1
10Koma Mulungu adzaŵapatsa ulemerero, ulemu ndi mtendere onse ochita zabwino, poyamba Ayuda, kenaka anthu a mitundu inanso.
11Deut. 10.17Pajatu Mulungu alibe tsankho.
12Anthu onse amene adachimwa osadziŵa Malamulo, iwonso adzaonongeka ngakhale sadaŵadziŵe Malamulowo. Ndipo onse amene adachimwa atadziŵa Malamulo, adzaweruzidwa potsata Malamulowo.
13Pakuti amene ali olungama pamaso pa Mulungu si amene amangomva Malamulo chabe ai. Koma okhawo amene amachitadi zonenedwa m'Malamulo ndiwo amene Mulungu adzaŵaona kuti ngolungama.
14Anthu amene sali Ayuda alibe Malamulo, koma pamene mwa iwo okha amachita zimene Malamulowo anena, amaonetsa kuti ali nawo malamulo mumtima mwao, ngakhale alibe Malamulo a Mose.
15Ntchito zaozo zimatsimikiza kuti Malamulowo ndi olembedwa m'mitima mwao. Mitima yao yomwe imatsimikiza kuti ndi momwemodi, popeza kuti maganizo ao m'chikatikati mwina amaŵatsutsa, mwina amaŵavomereza.
16Monga unenera Uthenga Wabwino umene ndimalalika, zidzateronso pa tsiku lija limene Mulungu mwa Khristu Yesu adzaweruza zinsinsi za m'mitima mwa anthu.
Za Ayuda ndi Malamulo17Koma tsono iweyo amene umati ndiwe Myuda, umadalira Malamulo, ndipo umanyadira Mulungu wako.
18Ukudziŵa zimene Mulungu afuna kuti uchite, ndipo chifukwa udaphunzira Malamulowo, umadziŵanso kusiyanitsa pakati pa zabwino ndi zoipa.
19Umakhulupirira kuti ndiwe mtsogoleri wa anthu akhungu, nyale younikira anthu amene ali mu mdima,
20mlangizi wa anthu opusa, ndiponso mphunzitsi wa anthu osadziŵa. Umatsimikiza kuti m'Malamulowo umapezamo nzeru zonse ndi zoona zonse.
21Tsono iwe wophunzitsa ena, bwanji sukudziphunzitsa wekha? Iwe wolalika kuti, “Osamaba,” bwanji iwenso umaba?
22Nanga iwe wonena kuti, “Osamachita chigololo,” bwanji iwenso umachita chigololo? Iwe amene umanyansidwa ndi mafano, bwanji umaba za m'nyumba zopembedzeramo mafanowo?
23Iwe wonyadira Malamulo a Mulungu, bwanji umachititsa Mulungu manyazi pakuphwanya Malamulowo?
24Yes. 52.5 Ndi monga Malembo anenera kuti, “Anthu akunja amanyoza Mulungu chifukwa cha inu Ayudanu.”
25Kuumbala kwako nkopindulitsa ngati utsata Malamulo a Mulungu. Koma ngati suŵatsata Malamulowo, ukadayenera kungokhala wosaumbalatu basi.
26Koma ngati munthu wosaumbala atsata zimene Malamulowo anena, kodi iyeyu pamaso pa Mulungu sadzakhala ngati munthu woumbala, ngakhale ndi wosaumbala m'thupi?
27Nchifukwa chake wosaumbalayo amene amatsata Malamulo ndiye adzakutsutsa iwe amene uli woumbala, ndipo uli ndi Malamulo olembedwa, koma umaŵaphwanya.
28Myuda weniweni si amene amangooneka chabe ngati Myuda pamaso pa anthu. Ndipo kuumbala kwenikweni si kumene kumachitika m'thupi nkuwonekera ku anthu ai.
29Deut. 30.6Myuda weniwenitu ndi amene ali Myuda mumtima mwake, ndipo kuumbala kwenikweni ndi kwa mtima, kochitika ndi Mzimu Woyera, osati ndi Malamulo olembedwa ai. Woyamikira munthu wotere ndi Mulungu, osati anthu ai.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.