1Ndikati ndibwezere anthu anga pabwino,
ndikati ndichiritse Aisraele,
uchimo wao umaonekera poyera.
Ntchito zoipa za anthu a ku Samariyawo sizibisika ai.
Sakhulupirika, amanyenga anthu,
amathyola nyumba ngati mbala,
ndi achifwamba, amalandanso zinthu za anthu poyera.
2Koma saganiza kuti Ine sindiiŵala ntchito zao zoipa.
Zolakwa zao zaŵazinga,
ndipo sizichoka m'maso mwanga.”
Achita chiwembu ku nyumba ya mfumu3Anthu amakopa mfumu ndi makhalidwe ao oipa,
nduna zake amazinyenga ndi mabodza ao.
4Onsewo ndi osakhulupirika,
udani wao ndi wonyeka ngati moto wamuuvuni,
umene mphikabuledi sasonkhezera
kuyambira pamene akukanyanga mtanda wa buledi
mpaka utafufuma.
5Pa tsiku la chikondwerero cha mfumu,
nduna zake zimadakwa,
mfumu nkuloŵa nawo m'gulu la anthu oipanganirana.
6Mitima yao imatentha ngati uvuni ndi upo wao.
Usiku wonse, ukali wao umanyeka,
ndipo m'maŵa umayaka ngati moto.
7Onsewo amakhala juu ngati uvuni,
ndipo amapha olamulira ao.
Imodziimodzi mafumu ao onse agwa,
koma palibe ndi mmodzi yemwe wondiitana.
Israele asakanizikana ndi anthu a mitundu ina8Chauta akuti,
“Aefuremu ali ngati keke yopsa kumodzi,
chifukwa amasakanizikana ndi anthu a mitundu ina.
9Alendowo akuŵatha mphamvu,
iwo osadziŵako.
Akuyamba kumera imvi,
iwo osadziŵako.
10Aisraele kunyada kwao komwe kukuŵatsutsa.
Koma pa zonsezi sakubwerera kwa Chauta Mulungu wao,
sakumfunafuna konse.
11“Aefuremu ali ngati nkhunda yopusa, yopanda nzeru.
Amaitana Aejipito,
namapita ku Asiriya kukapempha chithandizo.
12Kulikonse kumene amapita,
ndidzaŵatchera ukonde.
Ndidzaŵagwetsa pansi ngati mbalame zamumlengalenga.
Ndidzaŵalanga chifukwa cha zolakwa zao.
13“Tsoka kwa iwo pakuti andisiya Ine.
Aonongeke chifukwa chakuti andipandukira.
Ndimafuna kuŵapulumutsa,
koma amangolankhula zabodza za Ine.
14Kulira kwao kwa Ine nkwabodza,
amalira ali gone pa bedi.
Amadzichekacheka ngati akunja
chifukwa chofuna chakudya ndi chakumwa,
komabe amandipandukira.
15Ngakhale ndimaŵalera ndi kuŵalimbitsa,
komabe amandichita zachiwembu.
16Amatembenukira kwa mulungu wachabechabe,
osati kwa Mulungu wopambanazonse.
Ali ngati uta wokhota.
Atsogoleri ao adzaphedwa ndi lupanga
chifukwa chakuti amandilankhulira zachipongwe.
Motero a ku Ejipito adzaŵaseka kwambiri.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.