Zek. 13 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kuyeretsedwa kwa Yerusalemu

1Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Tsiku limenelo banja la Davide adzalikonzera kasupe wa madzi, kuti iwo pamodzi ndi anthu a ku Yerusalemu aŵachotsere machimo ao ndi zoipa zao.

2“Tsiku limenelo ndidzafafaniziratu ndi maina omwe a mafano m'dziko, kotero kuti sadzaŵakumbukiranso. Ndidzachotsanso m'dziko aneneri pamodzi ndi mzimu wonyansa Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.

3Wina aliyense akadzafunabe kuti azilosa, bambo wake ndi mai wake adzamuuza kuti, ‘Sudzakhalanso ndi moyo chifukwa choti ukulosa zabodza m'dzina la Chauta.’ Motero makolo ake omwe adzambaya pamene munthuyo akulosa.

4“Tsiku limenelo mneneri aliyense adzachita manyazi chifukwa cha zinthu zimene akuti amaziwona m'masomphenya pamene akulosa. Sadzavalanso mwinjiro wake waubweya woti azinamizira anthu.

5Koma adzati, ‘Sindine mneneri ai. Ndine mlimi, poti ndakhala ndikulima munda kuyambira ubwana wanga.’

6Ndipo wina akadzafunsa kuti, ‘Nanga zilonda zili kumsana kwakozi, udatani?’ Iye adzati, ‘Zilondazi ndidazilandira m'nyumba mwa abwenzi anga.’ ”

7 Mt. 26.31; Mk. 14.27 Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti,

“Lupanga iwe, dzambatuka, ukanthe mbusa wanga.

Ukanthe munthu amene ali pafupi ndi Ine.

Ndikutero Chauta Wamphamvuzonse.

Kantha mbusa kuti nkhosa zimwazikane.

Pamenepo ndidzakantha ndi anthu wamba omwe.”

8Chauta Wamphamvuzonse akuti,

“Mwa zigawo zitatu za anthu m'dziko monsemo

ziŵiri zidzaphedwa,

chidzangokhalako chigawo chimodzi chokha chamoyo.

9Anthu a m'chigawo chachitatuchi ndidzaŵaika pa moto,

ndidzaŵayeretsa monga m'mene amayeretsera siliva.

Ndidzaŵayesa monga m'mene amayesera golide.

Tsono adzatama dzina langa mopemba,

Ine mwiniwake nkuŵayankha.

Ndidzanena kuti, ‘Ameneŵa ndi anthu anga.’

Iwowo adzati, ‘Chauta ndi Mulungu wathu.’ ”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help