Ezek. 40 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ezekiele atengedwa kupita ku Yerusalemu(40.1—48.35)

1Ku mayambiriro a chaka, tsiku lakhumi la mwezi, chaka cha 25 cha ukapolo wathu, ndiye kuti patapita zaka khumi ndi zinai Yerusalemu ataonongedwa, dzanja la Chauta lidandigwira nkupita nane ku Yerusalemu.

2Chiv. 21.10 Ngati kutulo Chauta adapita nane ku dziko la Israele, nandiika pa phiri lalitali pamene ndidaona ngati mzinda.

3Chiv. 11.1; 21.15 Atandifikitsa kumeneko, ndidaona munthu wonyezimira ngati mkuŵa. M'manja mwake anali ndi chingwe chabafuta ndi bango loyesera, ndipo adaaimirira pa chipata.

4Munthuyo adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, penyetsetsa ndipo umvetsetse bwinobwino. Uikepo mtima pa zonse zimene ndikukuwonetsa, pakuti chimenechi ndicho chifukwa chake chimene adakubweretsera kuno. Tsono ukaŵauze Aisraele zonse zimene uziwonezi.”

Chipata chakuvuma

5 1Maf. 6.1-38; 2Mbi. 3.1-9 Tsono ndidaona chipupa chozinga Nyumba ya Mulungu ponseponse. Munthu uja anali ndi bango lopimira m'manja mwake. Bangolo kutalika kwake linali mamita atatu. Adapima kuchindikira kwa chipupacho napeza kuti ndi bango lathunthu. Kutalika kwake cham'mwamba kunalinso bango lathunthu.

6Adapita ku chipata choyang'ana kuvuma, adakwera pa makwerero ake napima chiwundo cha pachipatapo, kutalika kwake kunali bango lathunthu.

7Panalinso zipinda za alonda, ndipo chilichonse chinali bango lathunthu m'litali mwake, chimodzimodzinso mu ufupi mwake, bango lathunthu. Mipata ya pakati pa zipindazo inali ya mamita aŵiri ndi theka. Ndipo chiwundo cha pachipata pafupi ndi khonde lam'kati lapachipata, chinali bango lathunthu.

8Adapima khonde lam'kati lapachipata, napeza kuti linali la mamita anai.

9Mphuthu zake zinali mita limodzi kuchindikira kwake. Khonde lam'kati lapachipata linali kumapeto kwenikweni pafupi ndi Nyumba ya Mulungu.

10M'kati mwa chipata chakuvumacho munali zipinda za alonda zitatu mbali iliyonse. Zitatu zonsezo zinali zolingana, ndipo mphuthu zake pa mbali zonse zinali zolingananso.

11Pambuyo pake adapima chipata choloŵera. Chinali cha mamita asanu muufupi mwake. M'litali mwake chinali cha mamita 6 ndi theka.

12Kumaso kwa zipinda za alonda zija kunali kachipupa ka mita limodzi m'litali mwake ndi muufupi momwe. Zipinda zitatuzo zinali za mamita atatu mbali zonse.

13Tsono adayesa kutalika kuchokera ku khoma lakumbuyo la chipinda chimodzi mpaka ku khoma la chipinda china, kuchokera ku chitseko mpaka kuchitseko china. Kutalika kwake kunali mamita 12 ndi theka.

14Pambuyo pake adayesa khonde lam'kati, linali la mamita khumi. Ndipo pozungulira khondelo panali bwalo.

15Kuchokera pa khomo lapachipata mpaka ku mapeto a khonde la chipata cham'kati, kutalika kwake kunali mamita 25.

16Makoma a zipinda zija ndiponso makoma a pakati pa zipindazo anali ndi mazenera. Khonde lam'kati linali nawonso mazenera m'kati mwake. Pa makoma onse adaazokotapo zithunzi za kanjedza.

Bwalo lakunja

17Tsono munthu uja adandiloŵetsa m'bwalo lakunja, ndipo ndidaona zipinda ndi mseu wamiyala kuzungulira bwalo lonse. Zipinda zonse pamodzi zinali makumi atatu ndipo zinkayang'ana mseuwo.

18Mseuwo unkayenda m'mphepete mwa zipata zija, molingana ndi kutalika kwake kwa zipatazo. Umenewu unali mseu wam'munsi.

19Tsono adayesa m'kati mwa bwalo kuchokera ku chipata cham'munsi mpaka ku chipata chakunja cha bwalo lam'kati. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.

Chipata chakumpoto

20Pambuyo pake munthuyo adayesa chipata chakumpoto chopitira ku bwalo lakunja. Adayesa m'litali mwake ndi muufupi mwake.

21Zipinda za alonda zimene zinali zitatu pa mbali iliyonse, mphuthu zake ndiponso khonde lake lam'kati, zonse zinali zolingana ndi za chipata choyamba chija. M'litali mwake chinali mamita 25, ndipo muufupi mwake chinali mamita 12 ndi theka.

22Mazenera ake, khonde lake lam'kati ndiponso kanjedza wozokota uja, zonse zinali zolingana ndi zachipata choyang'ana kuvuma. Chipatacho chinali ndi makwerero asanu ndi aŵiri, ndipo khonde lake linali cham'kati.

