1Pa tsiku limene Mose adamaliza kumangitsa chihema cha Mulungu, nachidzoza ndi kuchipatula, pamodzi ndi zipangizo zake, adadzozanso guwa lansembe ndi kulipatula pamodzi ndi ziŵiya zake zomwe.
2Tsiku lomwelo akulu a Aisraele, ndiye kuti atsogoleri a mabanja ndi a mafuko amene ankayang'anira kuŵerenga kuja,
3adatenga zopereka zao, ndipo adabwera nazo pamaso pa Chauta. Adapereka ngolo zophimbidwa zisanu ndi imodzi ndiponso ng'ombe khumi ndi ziŵiri: atsogoleri aŵiri ngolo imodzi, ndipo mtsogoleri aliyense ng'ombe imodzi. Zimenezo adafika nazo ku chihema cha Chauta.
4Tsono Chauta adauza Mose kuti,
5“Ulandire zimenezi kwa anthuwo kuti zithandize potumikira m'chihema chamsonkhano. Uŵapatse Alevi zimenezo, aliyense zoyenera ntchito yake.”
6Choncho Mose adatenga ngolo ndi ng'ombe zija nazipereka kwa Alevi.
7Ana a Geresoni adaŵapatsa ngolo ziŵiri ndi ng'ombe zinai potsata ntchito yao.
8Ana a Merari adaŵapatsa ngolo zinai ndi ng'ombe zisanu ndi zitatu potsata ntchito yao, imene woyang'anira wake anali Itamara, mwana wa wansembe Aroni.
9Koma ana a Kohati sadaŵapatse kanthu, chifukwa iwowo anali ndi ntchito yosamala zinthu zoyera zimene ankanyamulira pa phewa.
10Pambuyo pake atsogoleri adabwera ndi zopereka zopatulira guwa pa tsiku lomwe adalidzozalo. Ndipo adafika nazo zopereka zao patsogolo pa guwalo.
11Apo Chauta adauza Mose kuti, “Atsogoleriwo azibwera ndi zopereka zao zopatulira guwa, mtsogoleri mmodzi pa tsiku.”
12Nasoni mwana wa Aminadabu, wa fuko la Yuda, ndiye adapereka zopereka zake pa tsiku loyamba.
13Adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wolemera magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, zoperekera za zakudya.
14Adaperekanso kambale kamodzi kagolide kolemera magaramu 110, kodzaza ndi lubani.
15Adaperekanso mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza.
16Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo.
17Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali izi: ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zimene zinali zopereka za Nasoni mwana wa Aminadabu.
18Netanele mwana wa Zuwara, mtsogoleri wa fuko la Isakara, adapereka zopereka zake pa tsiku lachiŵiri.
19Zopereka zake zinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, zoperekera za zakudya.
20Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzadza ndi lubani,
21mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza.
22Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo.
23Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zisanu zamphongo, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Netanele mwana wa Zuwara.
24Tsiku lachitatu linali la Eliyabu mwana wa Heloni mtsogoleri wa Azebuloni.
25Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, zoperekera za zakudya.
26Adaperekanso kambale kamodzi kagolide kolemera magaramu 110, kodzaza ndi lubani,
27mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza.
28Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo.
29Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Eliyabu mwana wa Heloni.
30Tsiku lachinai linali la Elizuri mwana wa Sedeuri, mtsogoleri wa Arubeni.
31Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wolemera magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ndi zopereka za zakudya.
32Adaperekanso kambale kamodzi kagolide kolemera magaramu 110, kodzaza ndi lubani,
33mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza.
34Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo.
35Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa amphongo asanu a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Elizuri mwana wa Sedeuri.
36Tsiku lachisanu linali la Selumiele mwana wa Zurishadai, mtsogoleri wa Asimeoni.
37Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya.
38Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani,
39mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza.
40Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo.
41Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Selumiele mwana a Zurishadai.
42Tsiku lachisanu ndi chimodzi linali la Eliyasafu mwana wa Deuwele mtsogoleri wa Agadi.
43Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya.
44Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani,
45mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza.
46Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo.
47Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Eliyasafu mwana wa Deuwele.
48Tsiku lachisanu ndi chiŵiri linali la Elisama mwana wa Amihudi, mtsogoleri wa Aefuremu.
49Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya.
50Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani,
51mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza.
52Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo.
53Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zimene zinali zopereka za Alisama mwana wa Amihudi.
54Tsiku lachisanu ndi chitatu linali la Gamaliele mwana wa Pedazuri, mtsogoleri wa Amanase.
55Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya.
56Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani,
57mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza.
58Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo.
59Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zimene zinali zopereka za Gamaliele mwana wa Pedazuri.
60Tsiku lachisanu ndi chinai linali la Abidani mwana wa Gideoni, mtsogoleri wa Abenjamini.
61Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya.
62Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani,
63mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza.
64Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo.
65Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zimene zinali zopereka za Abidani mwana wa Gideoni.
66Tsiku lakhumi linali la Ahiyezere mwana wa Amishadai, mtsogoleri wa Adani.
67Iye adapereka mbale yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya.
68Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani,
69mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza.
70Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo.
71Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Ahiyezere mwana wa Amishadai.
72Tsiku la 11 linali la Pagiyele mwana wa Okarani, mtsogoleri wa fuko la Asere.
73Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya.
74Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani,
75mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza.
76Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo.
77Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zimene zinali zopereka za Pagiyele mwana wa Okarani.
78Tsiku la 12 linali la Ahira mwana wa Enani, mtsogoleri wa Anafutali,
79Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya.
80Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzadza ndi lubani,
81mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza;
82tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo.
83Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Ahira mwana wa Enani.
84Zopereka zopatulira guwa zimene atsogoleri a Aisraele adapereka pa tsiku limene guwalo lidadzozedwa, nazi: adapereka mbale zasiliva khumi ndi ziŵiri, mikhate yasiliva khumi ndi iŵiri, timbale tagolide khumi ndi tiŵiri.
85Mbale yasiliva iliyonse inkalemera kilogaramu limodzi ndi theka, ndipo mkhate uliwonse unkalemera magaramu 800. Siliva yense wa zipangizo zimenezo, ankalemera makilogaramu 27 ndi theka, potsata muyeso wa ku malo opatulika.
86Timbale khumi ndi tiŵiri tagolide todzaza ndi lubani timene tinkalemera kalikonse magaramu 110, potsata muyeso wa ku malo opatulika, tonse pamodzi tinkalemera ngati kilogaramu limodzi ndi theka.
87Nyama zonse zoperekera nsembe zopsereza zinali ng'ombe zamphongo khumi ndi ziŵiri, nkhosa zamphongo khumi ndi ziŵiri, anaankhosa amphongo a chaka chimodzi khumi ndi aŵiri, pamodzi ndi chopereka cha chakudya, ndiponso atonde khumi ndi aŵiri operekera nsembe zopepesera machimo.
88Ndipo nyama zonse za nsembe zachiyanjano zinali ng'ombe zamphongo 24, nkhosa zamphongo 60, atonde 60, ndi anaankhosa amphongo a chaka chimodzi 60. Zimenezi ndizo zinali zopereka zopatulira guwa atalidzoza.
89Tsono Mose ataloŵa m'chihema chamsonkhano kukalankhula ndi Chauta, adamva mau kuchokera pa chivundikiro chokhala pamwamba pa Bokosi laumboni, pakati pa akerubi. Mulungu adalankhula naye.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.