Yak. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za kuchita chibwenzi ndi dziko lapansi

1Kodi nkhondo zimachokera kuti? Kukangana pakati panu kumachokera kuti? Kodi suja zimachokera ku zilakolako zanu zathupi, zimene zimachita nkhondo mwa inu?

2Mumalakalaka zinthu, koma zimakusoŵani, nchifukwa chake mumapha munthu. Mumasirira zinthu, koma simungathe kuzipeza, nchifukwa chake mumamenyana, nkumachita nkhondo. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu.

3Ndipo ngakhale mupemphe, simulandira, chifukwa mumapempha molakwa. Zimene mumapempha, mumafuna kungozimwazira pa zokukondweretsani basi.

4Inu anthu osakhulupirikanu, kodi simudziŵa kuti kuchita chibwenzi ndi zapansipano nkudana ndi Mulungu? Choncho munthu wofuna kukhala bwenzi la zapansipano, ameneyo amadzisandutsa mdani wa Mulungu.

5Kodi kapena mukuyesa kuti Malembo amanena pachabe kuti, “Mulungu amafunitsitsa mwansanje mzimu umene Iye adaika kuti uzikhala mwa ife?”

6Miy. 3.34 Koma amatikomera mtima koposa. Nchifukwa chake Malembo akuti, “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma odzichepetsa amaŵakomera mtima.”

7Tsono muzigonjera Mulungu. Satana muzilimbana naye, ndipo adzakuthaŵani.

8Yandikirani kwa Mulungu, ndipo Iye adzayandikira kwa inu. Muzisamba m'manja, inu anthu ochimwa. Chotsani maganizo onyenga m'mitima mwanu, inu anthu okayikakayika.

9Zindikirani umphaŵi wanu, imvani chisoni, lirani misozi. Kuseka kwanu kusanduke kulira, ndipo chimwemwe chanu chisanduke chisoni.

10Mudzichepetse pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.

Aŵachenjeza kuti asamaweruza mbale wao

11Abale, musamasinjirirana. Wosinjirira mbale wake kapena kumuweruza, akusinjirira ndi kuweruza Malamulo a Mulungu. Koma ukaweruza Malamulo a Mulungu, ndiye kuti sukuchita zimene Malamulowo akunena, ukudziyesa woweruza.

12Mulungu yekha ndiye wopanga Malamulo ndiponso woweruza. Ndiyenso wotha kupulumutsa ndi kuwononga. Nanga iwe ndiwe yani kuti uziweruza mnzako?

Aŵachenjeza kuti asamadzitama

13 Miy. 27.1 Lun. 2.4; 5.9-13 Onani tsono, inu amene mukuti, “Lero kapena maŵa tipita ku mzinda wakutiwakuti, ndipo tikachitako malonda chaka chimodzi kuti tikaphe ndalama,”

14m'menemo inuyo zamaŵa simukuzidziŵa. Kodi moyo wanu ngwotani? Pajatu inu muli ngati utsi chabe, umene umangooneka pa kanthaŵi, posachedwa nkuzimirira.

15Kwenikweni muyenera kumanena kuti, “Ambuye akalola, tikakhala ndi moyo, tidzachita chakutichakuti.”

16Koma monga zilirimu, mumanyada ndi kudzitama. Kunyada konse kotere nkoipa.

17Munthu akadziŵa zabwino zimene ayenera kuchita, napanda kuzichita, ndiye kuti wachimwa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help