2 Mbi. 19 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mneneri Yehu adzudzula Yehosafati

1Yehosafati mfumu ya ku Yuda adabwerera kunyumba kwake ku Yerusalemu mwamtendere.

2Koma mneneri Yehu, mwana wa Hanani, adatuluka kuti akumane naye, ndipo adafunsa mfumu Yehosafati kuti, “Kodi ndi bwino kuŵathandiza anthu oipa amene amadana ndi Chauta? Chifukwa cha zimenezi mkwiyo wa Chauta ulikudza kwa inu.

3Komabe pali zina zabwino zimene mudachita, pakuti mudaononga mafano a m'dziko muno, ndipo mwakhala mukulimbikira ndi mtima wonse kufunafuna Mulungu.”

Yehosafati akonza chipembedzo

4Yehosafati ankakhala ku Yerusalemu. Adayendera anthu kuchokera ku Beereseba mpaka ku dziko lamapiri la ku Efuremu, naŵabweza kwa Chauta, Mulungu wa makolo ao.

5Adaika anthu oweruza m'dzikomo, mu mzinda uliwonse wamalinga wa ku Yuda.

6Tsono adauza aweruziwo kuti, “Muganize bwino zimene mukuchita, pakuti simukuweruza m'dzina la munthu ai, koma m'dzina la Chauta. Chautayo ali nanu pamene mukuweruza.

7Tsono khalani anthu oopa Chauta. Muzisamala zimene mukuchita, pakuti Chauta, Mulungu wathu, sapotoza chiweruzo, kapena kukondera, kapenanso kulandira ziphuphu.”

8Ku Yerusalemuko Yehosafati adaika Alevi ena ndi ansembe ndiponso akulu a mabanja a Aisraele, kuti aziweruza m'dzina la Chauta ndi kugamula milandu ya anthu. Iwoŵa ankakhala ku Yerusalemu.

9Adaŵalamula kuti, “Muzichita ntchito imeneyi moopa Chauta, mokhulupirika, ndiponso ndi mtima wonse.

10Pakakhala mlandu wokhudza abale anu amene akukhala m'mizinda yao, monga mlandu wokhetsa magazi, kapena mlandu wa kusamvera malamulo kapena malangizo kapena zogamula zina, muziŵaphunzitsa nthaŵi zonse kuti asamachimwe pamaso pa Chauta. Motero mkwiyo wa Chauta sudzakugwerani inuyo ndi abale anu. Muzichita choncho, ndipo simudzachimwa konse.

11Tsono Amariya, mkulu wa ansembe, ndiye adzakhale wokutsogolerani pa zonse zokhudza Chauta. Zebadiya mwana wa Ismaele, kazembe wa fuko la Yuda, ndiye aziyang'anira zonse zokhudza mfumu. Ndipo Alevi adzakutumikirani ngati akapitao. Muzichita zimenezi molimba mtima, Chauta akhale naye amene ali wolungama.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help