1Yesu, ali wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, adabwerako ku mtsinje wa Yordani kuja. Mzimu Woyerayo ankamutsogolera m'chipululu
2masiku makumi anai, ndipo kumeneko Satana ankamuyesa. Yesu sankadya kanthu masiku amenewo, ndipo pamene masikuwo adatha, adamva njala.
3Tsono Satana adamuuza kuti, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, lamulani mwala uli apawu kuti usanduke chakudya.”
4 wa nyumba yamapemphero, nakhala pansi. Anthu onse amene adaasonkhana m'nyumbamo ankangomupenyetsetsa.
21Tsono Yesu adaŵauza kuti, “Lero zachitikadi zimene adaaneneratu Malembo amene mwamvaŵa.”
22Anthu onse adamtamanda, nkumadabwa ndi mau ogwira mtima amene Iye ankalankhula. Anthuwo ankati, “Kodi uyu si mwana uja wa Yosefeyu?”
23Apo Yesu adaŵauza kuti, “Ndithudi mudzandiwuza mwambi uja wakuti, ‘Iwe sing'anga, dzichiritse wekha.’ Mudzatinso, ‘Tidamva zimene mudachita ku Kapernao, tsono muchitenso zomwezo kwanu kuno.’ ”
24Yoh. 4.44Adaŵauzanso kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti palibe mneneri amene amalandiridwa bwino kumudzi kwao.
251Maf. 17.1 Kunena zoona, paja panali azimai amasiye ambiri pakati pa Aisraele pa nthaŵi ya mneneri Eliya, pamene mvula siidagwe zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, kotero kuti munali njala yaikulu m'dziko lonse.
261Maf. 17.8-16Eliya sadatumidwe ndi kwa mmodzi yemwetu mwa iwo aja, koma adatumidwa kwa mai wamasiye wa ku mudzi wa Sarepta, m'dziko la Sidoni.
272Maf. 5.1-14 Panalinso akhate ambiri pakati pa Aisraele nthaŵi ya mneneri Elisa, komabe panalibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo aja amene adachiritsidwa. Amene adachiritsidwa ndi Namani yekha wa ku dziko la Siriya.”
28Anthu onse amene anali m'nyumba yamapemphero muja atamva mau ameneŵa, adapsa mtima kwambiri.
29Adaimirira namtulutsira kunja kwa mudzi, nkupita naye pamwamba pa phiri pamene adaamangapo mudzi wao. Adaati akamponye kunsi,
30koma Iye adangodzadutsa pakati pao, nkumapita.
Yesu achiritsa munthu wogwidwa ndi mzimu woipa(Mk. 1.21-28)31Yesu adapita ku Kapernao, mudzi wina wa ku Galileya, nkumaphunzitsa pa tsiku la Sabata.
32Mt. 7.28, 29Zophunzitsa zake anthu zidaaŵagwira mtima kwambiri, chifukwa ankalankhula moonetsa ulamuliro ngati mwiniwake.
33M'nyumba yamapempheroyo munali munthu wogwidwa ndi mzimu womuipitsa. Adalankhula mokuwa kuti,
34“Aah, kodi takuputani chiyani, Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadzatiwononga? Ndakudziŵani, ndinu Woyera uja wa Mulungu.”
35Koma Yesu adazazira mzimu woipawo, adati, “Khala chete, tuluka mwa munthuyu.” Apo mzimu womuipitsa uja udamugwetsa pansi munthuyo pakati pa anthu, nkutuluka, osamupweteka konse.
36Anthu onse aja adazizwa, mpaka kumafunsana kuti, “Mau ameneŵa ngotani? Ngakhale mizimu yoipitsa anthu yomwe akuilamula ndi mphamvu ndi ulamuliro, ndipo ikutulukadi.”
37Motero mbiri ya Yesu idawanda ku dera lonselo.
Yesu achiritsa anthu ambiri(Mt. 8.14-17; Mk. 1.29-34)38Yesu adanyamuka nachoka ku nyumba yamapemphero kuja, nakaloŵa m'nyumba ya Simoni. Apongozi a Simoni ankadwala malungo aakulu, ndipo anthu adapempha Yesu kuti achitepo kanthu.
39Yesu adaŵeramira pa iye, nazazira malungowo, ndipo malungo aja adatha. Pomwepo amai aja adadzuka nayamba kukonzera anthu chakudya.
40Dzuŵa likuloŵa, anthu onse amene anali ndi anzao odwala nthenda zosiyanasiyana, adabwera nawo kwa Yesu. Iye adasanjika manja pa wodwala aliyense, naŵachiritsa onse.
41Nayonso mizimu yoipa inkatuluka mwa anthu ambiri ikufuula nkumanena kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.” Koma Iye adaidzudzula, osailola kuti ilankhule, chifukwa idaadziŵa kuti analidi Mpulumutsi wolonjezedwa uja.
Yesu apita kukalalika ku Yudeya(Mk. 1.35-39)42Kutacha, Yesu adachoka ku Kapernao kuja napita ku malo kosapitapita anthu. Makamu a anthu adayamba kumufunafuna, ndipo atampeza, adayesa kumletsa kuti asaŵasiye.
43Koma Iye adaŵauza kuti, “Ndiyenera kukalalika Uthenga Wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu ku midzi inanso, pakuti ndizo zimene Mulungu adanditumira.”
44Motero Iye ankalalika m'nyumba zamapemphero za ku Yudeya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.