1 Ezek. 21.28-32; 25.1-7; Amo. 1.13-15; Zef. 2.8-11 Za Aamoni, Chauta akufunsa kuti,
“Kodi Israele alibe ana aamuna?
Kodi alibe mloŵachuma?
Chifukwa chiyani tsono anthu opembedza
Milikomu alanda dziko la Gadi,
ndipo akukhala m'mizinda yake?
2Ndipotu nthaŵi ikudza,
pamene ndidzamveketse mfuu wankhondo ku Raba,
likulu la ku Amoni.
Mzinda umenewo udzasanduka bwinja lopanda anthu,
ndipo midzi yake idzapserera.
Tsono Israele adzaŵalanda zao adaniwo
amene adamulanda zake,”
akutero Chauta.
3“Lirani, inu a ku Hesiboni,
pakuti mzinda wa Ai waonongeka.
Lirani chokweza, inu ana aakazi a ku Raba.
Valani ziguduli kuwonetsa chisoni,
mulire, muthaŵire uku ndi uku m'kati mwa machinga.
Ndithu, mulungu wanu Milikomu adzatengedwa ukapolo,
pamodzi ndi ansembe ake ndi akalonga ake.
4Chifukwa chiyani mukunyadira zigwa zanu,
inu anthu osakhulupirika,
amene munkadalira chuma chanu nkumati,
‘Ndani angalimbane ndi ife?’ ”
5Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti,
“Chenjerani,
mudzaona zoopsa kuchokera kwa onse okuzungulirani.
Adzakupirikitsani muli kaŵeraŵera,
popanda wina wokusonkhanitsaninso othaŵanu.
6Komabe pambuyo pake ndidzaŵabwezera ufulu Aamoni,”
akutero Chauta.
Za chilango cha Edomu7 Yes. 34.5-17; 63.1-6; Ezek. 25.12-14; 35.1-15; Amo. 1.11, 12; Oba. 1.1-14; Mal. 1.2-5 Bar. 3.22, 23 Za Edomu, Chauta Wamphamvuzonse akufunsa kuti,
“Kodi nzeru sizikupezekanso ku Tema?
Kodi anzeru uphungu wao udatheratu?
Kodi nzeru zao zija zati zii?
8Anthu a ku Dedani bwererani,
thaŵani mukakhale ku makwaŵa.
Ndithudi ndidzalanga zidzukulu za Esau
pa tsiku lake la chiweruzo.
9Othyola mphesa akadakwera kwa inu,
akadakusiyiraniko mphesa pa nthambi.
Mbala zikadafika usiku,
bwenzi zitangotengako zofunikira zokha.
10Koma ine ndachotseratu chuma chonse
cha zidzukulu za Esau.
Ndaonetsa poyera malo ao obisalamo,
alibenso poti angabisale.
Ana ao, abale ao ndi anansi ao omwe aonongeka.
Palibe wina amene watsalako.
11Siyani ana anu amasiye, ndidzaŵalera ndine.
Akazi anu amasiye akhoza kudalira Ine.”
12Chauta akunena kuti, “Ngati amene sanali oyenera kumwa chikho cha chilango adzamwe ndithu, nanji inu, muyesa mudzakhala osalangidwa? Pepani, mudzalangidwa ndithu, ndipo mudzamwadi chikhocho.
13Pali Ine ndemwe, mzinda wa Bozira udzasanduka chinthu chochititsa nyansi, chomachiseka, chopanda kanthu ndi chotembereredwa. Ndipo midzi yake yonse idzakhala mabwinja mpaka muyaya.”
14Ndamva uthenga wochokera kwa Chauta
wamthenga watumidwa kwa anthu a mitundu ina.
Akufuula kuti,
“Sonkhanani pamodzi kuti mumenyane ndi Edomu,
dzambatukani mukonzekere nkhondo!
15Ndidzakuchepetsa pakati pa mitundu yonse,
anthu onse adzakunyoza.
16Kunyada kwako kwakunyenga,
kuwopseza kwako kwakusokeza,
iwe wokhala m'mapanga ndi m'matanthwe, ku mapiri.
Ngakhale umange chisa chako pamwambamwamba ngati nkhwazi,
ndidzakutsitsabe pamenepo,”
akutero Chauta.
17“Dziko la Edomu lidzasanduka lochititsa nyansi. Onse odutsamo azidzachita nyansi, nkumatsonya chifukwa cha kuwonongeka kwake koopsa.
18Gen. 19.24, 25 Monga momwe udaonongekera mzinda wa Sodomu ndi wa Gomora pamodzi ndi midzi yake yozungulira, momwemonso sikudzakhalako munthu ndi mmodzi yemwe kumeneko. Palibe ndi mmodzi yemwe wodzayendako kumeneko.
