2 Maf. 21 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Manase mfumu ya ku Yuda(2 Mbi. 33.1-20)

1Manase anali wa zaka khumi ndi ziŵiri pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 55 ku Yerusalemu. Mai wake anali Hepeziba.

2Yer. 15.4 Iyeyo adachita zoipa pamaso pa Chauta, potsata ntchito zonyansa za anthu a mitundu ina amene Chauta adaŵapirikitsa pofika Aisraele.

3Manaseyo adamanganso akachisi amene bambo wake Hezekiya adaaononga ku mapiri. Adamangira Baala maguwa, napanga mafano monga m'mene ankachitira Ahabu mfumu ya Aisraele. Ndipo ankapembedza zinthu zakuthambo namazitumikira.

42Sam. 7.13 Adamangira mafanowo maguwa m'Nyumba ya Chauta imene Chautayo adaanena kuti, “Ku Yerusalemu ndiye kumene azikandipembedzerako.”

5Manase yemweyo adamangira zinthu zakuthambo maguwa m'mabwalo aŵiri a Nyumba ya Chauta.

6Pambuyo pake adapereka mwana wake wamwamuna ngati nsembe. Ankatama mizimu mopemba ndiponso ankaombeza maula, namachita zobwebwetetsa ndi zaufiti. Adachita zoipa zambiri zimene zidakwiyitsa Chauta.

71Maf. 9.3-5; 2Mbi. 7.12-18 Adaika m'Nyumba ya Chauta fano losema la Asera. Nyumba imeneyo, Chauta anali atauza Davide ndi Solomoni mwana wake kuti, “M'nyumba iyi ndi mu Yerusalemu muno, ndimo m'mene ndasankha pakati pa mafuko onse a Israele kuti azindipembedzeramo mpaka muyaya.

8Tsono sindidzalola kuti Aisraele adzachotsedwe m'dziko lao limene ndidapatsa makolo ao, malinga kuti iwowo azisamala kuchita zinthu zonse motsata Malamulo amene ndaŵalamula, ndiponso motsata Malamulo amene Mose mtumiki wanga adaŵalamula.”

9Koma anthuwo sadamve zimenezo, ndipo Manase adaŵasokeretsa ndi kuŵachimwitsa kwambiri kupambana anthu a mitundu ina amene Chauta adaŵaononga pofika Aisraele.

10Nchifukwa chake Chauta adalankhula kudzera mwa atumiki ake aneneri, nati,

11“Manase mfumu ya ku Yuda wachita zonyansa zambiri, ndipo wachita zoipa kupambana zoipa zonse zimene ankachita Aamori amene adaalipo kale iye asanabadwe, ndipo wachimwitsanso anthu a ku Yuda ndi mafano akewo.

12Nchifukwa chake Ine Chauta, Mulungu wa Israele, ndikunena kuti, ‘Ndithu, ndidzabweretsa pa Yerusalemu ndi pa Yuda choipa chakuti aliyense amene adzachimve, adzadodoma nkupukusa mutu.

13Ndidzalanga Yerusalemu monga ndidalangira Samariya ndi Ahabu, pamodzi ndi banja lake. Tsono ndidzayeretsa Yerusalemu pochotsa anthu ake, monga momwe munthu amachitira popukuta mbale, ndipo ataipukuta amaivundikira pansi.

14Tsono anthu otsala ndidzaŵachotsa m'dziko ndi kuŵapereka m'manja mwa adani ao. Adzaphedwa ndipo adaniwo adzaŵalanda zonse.

15Zidzatero popeza kuti akhala akundichimwira ndipo andikwiyitsa, kuyambira tsiku limene makolo ao adatuluka ku Ejipito mpaka lero lino.’ ”

16Tsono Manase uja adakhetsa kwambiri magazi a anthu osachimwa, mpaka magaziwo kuyenderera m'miseu ya Yerusalemu kuyambira mbali ina mpaka mbali ina. Izi zidaonjezera pa machimo amene adachimwitsa nawo Ayuda pakuŵachititsa zoipa zonyoza Chauta.

17Tsono ntchito zina za Manase ndi zonse zimene adachita, ndiponso machimo amene adachita, zonsezo zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda.

18Choncho Manase adamwalira, naikidwa m'manda m'munda wa ku nyumba yake, m'munda wa Uza. Tsono Amoni mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.

Amoni mfumu ya ku Yuda(2 Mbi. 33.21-25)

19Amoni anali wa zaka 22 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka ziŵiri ku Yerusalemu. Mai wake anali Mesulemeti, mwana wa Haruzi wa ku Yotiba.

20Iyeyo adachita zoipa pamaso pa Chauta monga m'mene ankachitira Manase bambo wake.

21Iyeyo ankatsata chitsanzo choipa cha bambo wake pazonse, namatumikira mafano amene bambo wake ankaŵatumikira ndi kumaŵapembedza.

22Adakana Chauta, Mulungu wa makolo ake, ndipo sadamvere malamulo ake.

23Tsono anyamata ake adamchita chiwembu, namupha m'nyumba mwake momwe.

24Koma anthu am'dzikomo adapha onse aja amene adamchita chiwembu mfumu Amoniyo. Kenanaka anthuwo adalonga Yosiya mwana wake kuti akhale mfumu m'malo mwake.

25Tsono ntchito zonse zimene adachita Amoni zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda.

26Atamwalira adaikidwa m'manda m'munda wa ku nyumba yake, m'munda wa Uza. Ndipo mwana wake Yosiya adaloŵa ufumu m'malo mwake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help