1Chauta akuuza anthu ake kuti,
“Muzichita zabwino ndi zolungama,
chifukwa ndikuwombolani posachedwa,
chipulumutso changa chiwoneka.”
2Ndi wodala munthu amene amachita zimenezi,
munthu amene amalimbikira kuzichita,
amene amalemekeza tsiku la Sabata, osaliwononga,
ndipo amadziletsa kuchita zoipa.
3Mkunja amene waphatikana ndi Chauta,
asanene kuti,
“Mosapeneka konse Chauta
adzandichotsa pakati pa anthu ake.”
Nayenso wofulidwa asanene kuti,
“Ine ndiye ndine wouma ngati chikuni.”
4 Lun. 3.14, 15 Paja Chauta akuti,
“Ofulidwa amene amalemekeza masiku a Sabata,
amene amachita zokomera Ine,
ndi kusunga chipangano changa mokhulupirika,
5Ineyo ndidzaŵapatsa dzina ndi mbiri yabwino
pakati pa anthu anga,
m'kati mwa fuko langa,
koposa kukhala ndi ana aamuna ndi aakazi.
Ndidzaŵapatsa mbiri yabwino yosatha, yosaiŵalika.”
6Chauta akutinso,
“Akunja amene amaphatikana ndi Chauta
mpaka kumgwirira ntchito, kumkonda, ndi kumtumikira,
amenenso amalemekeza tsiku la Sabata, osaliwononga,
nasunga bwino chipangano changa,
7 Mt. 21.13; Mk. 11.17; Lk. 19.46 Ine ndidzaŵafikitsa ku Ziyoni, phiri langa lopatulika.
Ndidzaŵapatsa chimwemwe m'nyumba yanga yopemphereramo.
Zopereka zao zootcha ndiponso nsembe zao zinanso
ndidzazilandira pa guwa langa.
Paja Nyumba yanga idzatchedwa
nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonse.”
8Chauta, amene amasonkhanitsa Aisraele onse obalalika,
akunena kuti, “Ndidzasonkhanitsanso anthu ena
kuwonjezera pa amene adasonkhana kale.”
Atsogoleri a ku Israele adzudzulidwa9Chauta akuuza anthu a mitundu ina kuti,
“Inu nonse zilombo zakuthengo,
nonse zilombo zam'nkhalango, bwerani mudzadye.
10Atsogoleri onse a Israele ndi akhungu,
onsewo ndi opanda nzeru konse.
Ali ngati agalu opanda mau, osatha kuuwa.
Ntchito nkulota, kugona pansi, kukondetsa tulo.
11Ali ngati agalu a njala yaikulu, amene sakhuta konse.
Abusa nawonso ndi opanda nzeru.
Aliyense amachita monga m'mene afunira,
ndipo amangofuna zokomera iye yekha.
12Zidakwa zimenezi zimati,
‘Tiyeni timwe vinyo,
tiyeni timwe zakumwa zamphamvu mpaka kukhuta.
Maŵa lidzakhala ngati leroli,
mwina mwake nkudzaposa lero limene.’ ”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.