1Munthu wachikulire usamdzudzule mokalipa, koma umchenjeze monga ngati bambo wako. Amuna achinyamata uzikhalitsana nawo ngati abale ako.
2Azimai achikulire uzikhalitsana nawo ngati amai ako, ndipo azimai a zaka zochepa uzikhalitsana nawo ngati alongo ako, m'kuyera mtima kwenikweni.
3Uziŵachitira ulemu azimai amasiye, amenetu ali amasiye enieni.
4Koma ngati mai wamasiye ali ndi ana kapena adzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wao pa banja lao moopa Mulungu, kuti pakutero abwezere makolo ao zimene adalandira kwa iwo. Pakuti zimenezi Mulungu amakondwera nazo akamaziwona.
5Yud. 8.4-6Mai amene ali wamasiye kwenikweni, wopanda wina aliyense womsamala, ameneyo waika chiyembekezo chake pa Mulungu, ndipo amapemphera kosalekeza usana ndi usiku kuti Mulungu azimthandiza.
6Koma mai wamasiye amene amangodzisangalatsa ndi zapansipano, ameneyo wafa kale ngakhale akali moyo.
7Uziŵalamula zimenezi, kuti akhale opanda mlandu.
8Ngati wina aliyense saŵapatsa zofunika achibale ake, makamaka a m'banja mwake momwe, ameneyo wataya chikhulupiriro chake, ndipo kuipa kwake nkoposa kwa munthu wosakhulupirira.
9Wina aliyense asaloledwe kuloŵa m'gulu la azimai amasiye, asanakwanitse zaka 60. Akhale woti adakwatiwapo ndi mwamuna mmodzi yekha.
10Akhale mai woti anthu amamchitira umboni wakuti amachitadi ntchito zabwino. Akhale woti ankalera ana ake bwino, ankalandira bwino alendo, ankasambitsa mapazi a anthu a Mulungu, ndipo ankathandiza anthu amene anali m'mavuto. Akhalenso mai woti ankadzipereka pa ntchito zonse zabwino.
11Koma azimai amasiye a zaka zochepera uzikana kuŵalemba m'gulu limeneli. Pajatu zilakolako zao zikayamba kuŵavutitsa nkuŵalekanitsa ndi Khristu, amangofuna kukwatiwanso.
12Pamenepo amapezeka olakwa, chifukwa chosasunga lonjezo lao loyamba.
13Kuwonjezera pamenepo, amagwa m'chizoloŵezi cha kungokhala khale, motero amangoyendayenda ku nyumba za anthu. Tsonotu samangokhala khale chabe ai, amachitanso miseche nkumaloŵera za eni, ndi kukhala omalankhula zimene samayenera kulankhula.
14Nchifukwa chake nkadakonda kuti azimai amasiye a zaka zochepera azikwatiwanso, abale ana, ndipo azisamala bwino panyumba pao, kuti adani athu asapeze mpata wotisinjirira.
15Paja alipo kale azimai amasiye ena amene adapatukapo nkumatsata Satana.
16Koma ngati mai wina aliyense wachikhristu ali ndi achibale amene ali azimai amasiye, aziŵasamala iyeyo, osasenzetsa mpingo katundu wakeyo. Motero mpingo udzatha kusamala azimai amasiye opanda oŵathandiza.
17Akulu a mpingo otsogolera mpingo bwino, akhale oyenera kuŵalemekeza moŵirikiza, makamaka amene amagwira ntchito yolalika mau a Mulungu ndiponso yophunzitsa.
18Deut. 25.4; Mt. 10.10; Lk. 10.7 Paja Malembo akuti, “Usaimange pakamwa ng'ombe imene ikupuntha tirigu.” Penanso akuti, “Wantchito ngwoyenera kulandira malipiro ake.”
19Deut. 17.6; 19.15 Usamamvere mau oneneza mkulu wa mpingo, pokhapokha ngati pali mboni ziŵiri kapena zitatu.
20Opitirirabe kuchimwa uziŵadzudzula pamaso pa onse, kuti ena onsewo achite mantha.
21Pamaso pa Mulungu, pamaso pa Khristu Yesu, ndi pamaso pa angelo onse osankhidwa, ndikukulamula ndithu kuti uzitsata malamulo ameneŵa mopanda tsankho, ndipo kuti usachite chilichonse mokondera.
22Usafulumire kumsanjika manja munthu, ndipo usavomerezane ndi anthu ena pa uchimo wao. Iwe usunge bwino kuyera mtima kwako.
23Uleke kumangomwa madzi okha. Koma uzimwako vinyo pang'ono, paja umavutika ndi m'mimba, ndiponso chifukwa cha kudwaladwala kwako kuja.
24Pali anthu ena amene machimo ao amaonekeratu poyera asanakambe nkomwe mlandu wao, m'menemo ena machimo ao amayamba kudziŵika pokamba mlandu.
25Momwemonso ntchito zokoma zimaonekera poyera, ndipo ngakhale zipande kutero, sizingathe kubisika nthaŵi zonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.