1Tsono ndidamva chisoni mumtima mwanga, ndipo ndidalira ndi kupemphera modandaula kuti,
2“Ambuye ndinu olungama,
ndipo ntchito zanu zonse nzolungama.
Njira zanu zonse nzachifundo ndiponso nzoona.
Ndinu amene mumaweruza anthu onse a m'dziko lapansi.
3“Nchifukwa chake Inu Ambuye,
mundikumbukire ndipo mundiyang'ane.
Musandilange chifukwa cha machimo anga,
kapena chifukwa cha zolakwa zanga zina
zosadziŵa mwiniwakene,
kapenanso chifukwa cha machimo a makolo anga.
4“Paja tidakuchimwirani,
tidaphwanya malamulo anu.
Tsono Inu mudatipereka kwa otifunkha,
ku ukapolo ndi ku imfa.
Tsopano tasanduka chinthu chochiseka, chochinyodola
ndi chonyozeka pakati pa mitundu yonse ya anthu
kumene mudatimwazira.
5“Tsopano ndikuvomera kuweruza kwanu koona,
kwakuti mundilange chifukwa cha machimo anga
ndi machimo a makolo anga,
popeza kuti sitidamvere malamulo anu,
sitidakhale okhulupirika pamaso panu.
6“Tsono muchite nane monga mufunira,
mundilande moyo wanga,
ndilisiye dziko lino lapansi,
kuti ndibwerere ku dothi.
Zoonadi, ndiye bwino kuti ndife
koposa kukhala moyo,
chifukwa ndamva zambiri zondilalatira mosayenera,
ndipo ndili ndi chisoni chachikulu.
“Ambuye, mundipulumutse ku mavuto anga,
ndi kundifikitsa ku dziko langa lamuyaya.
Ambuye, chonde musandifulatire.
Ndi bwino koposa kuti ine ndife,
kupambana kuti ndikhale moyo m'mavuto otereŵa,
ndi kumamva zondinyoza zonsezi.”
Mavuto a Sara7Tsiku lomwelo Sara, mwana wa Raguele, wa ku Ekibatana ku Mediya, nayenso adamva mau omnyoza, kuchokera pakamwa pa mmodzi mwa adzakazi a atate ake.
8Ndiye kuti Sarayo adaakwatiwapo ndi amuna asanu ndi aŵiri. Tsono Asimodeo, demoni woipitsitsa, adaŵapha amuna onsewo, asanakhale naye malo amodzi mkaziyo. Mdzakaziyo adauza Sara kuti, “Ndithu, umaŵapha wekha amuna akoŵa! Taona, udakwatiwapo ndi amuna asanu ndi aŵiri, koma palibe ndi mmodzi yemwe amene udapeza naye mwai.
9Ukutilangiranji ife chifukwa choti amuna ako adafa? Alondole azimuna akowo. Ndithu asadzaoneke mwana wamwamuna kapena wamkazi wobadwa mwa iwe!”
10Tsiku limenelo Sara adamva chisoni kwambiri mumtima mwake ndipo adalira misozi. Adakwera ku chipinda cham'mwamba cha m'nyumba ya atate ake, kuti akadzikhweze. Koma ataganiza mofatsa, adati, “Ai, ndaleka! Anthu angamadzanyoze bambo wanga nkumanena kuti, ‘Akulu inu, munali ndi mwana mmodzi yekha, amene anali wapamtima, koma adadzipha chifukwa cha mavuto ake.’ Tsono atateŵa, ndi ukalamba waowu, chisoni chotere adzangofa nacho. Basi sindidzipha. Koma makamaka ndipempha Ambuye kuti Iwowo andilole ndife, osati ndikhalenso moyo ndi kumamvabe zondinyozazi.”
Pemphero la Sara11Atatero, Sara adaimirira pafupi ndi windo natambalitsa manja ake, nkuyamba kupemphera ndi mau akuti,
“Inu Mulungu wachifundo, mulemekezedwe!
Dzina lanu litamandike mpaka muyaya.
Ntchito zanunso zikuyamikeni masiku onse.
12“Tsopano ndikukweza maso anga
ndi kuyang'ana kwa Inu.
13Mundichotse m'dziko lino lapansi,
kuti ndisamvenso mau ondinyoza.
14“Inu Ambuye, mukudziŵa
kuti sindidachimwepo ndi mwamuna aliyense.
15Sindidanyoze dzina lanu
kapena dzina la bambo wanga
m'dziko la ukapolo lino.
“Ndine mwana mmodzi yekha wa bambo wanga,
palibe mwana wina woti angamusiyire chuma chake.
Atate alibe mbale,
alibenso msuweni woti nkundikwatira.
“Ndidataya amuna anga asanu ndi aŵiri,
choti ndikhalirenso moyo nchiyani?
Koma ngati simufuna kuti ndife,
mundichitire chifundo,
musalole kuti ndimvenso zondinyozazi.”
Mulungu amvera pemphero la Tobiti ndi la Sara16Pamene Tobiti ndi Sara ankapemphera choncho, mapemphero aowo adamveka pamaso pa Mulungu mu ulemerero wake.
17Num. 36.6-9; Tob. 6.10-12Tsono Mulungu adatuma Rafaele kuti akaŵachiritse anthu aŵiriwo: akamuchotse khungu Tobiti m'maso mwake, kuti azipenya kuŵala kwa Mulungu ndi maso ake; akathandizenso Sara mwana wa Raguele kukwatiwa ndi Tobiyasi mwana wa Tobiti, ndi kumpulumutsa kwa Asimodeo, demoni woipitsitsa uja. Amene adaayenera kumkwatira, anali Tobiyasi yekhayo. Nthaŵi imene Tobiti adachoka ku bwalo lake, nabwerera ku nyumba kwake, nthaŵi yomweyonso nkuti Sara, mwana wa Raguele, akutsika kuchokera ku chipinda cham'mwamba chija.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.