1Miyambo ya Solomoni:
Mwana wanzeru amakondweretsa atate ake,
koma mwana wopusa amanyoza amai ake.
2Chuma chochipeza monyenga sichipindulitsa,
koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.
3Chauta salola kuti munthu womukondweretsa iye,
azikhala ndi njala,
koma zimene woipa amazilakalaka, Mulungu amam'mana.
4Manja aulesi amagwetsa munthu mu umphaŵi,
koma manja achangu amalemeretsa munthu.
5Mwana womakolola nthaŵi yachilimwe ndiye wanzeru,
koma womangogona nthaŵi yokolola amachititsa manyazi.
6Madalitso amakhala pa munthu wokondweretsa Mulungu,
koma pakamwa pa munthu woipa pamabisa zandeu.
7Munthu wabwino anzake adzamkumbukira ngati dalitso,
pamene woipa, mbiri yake idzatha ngati chinthu choola.
8Munthu wa mtima wanzeru adzasamala malamulo,
koma chitsiru chomangolongolola chidzaonongeka.
9Munthu woyenda mwaungwiro, amayenda mosatekeseka.
Koma woyenda njira zoipa, adzadziŵika.
10Munthu wotsinzinira maso monyenga, amadzetsa mavuto,
wodzudzula molimba mtima amadzetsa mtendere.
11Pakamwa pa munthu wabwino ndi kasupe wa moyo,
koma pakamwa pa munthu woipa pamabisa zandeu.
12 Yak. 5.20; 1Pet. 4.8 Chidani chimautsa mikangano,
koma chikondi chimaphimba zolakwa zonse.
13Pakamwa pa munthu womvetsa zinthu pamatuluka zanzeru,
koma pamsana pa munthu wopanda nzeru sipachoka tsatsa.
14Anzeru amakundika nzeru,
koma kubwebwetuka kwa chitsiru kumadzetsa chiwonongeko.
15Chuma cha munthu wolemera ndiye chitetezo chake,
koma umphaŵi wa anthu osauka ndiye chiwonongeko chao.
16Moyo ndiye malipiro a anthu ochita zabwino,
koma phindu la ochimwa limadzetsa machimo ena.
17Wosamala malangizo amayenda pa njira ya moyo,
koma wokana chidzudzulo amasokera.
18Wobisa chidani chake ndi munthu wonama,
ndipo wochita ugogodi nchitsiru.
19Mau akachuluka, zolakwa sizisoŵa,
koma amene amasunga pakamwa ndi wanzeru.
20Mau a munthu wochita zabwino,
ali ngati siliva wabwino kwambiri,
koma maganizo a anthu oipa ngachabe.
21Mau a anthu wabwino amaphunzitsa ambiri,
koma zitsiru zimafa chifukwa chosoŵa nzeru.
22Madalitso a Chauta ndiwo amalemeretsa,
ntchito za munthu siziwonjezerapo kanthu.
23Kwa chitsiru kulakwa kumakhala ngati maseŵera,
koma kwa munthu womvetsa zinthu
kuchita zanzeru ndiye kumapatsa chimwemwe.
24Chimene woipa amachiwopa chidzamgwera,
koma zimene munthu wabwino amazilakalaka adzazipeza.
25Namondwe akaomba, oipa amachotsedwa,
koma anthu ochita chilungamo amakhazikika mpaka muyaya.
26Momwe amakhalira vinyo wosasa m'kamwa,
momwe umakhalira utsi m'maso,
ndi momwenso amakhalira mlesi kwa amene amamtuma.
27Kuwopa Chauta kumatalikitsa moyo,
koma zaka za anthu oipa zidzachepa.
28Chiyembekezo cha wokhulupirira chimapezetsa chimwemwe,
koma zimene woipa amayembekezera, zimafera m'mazira.
29Chauta ndi linga loteteza munthu woyenda molungama,
koma amaononga wochita zoipa.
30Munthu wabwino sadzachotsedwa pamalo pake,
koma woipa sadzakhazikika pa dziko.
31Pakamwa pa wochita chilungamo pamatuluka zanzeru,
koma lilime lokhota adzalidula.
32Anthu omvera Mulungu amadziŵa zoyenera kulankhula,
koma pakamwa pa anthu oipa pamatuluka zosayenera.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.