ana zikope zake.
10Uzimuyang'anira bwino mwana wako wamkazi wochita mwano.
Ukamlekerera pang'ono, adzangochita zakezake.
11Uchenjere nawo maso ake opanda manyazi,
ndipo usadabwe ngati akukokera ku zoipa.
12Munthu woyenda pa ulendo amamwa madzi aliwonse
amene waŵapeza.
Chimodzimodzinso mkaziyo amangodikira apa ndi apa,
nkuvomera aliyense amene wamufuna.
13Ubwino wa mkazi umakondweretsa mwamuna wake,
luso lake limanenepetsa thupi la mwamuna wake.
14Mkazi wosalankhula zambiri ndi mphatso yochoka kwa Ambuye,
palibe chuma cholingana ndi mkazi wodziŵa mwambo.
15Mkazi wodzisunga bwino amasangalatsa moŵirikiza,
palibe chinthu choposa mtima wopanda dama.
16Mkazi wokongola wosamala bwino za m'nyumba mwake
ngwokoma ngati dzuŵa
lotuluka m'maŵa mu mlengalenga wa Ambuye.
17Nkhope yokongola yokhala pa thupi lopangidwa bwino njoŵala
ngati nyale yokhala pa choikapo chake m'Nyumba ya Ambuye.
18Miyendo yake yokongola yoima pa mapazi olimba
ili ngati mizati yagolide pa tsinde lasiliva.
19Mwana wanga, khala ndi moyo wabwino
pa unyamata wako,
usapereke mphamvu zako
kwa anthu achilendo.
20Ufunefune m'chigwa monse malo achonde,
ndipo ubzalemo mbeu zako mokhulupirira ubwino wa mtundu wako.
21Tsono ana ako amene udzasiya kumbuyo kwako
adzakula bwino akunyadira ulemerero wa makolo ao.
22Mkazi wadama ali ngati malovu chabe.
Mkazi wokwatiwa ali ngati nsanja yopheramo odzamnyenga.
23Mkazi wosaopa Mulungu ngwoyenera mwamuna wosalabadira za Malamulo.
Koma munthu woopa Ambuye adzalandira mkazi wokonda za Mulungu.
24Mkazi wopanda manyazi amakonda kudzinyazitsa,
koma mkazi wa makhalidwe abwino amakhala wodzichepetsa
ngakhale pamene ali yekha ndi mwamuna wake.
25Mkazi wodzikuza ali ngati galu,
koma mkazi wa makhalidwe abwino amaopa Ambuye.
26Mkazi wolemekeza mwamuna wake
amaoneka wanzeru kwa aliyense,
koma wonyoza mwamuna wake monyada
onse amamudziŵa kuti ndi woipa.
Ngwodala mwamuna
amene ali ndi mkazi wabwino,
chifukwa adzakhala ndi moyo
nthaŵi yaitali.
27Mkazi wam'kamwa ndi wolongolola
ali ngati kulira kwa lipenga lankhondo loputa adani.
Mwamuna wokhala ndi mkazi wotere,
ali pa phokoso lankhondo nthaŵi zonse.
Za zinthu zokhumudwitsa28Pali zinthu ziŵiri izi
zimene zimandipweteka mtima,
ndi china chachitatu
chimene chimandikwiyitsa:
msilikali wosauka chifukwa cha umphaŵi,
anthu anzeru omanyozedwa
ndipo munthu wolungama wosandukanso woipa.
Wotereyu Mulungu amamukonzera imfa
yochita kuphedwa.
Za malonda29Nkwapatali kuti munthu wamalonda apewe
machitidwe oipa.
Nkwapatali kuti munthu wogulitsa zinthu apezeke
wosachimwa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.