Miy. 13 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Mwana wanzeru amamvera malangizo a atate ake,

koma wonyoza samvetsera akamamdzudzula.

2Munthu wabwino amapeza nako phindu kulankhula kwake,

koma anthu onyenga amalakalaka zandeu.

3 Mphu. 28.25, 26 Amene amagwira pakamwa pake amasunga moyo wake,

koma amene amangolakatika amaonongeka.

4Munthu waulesi amakhumbira zinthu koma sapeza kanthu,

m'menemo munthu wakhama amalemera.

5Munthu wokonda Mulungu amadana ndi bodza,

koma zochita za munthu woipa zimanyansa

ndipo zimachititsa manyazi.

6Chilungamo chimatchinjiriza munthu wabwino,

koma tchimo limagwetsa munthu woipa.

7Wina amadziyesa wolemera, m'menemo alibe nkanthu komwe.

Wina amadziyesa wosauka, m'menemo ali nchuma chochuluka.

8Chuma cha munthu wolemera

nchimene chimaombola moyo wake,

koma munthu wosauka alibe choti nkumuwombola.

9Kuŵala kwa anthu a Mulungu kumachita kuti ngwee,

koma nyale ya anthu oipa mtima siidzalephera kuzima.

10Chipongwe cha osasamala za anzao chimadzetsa mkangano,

koma omvera malangizo a anzao ndiwo ali ndi nzeru.

11Chuma chochipeza mofulumira

chidzanka chitha pang'onopang'ono,

koma chochipeza pang'onopang'ono

chidzanka chichulukirachulukira.

12Chinthu chochiyembekeza chikalephereka,

chimafooketsa mtima,

koma chinthu chochilakalaka chikachitikadi,

chili ngati mtengo wopatsa moyo.

13Wonyoza malangizo amadziwononga,

koma wosamala lamulo amalandira mphotho.

14Maphunzitso a anthu anzeru ali ngati kasupe wa moyo,

amathandiza anthu kuti asakodwe mu msampha wa imfa.

15Munthu wa nzeru zabwino, anthu amamkomera mtima,

koma munthu wosakhulupirika, kwake nkuwonongeka.

16Munthu wochenjera amachita zonse mwanzeru,

koma wopusa amaonetsa poyera uchitsiru wake.

17Wamthenga woipa amagwetsa anthu m'mavuto,

koma mtumwi wokhulupirika amadzetsa mtendere.

18Umphaŵi ndi manyazi zimagwera wonyozera mwambo,

koma munthu womvera chidzudzulo amalemekezeka.

19Chinthu chochilakalaka chikachitikadi,

chimasangalatsa mtima.

Koma kuleka zoipa

kuli ngati chinthu chonyansa kwa zitsiru.

20 Mphu. 6.33, 34 Woyenda ndi anthu anzeru nayenso amakhala ndi nzeru,

koma woyenda ndi zitsiru adzaonongeka.

21Choipa chitsata mwini,

koma wochita chilungamo amalandira zabwino.

22Munthu wabwino amasiyira zidzukulu zake choloŵa,

koma chuma cha munthu woipa

amachilandira ndi anthu abwino.

23M'tsala la munthu wosauka mumalola chakudya chambiri,

koma anthu opanda chilungamo amalanda chakudyacho.

24Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti samkonda,

koma amene amakonda mwana wake, sazengereza kumlanga.

25Munthu wabwino ali nazo zokwanira zoti adye nkukhuta,

koma m'mimba mwa munthu woipa mumakhala pululu ndi njala.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help