1Mundichitire chifundo, Inu Mulungu,
malinga ndi chikondi chanu chosasinthika.
Mufafanize machimo anga,
malinga ndi chifundo chanu chachikulu.
2Mundisambitse kwathunthu
pochotsa kulakwa kwanga,
mundiyeretse mtima
pochotsa machimo anga.
3Zolakwa zanga ndikuzidziŵa,
kuchimwa kwanga ndikukuzindikira nthaŵi zonse.
4 Aro. 3.4 Ndachimwira Inu, Inu nokha,
ndachita choipa pamaso panu.
Motero mwakhoza ponditchula wolakwa,
simudalakwe pogamula mlandu wanga.
5Zoonadi, ndidabadwa mu uchimo,
ndinali mu uchimo kuyambira pamene mai wanga
adatenga pathupi pa ine.
6Ndithudi, Inu mumakonda mtima woona,
choncho mundiphunzitse nzeru zanu.
7Mundiyeretse ndi hisope
ndipo ndidzakhala woyera.
Mundisambitse,
ndipo ndidzayera kupambana chisanu chambee.
8Mundilole ndimve chimwemwe ndi chikondwerero.
Ngakhale mwandiphwanyaphwanya mafupa,
mundilole ndidzasangalalenso.
9Mufulatire machimo anga,
mufafanize zoipa zanga zonse.
10Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu,
muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika.
11Musandipirikitse pamaso panu,
musachotse Mzimu wanu woyera mwa ine.
12Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu,
mulimbitse mwa ine mtima womvera.
13Pamenepo ochimwa ndidzaŵaphunzitsa njira zanu,
ndipo iwo adzabwerera kwa Inu.
14Mundikhululukire mlandu wanga wokhetsa magazi,
Inu Mulungu, Mulungu Mpulumutsi wanga,
ndipo ndidzakweza mau poimba za chipulumutso chanu.
15Ambuye, tsekulani milomo yanga,
ndipo pakamwa panga padzalankhula zotamanda Inu.
16Si nsembe wamba imene Inu imakusangalatsani.
Ndikadapereka nsembe yopsereza,
sibwenzi Inu mutakondwera nayo.
17Nsembe imene Inu Mulungu mumailandira,
ndi mtima wotswanyika.
Mtima wachisoni ndi wolapa,
Inu Mulungu simudzaunyoza.
18Muŵachitire zabwino anthu a ku Ziyoni,
chifukwa cha kukoma mtima kwanu.
Mumangenso kachiŵiri makoma a Yerusalemu.
19Pamenepo mudzakondwera ndi nsembe zoyenera,
nsembe zootcha ndi zopsereza kwathunthu.
Choncho adzapereka ng'ombe zamphongo
pa guwa lanu lansembe.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.