Zek. 14 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zodzachitika pa tsiku la Chauta

1Onani, tsiku likubwera, la Chauta, pamene zinthu zomwe adani ako adakulanda, azidzagaŵana iwe uli pomwepo.

2Chauta adzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse kuti adzathire nkhondo Yerusalemu. Adzaulanda mzindawo ndi kuphwasula nyumba zonse, ndipo akazi am'menemo adzaŵachita chigololo. Theka la anthu a mu mzindawo lidzatengedwa ukapolo, koma ena onse otsala mumzindamo sadzachotsedwa.

3Pambuyo pake Chauta adzabwera kudzamenyana ndi adani amenewo, monga m'mene amachitira pa tsiku la nkhondo.

4Tsiku limenelo adzaimirira pa phiri la Olivi loyang'anana ndi Yerusalemu chakuvuma, ndipo phirilo lidzagaŵika paŵiri ndi chigwa chachikulu choyenda kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe. Theka la phiri lidzasunthira chakumpoto, theka lina chakumwera.

5Inu mudzapulumuka podzera m'chigwa chimenecho cha pakati pa mapiri. Mudzathaŵa monga m'mene mudaathaŵira nthaŵi ija ya chivomezi pa nthaŵi ya Uziya mfumu ya ku Yuda. Kenaka Chauta, Mulungu wanu, adzabwera pamodzi ndi oyera ake onse.

6Tsiku limenelo sikudzatentha, sikudzazizira ndipo sikudzachita chisanu chambee.

7Lidzakhala tsiku la kuŵala kokhakokha, osakhala usana, osakhala usiku, chifukwa ndi madzulo omwe kuzidzaŵalabe. Tsiku limene zidzachitike zimenezi ndi Chauta yekha akulidziŵa.

8 Ezek. 47.1; Yoh. 7.38; Chiv. 22.1 Tsiku limenelo madzi a moyo adzatuluka ku Yerusalemu. Theka la madziwo lidzathira m'nyanja yakuvuma, theka lina lidzathira m'nyanja yakuzambwe. Zimenezi zidzachitika pa nthaŵi yachilimwe ndi yachisanu yomwe.

9Tsono Chauta adzakhala mfumu ya dziko lonse lapansi. Tsiku limenelo Chauta yekha anthu onse adzampembedza, adzamdziŵa ndi dzina lake limodzi lokhalo.

10Dziko lonse adzalisalaza kuyambira ku Geba mpaka ku Rimoni, kumwera kwa Yerusalemu. Koma Yerusalemu adzakwezedwa pamalo pakepo, kuyambira ku chipata cha Benjamini mpaka ku malo amene kunali chipata chakale mpaka ku chipata chapangodya, ndiponso kuchokera ku Nsanja ya Hananele mpaka ku malo opondera mphesa za mfumu.

11Chiv. 22.3Anthu adzakhala ku Yerusalemu mwamtendere, poti sadzaopsezedwanso ndi chiwonongeko kumeneko.

12Pambuyo pake Chauta adzalanga ndi mliri adani onse amene ankamenyana nkhondo ndi Yerusalemu. Matenda ake adzakhala motere: matupi ao adzaola eni ake akuyendabe, maso ao adzaola ali chikhalire m'malo mwake, ndipo malilime ao adzaola m'kamwa mwao.

13Pa tsiku limenelo Chauta adzasokoneza anthu ndi mantha aakulu, mpaka aliyense adzagwira dzanja la mnzake, ndipo adzayamba kumenyana okhaokha.

14Nawonso anthu a ku Yuda adzachita nkhondo ku Yerusalemu. Ndipo chuma cha anthu a mitundu yozungulira adzachisonkhanitsa pamodzi. Chuma chake ndi golide ndi siliva wambiri ndiponso zovala zochuluka.

15Mliri uja udzaphanso akavalo, ngamira ndi abulu a mitundu yonse, ndiponso nyama zonse zokhala ku zithando zankhondo.

16 Lev. 23.39-43 Zitatha zimenezi anthu onse otsala mwa adani amene ankamenyana ndi Yerusalemu, azidzabwera chaka ndi chaka kudzapembedza Mfumu, Chauta Wamphamvuzonse, ndiponso kudzachita chikondwerero chamisasa.

17Ngati mabanja ena pa dziko lapansi sadzapita ku Yerusalemu kukapembedza Mfumu, Chauta Wamphamvuzonse, mvula sidzaŵagwera.

18Ngati anthu a ku Ejipito sadzapita kukaonekera kumeneko, adzalandiranso chilango chonga chomwe Chauta adzalange nacho mtundu wina uliwonse wa anthu osapita kukachita chikondwerero chamisasa.

19Chimenechi ndicho chidzakhale chilango cha Aejipito ndiponso cha mtundu uliwonse wa anthu amene sadzachita nao chikondwerero chamisasacho.

20Pa tsiku limenelo pa mabelu ovala akavalo ankhondo padzalembedwa mau akuti, “Woperekedwa kwa Chauta.” Ndipo mbiya za ku Nyumba ya Chauta nazonso zidzakhala zoyera ngati mbale zakuguwa.

21Mbiya iliyonse ya ku Yerusalemu ndi ku Yuda idzakhala yoperekedwa kwa Chauta Wamphamvuzonse. Onse opereka nsembe ku Yerusalemu adzagwiritsa ntchito mbiyazo pophika nyama za nsembe. Nthaŵi imeneyo ikadzafika, sipadzaonekanso wamalonda aliyense m'Nyumba ya Chauta Wamphamvuzonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help