Miy. 31 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mau a Lemuwele.

1Naŵa mau a mfumu Lemuwele wa ku Masa

amene adamphunzitsa mai wake:

2Nchiyani, mwana wanga?

Nchiyani, mwana wa m'mimba mwanga?

Nchiyani, mwana wanga amene ndidachita

kukupempha polonjeza ndi malumbiro?

3Mphamvu zako usathere pa akazi,

usamayenda nawo ameneŵa, amaononga ndi mafumu omwe.

4Iwe Lemuwele, mafumu sayenera kumamwa vinyo,

olamulira asamalakalaka zakumwa zaukali,

5kuwopa kuti angaiŵale malamulo a dziko,

ndi kukhotetsa zinthu zoyenerera anthu osauka.

6Munthu amene ali pafupi kufa,

uzimpatsa chakumwa chaukali,

ndipo munthu amene ali pa mavuto oopsa, uzimpatsa vinyo.

7Amwe kuti aiŵale umphaŵi wake

asakumbukirenso kuvutika kwake.

8Munthu wosalankhula umlankhulire ndiwe.

Anthu osiyidwa uŵalankhulire pa zoŵayenerera.

9Uzilankhula ndi kuweruza mwachilungamo.

Uziteteza amphaŵi ndi osauka.

Mkazi wokhoza ntchito.

10Kodi mkazi wolemerera angathe kumpeza ndani?

Ndi wokwera mtengo kuposa miyala ya yamtengowapatali.

11Mtima wa mwamuna wake umamkhulupirira,

ndipo mwamunayo sadzasoŵa phindu.

12Masiku onse a moyo wake,

mkaziyo amachitira mwamuna wake zabwino osati zoipa.

13Amanka nafunafuna ubweya ndi thonje,

ndipo amagwira ntchito ndi manja ake mwaufulu.

14Ali ngati zombo za anthu amalonda,

zakudya zake amakazitenga kutali.

15Amadzuka usikusiku

nkuyamba kukonzera chakudya anthu a pabanja pake,

ndi kuŵagaŵira ntchito adzakazi ake.

16Amalingalira za munda, naugula.

Amalima munda wamphesa ndi ndalama

zozipeza ndi manja ake.

17Amavala dzilimbe

ndipo sachita manja khoba pogwira ntchito.

18Amazindikira kuti malonda ake ndi aphindu,

choncho nyale yake sizima usiku wonse.

19Thonje amadzilukira yekha,

ndipo nsalu amadziwombera yekha.

20Anthu osauka amaŵachitira chifundo,

amphaŵi amaŵapatsa chithandizo.

21A pabanja pake saŵaopera kuti nkufa nacho chisanu,

poti amadziŵa kuti onsewo amavala zovala zofunda.

22Amadzipangira yekha zofunda,

ndipo iye amavala zovala zabafuta

ndi za mtengo wapatali.

23Mwamuna wake ndi wodziŵika ndithu ku mabwalo,

akakhala pakati pa akuluakulu a dziko.

24Mkazi ameneyu amasoka zovala za nsalu yabafuta,

nazigulitsa,

amaperekanso mipango kwa anthu amalonda.

25Mphamvu ndi ulemu zimakhala ngati chovala chake.

Amaganiza zakutsogolo mosangalala.

26Amalankhula mwanzeru,

ndipo amaphunzitsa anthu ndi mau okoma.

27Amayang'anira makhalidwe a anthu a pabanja pake,

ndipo sachita ulesi mpang'ono pomwe.

28Ana ake amamnyadira nkumutchula kuti ndi wodala.

Mwamuna wake nayenso amamtamanda, amati,

29“Inde alipo akazi ambiri olemerera kwabasi,

koma kuyerekeza ndi iwe, onsewo nchabe.”

30Nkhope yachikoka ndi yonyenga,

kukongola nkosakhalitsa,

koma mkazi woopa Chauta ndiye woyenera kumtamanda.

31Muzimlemekeza chifukwa cha zochita zake,

ntchito zake zizimpatsa ulemu ku mabwalo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help