Nyi. 7 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mwamuna

1Iwe namwali wachifumu,

mapazi ako ngokongola m'nsapato wavalazo.

Ntchafu zako nzoulungika bwino

ngati miyala yamtengowapatali,

yosemedwa ndi mmisiri waluso.

2Mchombo wako uli ngati chikho choulungika,

chimene nthaŵi zonse nchodzaza ndi vinyo wabwino.

Pamimba pako mponing'a

ngati mtolo wa tirigu wozingidwa ndi akakombo.

3Maŵere ako akuwoneka ngati mbaŵala ziŵiri,

ngati mphoyo zamapasa.

4Khosi lako lili see

ngati nsanja ya mnyanga wanjovu.

Maso ako ali ngati maiŵe a ku Hesiboni,

amene ali pafupi ndi chipata cha ku Batirabimu.

Mphuno yako ikuwoneka ngati nsanja ya ku Lebanoni,

yoyang'ana ku Damasiko.

5Mutu wako uli bwinobwino neng'a,

ngati phiri la Karimele,

ndipo tsitsi lako lalitali lili chezichezi.

Kukongola kwake kumatha kudolola ndi mfumu yomwe.

6Ndiwe wokongola zedi, ndiponso wosangalatsa,

iwe wokondedwawe, namwali wokondweretsawe.

7Msinkhu wako uli ngati mtengo wa mgwalangwa,

maŵere ako ali ngati masango a zipatso zake.

8Ndidati, ndikwera mu mtengo wa mgwalangwawu,

ndikathyole zipatso zake.

Maŵere ako akhale ngati masango a mphesa,

fungo la mpweya wako likhale lonunkhira bwino

ngati la maapulosi.

9Ukamandimpsompsona, ine kukhosi see,

ngati ndikumwa vinyo wokoma kwambiri.

Mkazi

Tsono vinyo ameneyu amthirire wokondedwa wanga,

ayenderere pa milomo yake ndi m'mano mwake.

10Wokondedwayo ine ndine wake,

chilakolako chake chonse chili pa ine.

11Bwera, wokondedwa wanga,

tiye tiloŵe m'minda,

tikagone ku midzi.

12Tiye tilaŵirire m'mamaŵa

kupita ku minda yamphesa,

tikaone ngati mipesa idaphuka,

ngati nkhunje zake zidachita maluŵa,

ndiponso ngati makangaza adachita maluŵa.

Kumeneko ndidzakuwonetsa chikondi changa.

13Mitengo ya mankhwala a chisulo

imapereka fungo labwino,

pakhomo pathu pali zipatso zokoma zonse,

zimene ndakusungira, iwe wokondedwa wanga.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help