1Chauta adauza Mose kuti,
2“Uza Aroni pamodzi ndi ana ake aamuna kuti azilemekeza zinthu zopatulika zimene Aisraele amapereka kwa Ine, kuti angaipitse dzina langa loyera. Ine ndine Chauta.
3Munthu wina aliyense mwa zidzukulu zake pa mibadwo yonse, akayandikira zopatulika zimene Aisraele adazipereka kwa Chauta, pamene iyeyo ali woipitsidwa, asaonekenso pamaso panga. Ine ndine Chauta.
4Munthu aliyense mwa zidzukulu za Aroni amene ali ndi khate kapena amene amatulutsa zoipa m'thupi mwake, asadyeko zinthu zopatulika mpaka atayeretsedwa. Mwina wansembe angathe kukhudza chinthu choipitsidwa chifukwa chokhudzana ndi chinthu chakufa, kapena angathe kutaya mbeu yake yaumuna.
5Mwina angathe kukhudza kachilombo kokwaŵa, kamene kangathe kumuipitsa, kapena kukhudza munthu amene angathe kumuipitsa mwa mtundu uliwonse.
6Wansembe aliyense wokhudza chinthu chotere, akhala woipitsidwa mpaka madzulo, ndipo asadyeko zinthu zopatulika mpaka atasamba thupi lonse.
7Adzakhala woyeretsedwa dzuŵa litaloŵa, ndipo pambuyo pake adzatha kudyako zinthu zopatulikazo, poti zimenezo ndi chakudya chake.
8Asadye chinthu chofa chokha kapena chojiwa ndi chilombo, ndi kumadziipitsa nazo zimenezo. Ine ndine Chauta.
9Nchifukwa chake ansembe asunge malamulo anga kuti angachimwe ndipo angafe chifukwa choŵaphwanya. Ine ndine Chauta, amene ndimaŵayeretsa.
10“Wapadera asadyeko zinthu zopatulika. Mlendo wongokhala nao kwa wansembe, kapena wantchito wake, asadyeko chinthu chopatulika.
11Koma wansembe akagula kapolo ndi ndalama kuti akhale wake, kapoloyo angathe kudya nao zinthuzo. Ndipo onse amene abadwa m'nyumba mwa wansembe angathe kudyako chakudya chake.
12Mwana wamkazi wa wansembe akakwatiwa ndi wapadera, asadyeko zopereka zopatulikazo.
13Koma mwana wamkazi wa wansembeyo akakhala wamasiye kapena wosudzulidwa, ndipo alibe mwana, nabwerera ku nyumba ya bambo wake monga pa nthaŵi ya utsikana wake, angathe kudyako chakudya cha bambo wake. Koma wapadera asadyeko.
14Munthu wapadera akadyako chinthu chopatulika mosadziŵa, alipire wansembe chifukwa cha chinthucho, ndipo aonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengo wake.
15Ansembe asaipitse nsembe zopatulika za Aisraele zimene amazipereka kwa Chauta.
16Asachimwitse ndi kupalamulitsa Aisraelewo pakuŵalola kudya zakudya zao zopatulika. Inetu ndine Chauta, amene ndimazipatula.”
17Chauta adauza Mose kuti,
18“Uza Aroni, ana ake ndi Aisraele onse kuti, mwina munthu wa m'banja la Aisraele, kapena mlendo wokhala m'dziko la Israele, adzabwera ndi chopereka chake kuti aperekere chimene wachilumbirira. Mwina adzabwera ndi chopereka kuti chikhale nsembe yaufulu yopereka kwa Chauta ngati nsembe yopsereza.
19Kuti nsembeyo ilandiridwe, apereke nyama yopanda chilema kaya ndi ng'ombe yamphongo, kapena nkhosa yamphongo kapenanso tonde.
20Deut. 17.1 Musapereke nyama iliyonse yachilema, chifukwa Chauta sadzakulandirani.
21Mwina munthu wina adzapereka nsembe yachiyanjano kwa Chauta, kuti achitedi zimene adalumbirira, kapena kuti ikhale nsembe yaufulu. Ngati ndi ng'ombe kapena nkhosa, kuti Chauta ailandire, iyenera kukhala yopanda chilema.
22Musapereka kwa Chauta nyama zakhungu kapena zopunduka, kapena zoduka chiwalo, kapena zotulutsa mafinya m'thupi, kapena za nthenda zonyerenyesa, kapena zamphere. Nyama zotere asazipereke kwa Chauta, zisakhale nsembe zopsereza pa guwa la Chauta.
23Mungathe kupereka ng'ombe yamphongo kapena nkhosa imene ili ndi chiwalo chachitali kapena chachifupi, kuti ikhale nsembe yaufulu, koma ikakhala nsembe yolumbirira, singathe kulandiridwa.
24Nyama iliyonse imene mavalo ake ali onyuka kapena otswanyika, kapena ong'ambika kapena oduka, musaipereke ngati nsembe kwa Chauta m'dziko mwanu.
25Ndipo musapereke nyama iliyonse ya mtundu umenewo imene mwailandira kwa mlendo, kuti ikhale nsembe ya chakudya chopereka kwa Chauta. Zimenezi sadzazilandira chifukwa zili ndi chilema ndipo nzopunduka.”
26Chauta adauza Mose kuti,
27“Ng'ombe, nkhosa kapena mbuzi ikabadwa, ikhale ndi make masiku asanu ndi aŵiri. Ndipo kuyambira pa tsiku lachisanu ndi chitatu mpaka m'tsogolo mwake, ingathe kulandiridwa kuti ikhale nsembe yopsereza, yopereka kwa Chauta.
28Make akakhala ng'ombe kapena nkhosa, musaphe makeyo pamodzi ndi mwana wake tsiku limodzi.
29Pamene mupereka nsembe yothokoza Chauta, muipereke mwa njira yoti ilandiridwe.
30Muidye pa tsiku lomwelo, ndipo musaisiyeko mpaka m'maŵa. Ine ndine Chauta.
31“Tsono muzimvera malamulo anga ndi kuŵatsata. Ine ndine Chauta.
32Musanyoze dzina langa loyera, koma likhale lolemekezeka pakati pa Aisraele. Ine ndine Chauta, amene ndimakuyeretsani,
33ndipo ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito, kuti ndikhale Mulungu wanu. Ine ndine Chauta.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.