1Tsiku limenelo m'dziko la Yuda anthu adzaimba nyimbo iyi yakuti,
“Tili ndi mzinda wamphamvu,
Mulungu amautchinjiriza ndi zipupa ndi malinga.
2Tsekulani zipata za mzinda,
kuti mtundu wotsata malamulo ndi wokhulupirika uloŵe.
3Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni
kwa amene ali ndi mtima wokhazikika,
chifukwa chokhulupirira Inu.
4Inu anthu, mukhulupirire Chauta mpaka muyaya,
chifukwa chakuti Chauta Mulungu ndiye thanthwe losatha.
5Iye watsitsa anthu okhala pa malo okwera,
waononga mzinda wamphamvu uja.
Wagumula zipupa zake,
ndipo waugwetsera pansi, pafumbi penipeni.
6Mapazi a anthu akuupondereza,
mapazi a anthu otsika,
mapazi a anthu osauka.”
7Inu Chauta ndinu Wolungama,
mumasalaza njira ya munthu womvera inu,
8Inu Chauta, ife timatsata njira ya malamulo anu,
ndipo timakhulupirira Inu.
Mtima wathu umangolakalaka kukumbukira
ndi kulemekeza dzina lanu.
9Mtima wanga wonse umalakalaka Inu usiku,
mzimu wanga m'kati mwa ine umakufunafunani.
Pamene muweruza dziko lapansi,
anthu onse okhalamo amaphunzira chilungamo.
10Munthu woipa mukamchitira zabwino,
saphunzira zachilungamo.
Amachita zoipa m'dziko lachilungamoli,
ndipo amalephera kuzindikira ukulu wa Chauta.
11 Ahe. 10.27 Inu Chauta, mwasamula dzanja lanu
kuti muŵalange, koma iwo sakuliwona.
Anthuwo achite manyazi
poona m'mene mumakondera anthu anu,
ndipo moto umene mwasonkhera adani anu,
uŵapsereze.
12Inu Chauta, mumatipatsa mtendere,
chifukwa choti zonse zimene timakhoza,
mumatichitira ndinu.
13Chauta, Mulungu wathu,
ife ngakhale takhala tikulamulidwa ndi ena,
sitilemekeza dzina lina, koma lanu lokha.
14Ankhanza aja tsopano adafa,
sadzakhalanso ndi moyo,
sadzabweranso kudzativutitsa,
pakuti mwaŵalanga ndi kuŵaonongeratu.
Palibenso amene amaŵakumbukira.
15Koma Inu Chauta, mwachulukitsa mtundu wathu,
mwaukulitsa ndithu. Mwakuza dziko lathu,
mwalandirapo ulemu mbali zake zonse.
16Inu Chauta, pamene anali m'masautso,
anthu anu adakufunafunani,
pamene munkaŵalanga,
adapemphera kwa Inu.
17Inu Chauta, mwatiliritsa
monga momwe amalirira mkazi
pa nthaŵi yobala mwana.
18Ife tidamva ululu,
ndipo tidavutika ngati mkazi pa
nthaŵi yobala mwana,
koma sitidapindule kanthu.
Sitidadzetse chipulumutso m'dziko lapansi pano,
sitidabadwitse anthu atsopano pansi pano.
19Anthu anu amene adafa adzakhalanso ndi moyo,
matupi ao adzauka.
Inu nonse amene muli m'manda,
dzukani ndi kuimba mosangalala.
Monga momwe mame amafeŵetsera pansi
kutsitsimutsa zomera,
momwemonso Chauta adzaukitsa anthu amene adafa kale.
20Abale anga, pitani mukaloŵe m'nyumba zanu,
ndipo mukadzitsekere.
Mubisale pang'ono mpaka mkwiyo wa Chauta utatha.
21Chauta akubwera kuchokera kumene amakhala,
akubwera kudzalanga anthu a dziko lapansi
chifukwa cha machimo ao.
Magazi okhetsedwa pa dziko lapansi adzaululuka,
mitembo ya anthu ophedwa sidzabisikanso.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.