Gen. 46 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yakobe pamodzi ndi banja lake apita ku Ejipito

1Israele adasonkhanitsa zake zonse napita ku Beereseba kukapereka nsembe kwa Mulungu wa atate ake Isaki.

2Usiku Mulungu adaonekera Israele m'masomphenya, ndipo adati, “Yakobe, Yakobe!” Iye adayankha kuti, “Ee Ambuye!”

3Ndipo adamuuza kuti “Ine ndine Mulungu, Mulungu wa atate ako. Usaope kupita ku Ejipito. Kumeneko ndidzachulukitsa zidzukulu zako, kuti zikhale mtundu waukulu wa anthu.

4Ineyo ndidzapita nawe ku Ejipito, ndipo zidzukulu zakozo ndidzazibwezeranso konkuno. Yosefe adzakhala nawe pa nthaŵi yako yomwalira.”

5Tsono Yakobe adanyamuka kuchoka ku Beereseba. Ana ake a Israele aja adakweza bambo wao Yakobe, pamodzi ndi akazi ndi ana, pa ngolo zimene Farao adaatumiza.

6Ntc. 7.15 Adatenga zoŵeta zao zonse pamodzi ndi zinthu zonse zimene anali nazo ku Kanani, ndipo adapita ku Ejipito. Yakobe adatenga zidzukulu zake zonse,

7ndiye kuti ana ndi adzukulu ake aamuna, ndiponso ana ndi adzukulu ake aakazi. Onsewo adapita nawo ku Ejipito.

8Naŵa maina a Aisraele amene adapita ku Ejipito, ndiye kuti Yakobe ndi ana ake. Rubeni, mwana wachisamba wa Yakobe,

9ndi ana aŵa a Rubeni: Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi.

10Ana a Simeoni anali aŵa: Yemuwele, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Shaulo, amene mai wake anali mkazi wa ku Kanani.

11Ana a Levi anali aŵa: Geresoni, Kohati ndi Merari.

12Ana a Yuda anali aŵa: Ere, Onani, Sela, Perezi ndi Zera, (koma Ere ndi Onani adaafera ku Kanani.) Ana a Perezi anali aŵa: Hezironi ndi Hamuli.

13Ana a Isakara anali aŵa: Tola, Puva, Iyobu ndi Simironi.

14Ana a Zebuloni anali aŵa: Seredi, Eloni ndi Yaleele.

15(Ana ameneŵa ndiwo amene Leya adabalira Yakobe ku Mesopotamiya kuja, ndipo panalinso mwana wake wamkazi Dina. Adzukulu obadwa mwa Leya analipo 33 onse pamodzi.)

16Ana a Gadi anali aŵa: Zifiyoni, Hagi, Suni, Eziboni, Eri, Arodi ndi Areli.

17Ana a Asere anali aŵa: Imina, Isiva, Isivi, Beriya ndi mlongo wao Sera. Ana a Beriya anali aŵa: Hebere ndi Malikiele.

18(Onseŵa anali adzukulu a Yakobe obadwa mwa Zilipa amene Labani adaapereka kwa mwana wake Leya.)

19Ana a Rakele mkazi wa Yakobe anali aŵa: Yosefe ndi Benjamini.

20Gen. 41.50-52 Manase ndi Efuremu anali ana amene Yosefe adabereka mwa Asenati, mwana wa Potifera wansembe wa ku Oni.

21Ana a Benjamini anali aŵa: Bela, Bekara, Asibele, Gera, Naamani, Ehi, Rosi, Mupimu, Hupimu ndi Aridi.

22(Onseŵa 14 ndiwo adzukulu a Yakobe mwa mkazi wake Rakele.)

23Dani anali ndi mwana mmodzi yekha dzina lake Husimu.

24Ana a Nafutali anali aŵa: Yazeele, Guni, Yezera ndi Silemu.

25(Asanu ndi aŵiriŵa ndiwo adzukulu a Yakobe amene adabadwa mwa Biliha, amene Labani adaapereka kwa mwana wake Rakele.)

26Chiŵerengero chonse cha anthu ochokera mwa Yakobe, amene adapita ku Ejipito, chinali 66, osaŵerengera akazi a ana ake.

27Ntc. 7.14Popeza kuti Yosefe adaabereka ana aŵiri ku Ejipito, chiŵerengero chidafika 70. Onseŵa anali a m'banja la Yakobe, ndipo ndiwo adapita ku Ejipito.

Yakobe ndi banja lake ku Ejipito

28Israele adatuma Yuda kuti atsogole kupita kwa Yosefe kukampempha kuti akamchingamire ku dziko la Goseni. Yakobe atafika ku dziko la Goseni,

29Yosefe adaitanitsa galeta lake, napita ku Goseni kukakumana ndi Israele bambo wake. Atangofika pamaso pake, adamkumbatira m'khosi, nalira nthaŵi yaitali ndithu, osalekerapo.

30Israele adauza Yosefe kuti, “Tsopano ndimwalire, popeza kuti ndakuwona, ndipo ndikudziŵadi kuti uli moyo.”

31Apo Yosefe adauza abale ake aja pamodzi ndi banja lonse la bambo wake kuti “Ndipita ndikamuuze Farao kuti abale anga pamodzi ndi onse a m'banja la atate anga amene ankakhala ku Kanani, abwera kuno kwa ine.

32Anthu ameneŵa ndi abusa, amaŵeta zoŵeta. Nkhosa zao ndi ng'ombe zomwe abwera nazo, pamodzi ndi zinthu zao zonse.

33Tsono Farao akakuitanani, ndipo akakufunsani kuti, ‘Mumagwira ntchito yanji?’

34Inu mukamuuze kuti, ‘Ife bwana, ndife oŵeta zoŵeta kuyambira ubwana wathu, monga momwe ankachitira makolo athu.’ Mukatero, ndiye kuti mudzatha kukakhala m'dziko la Goseni.” Yosefe adaanena zimenezi chifukwa choti Aejipito ankanyansidwa ndi abusa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help