Mphu. 31 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za mavuto obwera ndi chuma

1Munthu wosagona tulo chifukwa cha chuma

amaonda,

chumacho chimadzetsa nkhaŵa nkuthaŵitsa tulo.

2Kuda nkhaŵa kwamasana kumaletsa tulo,

m'maso mumangoti gwa ngati wadwala koopsa.

3Munthu wolemera amalimbikira pa ntchito,

kuti adziwunjikire chuma,

ndipo akasiya ntchito, amasangalala

nkumadyerera.

4Munthu wosauka amagwira ntchito yoŵaŵa

nangopeza pang'ono zofunikira moyo wake,

ndipo akasiya ntchito, amasaukirasaukira.

5Munthu wokondetsa golide sadzakhala wolungama,

ndipo munthu wakhwinthi ndi ndalama adzasokera nazo.

6Anthu ambiri adatayikiratu chifukwa cha golide,

adakumana ndi chiwonongeko.

7Chuma ndi msampha kwa anthu ochikondetsa,

chimakola opusa onse.

8Ngwodala munthu wolemera amene alibe tchimo,

ndipo sathamangira golide.

9Mutiwonetse munthu wotero ndipo tidzamuyamika,

chifukwa ameneyo adachita zozizwitsa pakati pa

anthu a fuko lake.

10Ndani adayesedwapo pa zimenezi napezeka wangwiro?

Ngati alipo, ayenera kunyadira.

Ndani woti akadatha kuchimwa koma sadachimwe,

kapena kuchita choipa koma sadachite?

11Munthuyo chuma chake chidzakhazikika bwino,

anthu anzake adzamtamanda chifukwa cha ntchito

zake zachifundo.

Za makhalidwe apaphwando

12Ukakhala pa phwando ladzaoneni,

usaonetse maso adyera,

usanene kuti, “Lero kuli madyerero!”

13Kumbukira kuti kuyang'ana ndi diso ladyera nkulakwa.

Palibe chinthu chaumbombo kupambana diso,

nchifukwa chake limangodza misozi kaŵirikaŵiri.

14Usakhale kagwam'masotola,

usamakankha mnzako popisa dzanja m'mbale.

15Uziganizira zofuna za anzako poyang'anira zako zomwe,

pa zonse uziganizira bwino.

16Uzidya mwaulemu zimene akupatsa.

Usamatafuna mwaphokoso, mwinamwina anthu ena

adzadana nawe.

17Potsata ulemu, uziyamba ndiwe kuleka kudya.

Usaonetse dyera pakudya, mwinamwina anthu ena

adzaipidwa nazo.

18Ukamadya pa gulu lalikulu la anthu,

usamayamba ndiwe kudya, ena asanayambe.

19Munthu wamkhalidwe

ngakhale chakudya chochepa chimamukwanira,

ndipo sachita pefupefu akagona pabedi pake.

20Munthu wodya moyenera

amagona tulo tabwino,

ndipo amadzuka msanga,

akupeza bwino.

Kusapeza tulo, kuchita mseru, kugeya ndulu,

zonsezi zimachitika ndi munthu wadyera.

21Ngati akuumiriza kudya kopitirira,

tuluka ukasanze, udzakhala bwino.

22Ndimvere, mwana wanga, usanyozere,

ndipo potsiriza udzavomereza mau anga.

Zochita zako zonse uzichita moyenera,

ndipo matenda sadzakukhudza.

23Munthu wodyetsa anzake bwino, anthu

amamuyamika,

umboni wao pa ufulu wakewo umakhaladi

wokhulupirika.

24Koma mumzinda monse anthu amamdandaula munthu womana,

umboni wao pa kumana kwake umakhala wokhoza zedi.

Za vinyo

25Usayese kuwonetsa kuti ndiwe katundu

pakumwa vinyo,

chifukwa ambiri adaonongeka naye vinyo.

26Monga moto ndi madzi zimayesa kulimba kwa chitsulo,

momwemonso vinyo amayesa mitima ya anthu

odzikuza akamamenyana.

27Vinyo ndiye moyo umene wa anthu,

akamumwatu moyenera.

Kodi popanda vinyo moyo uli nchiyaninso?

Vinyo adalengedwa kuti azisangalatsa anthu.

28Vinyo amapatsa chimwemwe ndi chisangalalo mu mtima,

kumumwatu pa nthaŵi yabwino

ndi mwa muyesonso wabwino.

29Koma kumumwa mobzola muyeso,

amaŵaŵitsa mtima,

amautsa mikangano ndi ndeu.

30Munthu wopusa kuledzera kumamuutsira ukali

wodzipweteketsa nawo,

kumamlanda mphamvu nkumuwonjezera kumenyedwa.

31Pakumwa vinyo pa phwando usadzudzule mnzako,

kapena kumchedzera pamene iye akusangalala.

Usamdzudzule kapena kumvutitsa pomulonjerera ngongole.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help