1 Miy. 22.1 Mbiri yabwino ndi yopambana mafuta
onunkhira bwino amtengowapatali.
Tsiku lomwalira ndi lopambana tsiku lobadwa.
2Kuli bwino kupita ku nyumba yamaliro
kupambana kupita ku nyumba yamadyerero.
Pakuti imfa ndiye mathero ake a anthu onse,
tsono amoyo azisinkhasinkha bwino zimenezi.
3Chisoni nchabwino kupambana chimwemwe,
chifukwa ngakhale nkhope ikhale yakugwa,
mtima umathabe kutolapo nzeru.
4Mtima wa munthu wanzeru
umalingalira kaŵirikaŵiri za imfa.
Koma mtima wa munthu wopusa
umalingalira za chimwemwe.
5Kuli bwino kuti munthu azimva kudzudzula
kwa anthu anzeru,
kupambana kumvera nyimbo zotamanda za zitsiru.
6Kuseka kwa zitsiru
kuli ngati kuthetheka kwa moto kunsi kwa mbiya.
Zimenezinso nzachabechabe.
7Ndithudi kuzunza ena
kumamsandutsa munthu wanzeru kuti akhale wopusa,
ndipo kulandira chiphuphu kumaononga mtima.
8Mathero ake a chinthu
ndi abwino kupambana chiyambi chake.
Mtima wopirira ndi wopambana mtima wodzikuza.
9 Yak. 1.19 Usamafulumira kukwiya,
pakuti mkwiyo umakhalira zitsiru.
10Usamafunsa kuti,
“Chifukwa chiyani masiku amakedzana
anali abwino kupambana masiku ano?”
Limeneli si funso lanzeru.
11Nzeru nzabwino ngati choloŵa chomwe,
zimapindulitsa wamoyo aliyense pansi pano.
12Chitetezo cha nzeru
chili ngati chitetezo cha ndalama.
Koma kudziŵa zinthu kukuposerapo,
chifukwa nzeru zimasunga moyo wa amene ali nazo.
13Taganizira ntchito ya Mulungu.
Ndani angathe kuwongola
chinthu chimene Iye adachipanga chokhota?
14Uzikondwa mwai ukakufikira, ndipo tsoka likakugwera uzilingalirapo bwino pamenepo. Udziŵe kuti ndi Mulungu yemwe amene amatumiza mwai ndi tsoka. Amatero kuti munthu asadziŵiretu zimene zidzachitike m'tsogolo.
15Pa moyo wanga wopandapakewu, ndaona zinthu ziŵiri izi: mwina anthu abwino amaonongeka, zabwino chichitirecho, mwinanso anthu oipa amakhala ndi moyo nthaŵi yaitali, zoipa chichitirecho.
16Ndiye usachite kunkitsa nako kulungama, kapena kunkitsa nazo nzeru. Nanga ufere ziti?
17Usachite kunyanyanso kuipa, usanyanye nawonso uchitsiru. Nanga uferenji nthaŵi yako isanakwane?
18Nkwabwino kuti utsate njira imodzi, komanso osataya njira inayo. Munthu woopa Mulungu adzapeza phindu ndi ziŵiri zonsezo.
19Nzeru zimapatsa munthu mphamvu zoposa zimene angampatse atsogoleri khumi amumzinda.
20Ndithudi, pa dziko lapansi palibe munthu amene amachita zabwino zokhazokha osachimwa konse.
21Usamasamala zonse zokamba anthu, mwinamwina udzamva wantchito wako akukutukwana.
22Mumtima mwako ukudziŵa kuti iweyonso udatukwanapo anthu ena.
23Zonsezi ndidaziyesa ndi nzeru zanga. Ndinkati, “Ndidzakhala wanzeru.” Koma nzeruzo zinali nane kutali.
24Zimene zilipo zili kutali ndipo nzozama, kuzamatu kwambiri. Ndani angathe kuzidziŵa?
25Motero ndidaikapo mtima kwambiri kuti ndidziŵe, ndifufuze ndi kumafunafuna nzeru ndi m'mene zinthu zimakhalira. Ndidafunanso kumvetsa kuipa kwake kwa uchitsiru ndiponso kupusa kwake kwa msala.
26Ndidapeza china choŵaŵa kupambana imfa. Chinthucho ndi mkazi amene ali ngati msampha, amene mtima wake uli ngati ukonde, ndipo manja ake ali ngati maunyolo. Munthu wokondweretsa Mulungu amamthaŵa mkaziyo, koma wochimwa amalolera kukhala kapolo wake.
27Zimenezitu nzimene ndidazipeza pakusonkhanitsa izi ndi izi, kuti ndidziŵe m'mene zinthu zimakhalira.
28Ndizo zimene mtima wanga unkazifunafuna kaŵirikaŵiri, koma osazipeza. Ndidapeza mwamuna mmodzi yekha wolungama pakati pa anthu 1,000, koma mkazi wolungama sindidampezepo ndi mmodzi yemwe pakati pa anthu onsewo.
29Ndidapeza chokhachi chakuti Mulungu pomulenga munthu, adampatsa mtima wolungama, koma anthu amatsata njira zaozao zambirimbiri.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.