1Abale, inu nomwe mukudziŵa kuti kucheza kuja tidadzacheza kwanuku, kunali kwaphindu.
2Ntc. 16.19-24; Ntc. 17.1-9 Monga mukudziŵa, paja nthaŵi imene ija nkuti anthu a ku Filipi atatizunza kale ndi kutichita chipongwe. Komabe Mulungu wathu adatilimbitsa mtima mpaka tidakulalikirani ndithu Uthenga wake Wabwino, ngakhale ambiri ankatsutsana nafe.
3Pakuti zimene timalalika sitizilalika chifukwa chofuna kuphunzitsa zonama, kapena kuganiza zoipa, kapena kufuna kunyenga anthu ai.
4Koma timalalika chifukwa Mulungu adativomereza natisungiza Uthenga Wabwino kuti tiulalike. Choncho tikamaphunzitsa sitifuna kukondweretsa anthu, koma timafuna kukondweretsa Mulungu, amene amapenyetsetsa mitima yathu.
5Monga mukudziŵa, sitidabwere kwanuko ndi mau oshashalika kapena ndi mtima womangofuna phindu. Apo Mulungu angathe kutichitira umboni.
6Sitinkafunanso ulemu wochokera kwa anthu, kapena kwa inu, kapena kwa ena, ngakhale kunali kotheka kukulamulani kuti mutithandize, popeza kuti ndife atumwi a Khristu.
7Koma tidakhala ofatsa pakati panu ngati mai wosamalira ana ake.
8Tinkakukondani, ndipo chifukwa cha kukulakalakani kwambiri, tidatsimikiza zogaŵana nanu osati Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso ngakhale moyo wathu womwe.
9Abale, simukumbukira nanga kuti tinkagwira ntchito kwambiri mpaka kutopa? Monse muja tinkakulalikirani Uthenga Wabwino wa Mulungu, tinkagwira ntchito zamanja usana ndi usiku, kuwopa kuti tingavutitse wina aliyense mwa inu.
10Inu ndinu mboni, Mulungu yemwe ndi mboninso, kuti mkhalidwe wathu pakati pa inu okhulupirira unali wangwiro, wolungama, ndi wopanda cholakwa.
11Paja mukudziŵa kuti, tinkasamala aliyense mwa inu monga momwe amachitira bambo ndi ana ake.
12Tinkakulimbitsani mtima, kukuthuzitsani mtima ndi kukupemphani kuti mayendedwe anu akhale okomera Mulungu, amene amakuitanani kuti mukaloŵe mu Ufumu wake waulemerero.
13Pa mbali yathu, timathokoza Mulungu kosalekeza. Timatero chifukwa chakuti pamene mudamva mau a Mulungu amene tidakulalikirani, mudaŵalandira osati ngati mau a anthu chabe, koma monga momwe aliri ndithu, mau a Mulungu. Mauwo ndi omwe akugwira ntchito mwa inu okhulupirira.
14Ntc. 17.5 Abale, zimene zidakugwerani inu ndi zomwe zidagweranso mipingo ya Mulungu ya mwa Khristu Yesu imene ili ku Yudeya. Paja inunso anthu akwanu adakuzunzani monga momwe Ayuda adazunzira akhristu a ku Yudeya.
15Ntc. 9.23, 29; 13.45, 50; 14.2, 5, 19; 17.5, 13; 18.12Ayudawo ndi amene adapha Ambuye Yesu ndi aneneri akale, ndipo adatizunza ifenso kwambiri. Ameneŵa sakondweretsa Mulungu konse, ndipo amadana ndi anthu onse.
16Iwowotu amatiletsa kulalika Uthenga Wabwino kwa anthu a mitundu ina woŵathandiza kuti apulumuke. Motero nthaŵi zonse amanka nawonjezerawonjezera machimo ao, mwakuti tsopano mkwiyo wa Mulungu waŵagwera.
Paulo alakalaka kukayenderanso Atesalonika17Abale, pamene tidasiyana nanu ngakhale kanthaŵi pang'ono, tinkalakalaka kwambiri kuwonana nanunso maso ndi maso. Ngakhale tinkachoka, mtima wathu unali nanube.
18Nchifukwa chake tidaayesetsa kubweranso kwanuko. Ineyo Paulo, ndidaayesa kangapo, koma Satana adaatilepheretsa.
19Kodi pamaso pa Ambuye athu Yesu, nchiyani chidzakhale chiyembekezo chathu, chimwemwe chathu, ndi mphotho yoti ife tidzanyadire, Iye akadzabweranso? Si ndinu nomwe nanga?
20Pajatu ulemu wathu ndi chimwemwe chathu ndinu amene.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.