1Mvetsani inu Aisraele. Muli pafupi kuwoloka mtsinje wa Yordani ndi kukakhala m'dziko la anthu aakulu ndi amphamvu kupambana inu. Mizinda yao ndi ya malinga aatali ofika mpaka kumwamba.
2Anthu ake ngotchuka ndiponso ataliatali. Anthu amenewo ndi zidzukulu za Aanaki amene mukuŵadziŵa kale. Paja mudamva kale kuti amati, “Ndani angalimbane ndi zidzukulu za Anaki?”
3Koma lero mudziŵe kuti Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene adzakutsogolerani monga momwe umachitira moto wopsereza. Adzagonjetsa onse pamaso panu, kotero kuti mudzaŵapirikitsa ndi kuŵaononga mwamsanga monga Chauta adakulonjezerani.
4Chauta, Mulungu wanu, ndiye adzakupirikitsirani iwowo. Ndiye inu musadzanene kuti wakuloŵetsani ndi kukupatsani dzikolo chifukwa cha zabwino zimene mwachita. Ai, Chauta akupirikitsirani anthu ameneŵa chifukwa choti iwowo ngoipa.
5Chimene Chauta akukulolerani kuŵalanda dziko anthuwo, si chifukwa chakuti ndinu abwino ndi angwiro ai. Akuŵapirikitsa chifukwa iwowo ngoipa, ndiponso chifukwa choti Mulungu ndi wosunga lonjezo limene adachita ndi makolo anu Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.
6Mudziŵe tsono kuti Chauta sakukupatsani dziko labwinoli popeza kuti ndinu olungama ai. Inu ndinu anthu okanika.
7Musaiŵale m'mene mudakwiyitsira Chauta, Mulungu wanu, m'chipululu muja. Kuyambira tsiku lija mudatuluka ku Ejipito kuja, mpaka tsiku limene mudafika kuno, mwakhala mukuukira Chauta, Mulungu wanu.
8Ngakhale ku phiri la Horebu kuja, mudakwiyitsa Chauta, kukwiya kwake koti akadakuwonongani.
9Eks. 24.18 Ine ndidakwera phiri kukalandira miyala iŵiri imene padalembedwapo chipangano chimene Chauta adachita nanu. Ndidakhala kumeneko masiku makumi anai, usana ndi usiku, ndipo sindidadye kapena kumwa kanthu kalikonse.
10Tsono Chauta adandipatsa miyala iŵiri ija imene Iye yemwe adaalembapo ndi dzanja lake zonse zimene adalankhula ndi inu ali m'moto, pa tsiku lija mudasonkhana kuphiri kuja.
11Zedi, patapita masiku makumi anaiwo, usana ndi usiku, Chauta adandipatsa miyala iŵiri ija, imene adaalembapo chipangano.
12Pamenepo Chauta adandiwuza kuti, “Nyamuka tsika msanga, choka kuphiri kuno, chifukwa anthu ako aja udaŵatsogolera kuchokera ku Ejipitoŵa, adziipitsa kwambiri. Sadakhalire kupatuka pa zimene ndidaŵalamula kuti azichita, ndipo adzipangira fano losungunula.”
13Chauta adandiwuzanso kuti, “Anthuŵa ndikuŵadziŵadi, ndi anthu okanika.
14Usandiletse, ndikufuna kuŵaononga ndi kufafaniziratu dzina lao pansi pa thambo. Koma iwe ndidzakusandutsa mtundu waukulu ndi wamphamvu kupambana iwoŵa.”
15Pomwepo ndidatsika phiri, nditanyamula m'manja mwanga miyala iŵiri ija ya chipangano. M'phirimo munkatuluka malaŵi a moto.
16Nditayang'ana, ndidaona kuti inu mudachimwira Chauta, Mulungu wanu, pakudzipangira fano lachitsulo la mwanawang'ombe. Simudakhalire kuleka kusunga malamulo amene Chauta adakulamulani.
17Pompo ine ndidaponya pansi miyalayo ndi kuiswa, inu mukuwona.
18Tsono masiku enanso makumi anai, usana ndi usiku, ndidagwada pamaso pa Chauta ndipo ndidapemphera. Sindidadye kapena kumwa kanthu kalikonse, chifukwa inuyo mudaachimwira Chauta ndikumkwiyitsa.
19Ahe. 12.21 Ine ndinkaopa mkwiyo wa Chauta woopsawo, chifukwa kukwiya kwake kunali koti akadakuwonongani. Koma nthaŵi imeneyo Chauta adamvanso pemphero langa.
20Chauta adakwiyiranso Aroni, kotero kuti akadamupha ndithu, koma ndidampemphereranso nthaŵi yomweyo.
21Chinthu chimene mudachipangacho, fano lachitsulo la mwanawang'ombelo, ndidaliponya pa moto. Tsono ndidaliphwanya pafupipafupi ndi kuliperapera, ndipo ndidataya phulusa lake ku mtsinje wotsika m'phiri uja.
22 Num. 11.3; Eks. 17.7; Num. 11.34 Inu mudakwiyitsanso Chauta, Mulungu wanu, pamene munali ku Tabera, ku Masa ndi ku Kibroti-Hatava.
23Num. 13.17; Deut. 1.21; Num. 13.31; Deut. 1.26; Ahe. 3.16 Ndipo Chauta atakutumani kuchokera ku Kadesi-Baranea kuti mupite kukalandira dziko limene adakupatsanilo, inu mudakana malamulo a Chauta, Mulungu wanu, ndipo simudamkhulupirire kapena kumumvera.
24Mwakhala mukumuukira Chauta kuyambira pamene ine ndidakudziŵani.
25Motero ndidagwada pamaso pa Chauta ndipo ndidapemphera masiku makumi anai, usana ndi usiku, chifukwa Chauta adaatsimikiza zokuwonongani.
26Ndidapemphera motere, ndidati, “Inu Chauta, Ambuye athu, chonde musaŵaononge anthuŵa amene mudaŵasankha kuti akhale anuanu. Anthu ameneŵa mudaŵapulumutsa ndi ukulu wanu ndipo mudaŵatulutsa ku Ejipito ndi mphamvu zanu zazikulu.
27Kumbukirani atumiki anu aja, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, ndipo musasamale kukanika kwa anthu anuŵa, kuipa kwao ndi kuchimwa kwao,
28kuti Aejipito aja angamadzanene kuti Inu simudathe konse kuŵaloŵetsa anthu anu m'dziko limene mudaŵalonjeza. Azidzanenanso kuti: Adaŵatulutsa anthuwo kuti akaŵaphe ku chipululu poti adadana nawo.
29Chonsecho anthu ameneŵa mudaŵasankha kuti akhale anuanu, ndipo mudaŵatulutsa ku Ejipito ndi mphamvu zanu zazikulu ndi mkono wanu wotambalitsa.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.