Esr. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Estere akwatiwa ndi mfumu

1Pambuyo pake, mtima wake utatsika, Ahasuwero adakumbukira Vasiti ndi zimene Vasitiyo adaachita, ndiponso lamulo limene adaamuikira.

2Tsono anthu amene ankatumikira mfumu adaiwuza kuti, “Aisankhulire mfumu anamwali okongola.

3Mfumu iike akapitao m'madera onse a dziko lake, kuti asonkhanitse anamwali onse okongola ku nyumba yosungira azikazi ku Susa, likulu la dziko, ndipo kuti asungidwe ndi Hegai, mdindo wofulidwa wa mfumu, amene ankayang'anira azikaziwo. Aŵapatse zodzoladzola.

4Namwali amene adzakondwetse mfumu, akhale mkazi wamkulu m'malo mwa Vasiti.” Zimenezi zidakondwetsa mfumu, ndipo idachitadi momwemo.

5Ku Susa, likulu la dziko, kunali Myuda wina, dzina lake Mordekai, mwana wa Yairo, mwana wa Semei, mwana wa Kisi, Mbenjamini.

62Maf. 24.10-16; 2Mbi. 36.10Iyeyo anali mmodzi mwa anthu ogwidwa ukapolo pamodzi ndi Yekoniya, mfumu ya ku Yuda, amene Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, idaaŵatenga kuŵachotsa ku Yerusalemu.

7Mordekai anali atalera Hadasa, ndiye kuti Estere, mwana wamkazi wa bambo wake wamng'ono, poti analibe bambo kapena mai. Namwaliyo anali wokongola ndi wooneka bwino. Pamene bambo wake ndi mai wake adamwalira, Mordekai adamtenga, kukhala ngati mwana wake.

8Choncho pamene mfumu idalamula ndi kulilengeza lamulo lake lija, ndipo pamene anamwali ambiri adaŵasonkhanitsa ku Susa, likulu la dziko, Hegai akuŵasunga, Estere nayenso adamtenga kunka naye ku nyumba ya mfumu, kuti Hegai amene ankayang'anira azikazi uja, azikamsamalira.

9Namwaliyo adamkomera Hegai, ndipo zinthu zinkamuyendera bwino. Motero adampatsa mofulumira zodzoladzola, pamodzi ndi chakudya chapadera. Adampatsanso anamwali asanu ndi aŵiri a ku nyumba ya mfumu oti azimtumikira. Iyeyo ndi anamwali ake omtumikirawo adaŵapatsa malo abwino kwambiri m'nyumba mosungira akazi.

10Estere sadaulule kanthu za mtundu wake kapena za achibale ake, poti Mordekai adaamuletsa kuti asaulule.

11Tsiku ndi tsiku Mordekai ankayenda ku bwalo la nyumba yosungira azikazi ija, kuti aonetsetse m'mene ankakhalira Estere ndiponso m'mene zinkamuyendera zinthu.

12Tsono nthaŵi idafika yakuti namwali aliyense apite kwa mfumu Ahasuwero, atatha miyezi khumi ndi iŵiri ali pa mwambo wake wokonzekera. Nthaŵi imeneyi inali nthaŵi yoti adzikongoletse, miyezi isanu ndi umodzi yodzola mafuta a mure, miyezi isanu ndi umodzi inayo yodzola zonunkhira zina.

13Namwali akamapita kunyumba kwa mfumu, ankamupatsa kalikonse kamene ankafuna kutenga pochoka ku nyumba yosungira azikaziyo, kuti apite nazo ku nyumba ya mfumu.

14Ankapita madzulo nkumabwerako m'maŵa, namapita ku nyumba yachiŵiri yosungiramo azikazi, imene Hegai mdindo wofulidwa wa mfumu, ankayang'anira. M'nyumbamo iye ankasunga azikazi a mfumu. Mzikazi aliyense sankapitanso kwa mfumu, koma pokhapokha mfumu itakondwera naye nkuchita kumuitana pomtchula dzina.

15Pamene idakwana nthaŵi yomloŵetsa Estere, mwana wa Abihaili, bambo wamng'ono wa Mordekai, amene Mordekaiyo adaamlera ngati mwana wake, Estere sadapemphe kanthu kalikonse. Adangopempha zokhazo zimene Hegai, mdindo wofulidwa wa mfumu, amene ankayang'anira azikazi, adaamuuza. Onse amene adamuwona Estere, adakondwera naye.

16Tsono adamtenga Estereyo napita naye kwa mfumu Ahasuwero ku nyumba yake yaufumu pa mwezi wakhumi wa Tebeti, pa chaka chachisanu ndi chiŵiri cha ufumu wake.

17Mfumu idamkonda Estere kopambana akazi onse. Ndipo zinthu zinkamuyendera bwino pamaso pa mfumu kupambana anamwali onse, kotero kuti mfumuyo idamuveka chisoti chachifumu, nimsandutsa mfumukazi m'malo mwa Vasiti uja.

18Pamenepo mfumu idachita phwando lalikulu kuchitira akuluakulu ake onse ndi atumiki ake. Phwando limenelo linali la Estere. Idapumulitsanso msonkho anthu a m'maiko ake onse, ndipo idapereka mphatso mwa ufulu woyenera mafumu.

Mordekai apulumutsa moyo wa mfumu

19Pamene adasonkhanitsa anamwali ena pamodzi kachiŵiri, Mordekai adaakhala pansi pa chipata cha mfumu.

20Tsono Estere anali asanaulule za achibale ake, ngakhalenso za mtundu wake, monga momwe Mordekai adaamuuzira. Paja Estere ankamvera Mordekai monga pa nthaŵi yomwe Mordekaiyo ankamulera.

21Masiku amenewo, pamene Mordekai anali ndi ntchito yokhala pa chipata cha mfumu, Bigitana ndi Teresi, adindo aŵiri ofulidwa a mfumu, amene ankalonda pa khomo loloŵera mfumu, adapsa mtima nafuna kupha mfumu Ahasuwero.

22Zimenezi Mordekai adaazidziŵa, nakauza Estere, mkazi wamkulu wa mfumu, ndipo iye adakauza mfumu m'malo mwa Mordekai.

23Pamene nkhaniyo adaifufuza napeza kuti nzoonadi, aŵiri onsewo adapachikidwa pa mtengo. Ndipo zimenezi zidalembedwa m'buku la Mbiri pamaso pa mfumu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help