19Lun. 12.12Monga momwe mkango wotuluka ku nkhalango za ku Yordani umaopsera khola la nkhosa lotetezedwa bwino, Inenso mwadzidzidzi ndidzapirikitsira Aedomu kutali ndi kwao. Pambuyo pake ndidzaŵaikira woŵalamulira amene ndidzamufune Ine. Nanga ndani angafanefane ndi Ine? Ndani angandipititse kubwalo lamilandu? Ndi mtsogoleri uti amene angalimbike pamaso panga?
20Nchifukwa chake imvani, zimene Ine Chauta ndakonza zolangira Edomu, ndiponso zolinga zake zolangira anthu a ku Temani ndi izi: Ana ao omwe adzatengedwa ndithu, ndipo anthu onse adzada nalo nkhaŵa tsoka lao.
21Dziko lapansi lidzanjenjemera chifukwa cha kugwa kwao. Kulira kwao kudzamveka mpaka ku Nyanja Yofiira.
22Ndithu mtundu wina udzachita kuuluka nkudzagwera Bozira ngati nkhwazi ya mapiko otambalitsa. Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Edomu idzakhala ili thithithi ndi mantha, ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira.”
Za chilango cha Damasiko23 Yes. 17.1-3; Amo. 1.3-5; Zek. 9.1 Za Damasiko Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti,
“Anthu a ku Hamati ndi ku Aripadi asokonezeka,
chifukwa adamva uthenga woipa.
Mtima wao wachita kuti phwi ndi mantha,
ndi osakhazikika ngati nyanja yosatha kukhala bata.
24Damasiko wataya mtima,
akufuna kuthaŵa chifukwa chogwidwa ndi mantha aakulu.
Akumva nkhaŵa ndi zoŵaŵa
zonga za mkazi pa nthaŵi yake yochira.
25Mzinda wotchuka uja wasiyidwa,
mzinda wachikondwerero uja!
26Nchifukwa chake anyamata ake adzagwa m'mabwalo ake,
ndipo ankhondo ake onse adzaonongedwa tsiku limenelo.
27Ndidzatentha malinga a Damasiko,
moto wake udzapsereza nyumba zamphamvu za Benihadadi.”
Za chilango cha Kedara ndi cha Hazori28Kunena za Kedara ndi za maufumu a ku Hazori amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adagonjetsa,
Chauta akunena kuti,
“Nyamukani mukaŵathire nkhondo ku Kedara!
Aonongeni anthu akuvumawo!
29Gwetsani mahema ao ndipo mulande nkhosa zao.
Tengani nsalu ndi katundu wao yense m'mahemamo.
Landaninso ngamira zao.
Anthu adzafuula kwa iwo kuti,
‘Pali zoopsa pa mbali zonsezonse!’
30Inu anthu a ku Hazori, thaŵani,
fulumirani, kabisaleni ku makwaŵa.
Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni,
wakonzekera kuti amenyane nanu,”
akutero Chauta.
31“Nyamukani, kauthireni nkhondo mtundu wa anthuwo
umene uli pa mtendere,
anthu amene akuyesa kuti ali pabwino.
Mzinda wao ndi wopanda zipata kapena mipiringidzo,
udangokhala pawokha.
32Ngamira zao zidzafunkhidwa,
ndipo makola ao a ng'ombe adzalandidwa.
Ndidzaŵabalalitsira ku mphepo zonse zinai
onse ometa tsitsi lao cham'mbali.
Ndidzaŵagwetsera zoopsa kuchokera ku mbali zonse.
33Hazori adzasanduka bwinja,
malo a nkhandwe, mpaka muyaya.
Simudzakhalanso munthu m'menemo,”
akutero Chauta.
Za chilango cha Elamu34Zedekiya, mfumu ya ku Yuda, atangoyamba kumene kulamulira, Chauta adalankhula ndi mneneri Yeremiya za Elamu. Adati,
35“Tamvera, ndidzathyola uta wa Elamu umene ndiye chida chake champhamvu.
36Ndidzafitsa mphepo zinai pa anthu a ku Elamu kuchokera ku mbali zonse za mlengalenga. Ndidzaŵamwazira ku mphepo zinaizo ndipo silidzakhalapo dziko kumene anthuwo sadzafikako.
37A ku Elamuwo ndidzaŵachititsa mantha pamaso pa adani ao ndiponso pamaso pa amene afuna kuwononga moyo wao. Ndidzaŵagwetsera mkwiyo wanga waukali. Ndidzaŵapirikitsa ndi lupanga mpaka kuŵatheratu.
38Tsono ndidzaika mpando wanga waufumu ku Elamu. Kumeneko ndidzaononga mfumu ndi akalonga ake.
39Komabe, patsogolo pake ndidzaŵabwezera ufulu anthu a ku Elamu,” akutero Chauta.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.