1Tsono Hiramu mfumu ya ku Tiro adatuma akazembe ake kwa Solomoni, atamva kuti adamdzoza ufumu m'malo mwa bambo wake, poti Hiramuyo ankakondana ndi Davide nthaŵi zonse.
2Ndipo Solomoni adabweza mau kwa Hiramu akuti,
3“Mukudziŵa kuti Davide, bambo wanga, sadathe kumangira nyumba Chauta Mulungu wake, chifukwa cha nkhondo zomwe adani ake adaamzinga nazo mbali zonse. Koma potsiriza Chauta adapereka adani akewo mu ulamuliro wake.
4Tsopano Chauta Mulungu wanga wandipatsa mtendere mbali zonse za dziko, kotero kuti ndilibe mdani kapena chovuta chilichonse.
52Sam. 7.12, 13; 1Mbi. 17.11, 12Choncho ndikufuna kumangira nyumba Chauta Mulungu wanga, monga momwe Iye adaauzira bambo wanga Davide kuti, ‘Mwana wako amene ndidzamukhazike pa mpando wako waufumu m'malo mwako, ndiye amene adzandimangire nyumba.’
6Nchifukwa chake tsono, mulamule anthu anu kuti andidulire mikungudza ya ku Lebanoni. Tsono anthu anga adzagwira ntchito pamodzi ndi anthu anuwo, ndipo ine ndidzakulipirani chifukwa cha anthu anu malipiro amene mungatchule. Inu mukudziŵa kuti pakati pathupa, palibe munthu wodziŵa kudula mitengo ngati Asidoni.”
7Tsono Hiramu atamva mau a Solomoniwo, adakondwa kwambiri, ndipo adati, “Lero Chauta atamandike chifukwa adapatsa Davide mwana wanzeru kuti alamulire mtundu wotchukawu.”
8Ndipo adabweza mau kwa Solomoni akuti, “Ndamva zimene mwandipempha. Ndili wokonzeka kuchita zonse zimene mukufunazo, zoti anthu anga akudulireni mitengo ya mkungudza ndi ya paini.
9Anthu anga adzatsika nayo kuchokera kuno ku Lebanoni mpaka ku nyanja. Ndipo adzaiyandamitsa pa madzi pa phaka, kuti apite nayo ku malo amene munene. Tsono adzaimasulira kumeneko, ndipo inu mudzailandira. Chofuna ine nchongoti inuyo mudzandipatse chakudya chodyetsa anthu anga.”
10Choncho Hiramu adapereka kwa Solomoni mitengo yonse ya mkungudza ndi ya paini imene ankakhumbayo.
11Ndipo Solomoni adapatsa Hiramu tirigu wokwanira mitanga 20,000 kuti akhale chakudya cha anthu ake, ndiponso mafuta oyenga bwino okwanira mbiya zikuluzikulu 20,000. Ankapereka zimenezi kwa Hiramu chaka ndi chaka.
12Tsono Chauta adampatsa Solomoni nzeru monga momwe adaalonjezera. Choncho panali mtendere pakati pa Hiramu ndi Solomoni, ndipo aŵiriwo adachita chipangano cha ubwenzi.
13Mfumu Solomoni adayambitsa ntchito yathangata m'dziko lonse la Israele. Ndipo anthu athangatawo analipo 30,000.
141Maf. 12.18 Ankaŵatuma ku Lebanoni anthu 10,000 pamwezi, mosinthanasinthana. Ku Lebanoni ankakhalako mwezi umodzi, ndipo kwao ankakhalako miyezi iŵiri. Adoniramu ndiye amene ankayang'anira ntchito yathangatayo.
15Solomoni analinso ndi anthu amtengatenga 70,000, ndi anthu 80,000 osema miyala ku dziko lamapiri.
16Analinso ndi akapitao 3,300 amene ankayang'anira anthu ogwira ntchito.
17Mfumu idalamula kuti anthuwo akumbe ndi kusema miyala ikuluikulu yabwino kwabasi, yoti akamangire maziko a Nyumba ya Chauta.
18Amisiri omanga a Solomoni, pamodzi ndi a Hiramu, ndiponso anthu a ku Gebala, ndiwo amene ankasema miyala, ndi kukonza mitengo ndi miyala yomangira Nyumbayo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.