23Chipata chonga chakuvuma chija chidakaloŵa ku bwalo lam'kati moyang'anana ndi chipata chakumpoto. Adachiyesa kuchokera ku chipata china mpaka ku chipata china, kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.

Chipata chakumwera

24Pambuyo pake munthu uja adapita nane kumwera, ndipo ndidaona chipata choyang'ana kumwera. Adayesa mphuthu zake ndi khonde lake lam'kati, zinali zolingana ndi zinzake zija.

25M'zipinda za chipata chimenechi ndi m'khonde lake lam'kati munali mazenera onga a m'zipinda zina. M'litali mwake munali mamita 25, muufupi mwake munali mamita 12 ndi theka.

26Panalinso makwerero asanu ndi aŵiri, ndipo khonde lake linali cham'kati. Pa mphuthu zake adaazokotapo zithunzi za kanjedza uku ndi uku.

27Bwalo lam'kati linali ndi khomo loyang'ana kumwera. Adaliyesa kuchokera ku chipata chimenechi mpaka ku chipata chakunja, kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.

Bwalo lam'kati: Chipata chakumwera

28Munthu uja adandiloŵetsa m'bwalo lam'kati kudzera ku chipata chakumwera. Adayesa chipatacho, chinali cholingana ndi zinzake zija.

29Zipinda zake, mphuthu zake ndi khonde lake lam'kati zinalinso zolingana ndi zinzake zija. Zipindazo zinali ndi mazenera kuzungulira ponse ndiponso m'khonde mwake. M'litali mwake munali mamita 25, muufupi mwake munali mamita 12 ndi theka.

30Tsono panali makonde pozungulira ponse. Lililonse m'litali mwake munali mamita 12 ndi theka, muufupi mwake mamita aŵiri ndi theka.

31Khonde lake lam'kati lidaayang'ana bwalo lakunja. Pa mphuthu zake adaazokotapo zithunzi za kanjedza, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu.

Chipata chakuvuma

32Kenaka munthuyo adapita nane m'bwalo lam'kati chakuvuma. Adachiyesa chipatacho napeza kuti chinali cholingana ndi zinzake zina.

33Zipinda zake, mphuthu zake ndiponso khonde lake lam'kati zinali zolingana ndi zinzake zija. Zipindazo zinali ndi mazenera kuzungulira ponse, ndiponso m'khonde mwake. M'litali mwake munali mamita 25, muufupi mwake mamita 12 ndi theka.

34Khonde lake lam'kati lidaayang'ana bwalo lakunja, ndipo pa mphuthu zake adaazokotapo zithunzi za kanjedza uku ndi uku. Linali ndi makwerero asanu ndi atatu.

35Pambuyo pake adapita nane ku chipata chakumpoto. Adachiyesa napeza kuti ncholingana ndi zinzake zija.

36Zipinda zake, mphuthu zake ndi khonde lake lam'kati zinali chimodzimodzi. Linali ndi mazenera kuzungulira ponse. M'litali mwake munali mamita 25, muufupi mwake mamita 12 ndi theka.

37Khonde lake lam'kati lidaayang'ana bwalo lakunja. Pa mphuthu zake adaazokotapo zithunzi za kanjedza uku ndi uku, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu.

Nyumba zokonzeramo nsembe

38Panali chipinda ndi khomo lake pafupi ndi khonde lam'kati la kuchipata kumene ankatsukirako nyama ya nsembe zopsereza.

39M'khondemo munali matebulo aŵiri, lina uku lina uku. Ankapherako nyama za nsembe zopsereza, nsembe zopepesera machimo ndiponso nsembe zopepesera kupalamula.

40Kunja kwake kwa khonde lam'kati lija la ku chipata chakumpoto kunali matebulo aŵiri.

41Panali matebulo anai cham'kati, ndiponso anai ena chakunja kwa chipatacho. Onse pamodzi anali matebulo asanu ndi atatu. Pamatebulopo ankapherako nyama za nsembe zopsereza.

42Matebulo anai a nsembe zopsereza anali a miyala yosema. Lililonse m'litali mwake linali la masentimita 75, muufupi mwake linali la masentimita 75, ndipo msinkhu wake unali wa masentimita 50. Patebulopo ankaikapo zipangizo zophera nsembe zopserezazo ndi nsembe zina.

43Motero nyama ya nsembezo ankaiika pa matebulowo. Ndipo mbedza zitalizitali ngati chikhatho anakazimangirira pozungulira ponse cham'kati.

44Tsono munthu uja adapita nane m'kati mwenimweni mwa bwalo. Ndidaonamo zipinda ziŵiri m'kati mwa bwalolo. China chinali pafupi ndi chipata chakumpoto kuyang'ana kumwera. China chinali pafupi ndi chipata chakumwera kuyang'ana kumpoto.

45Tsono adandiwuza kuti, “Chipinda choyang'ana kumwerachi ncha ansembe oyang'anira Nyumba ya Mulungu.

46Chipinda choyang'ana kumpotochi ncha ansembe oyang'anira za guwa lansembe. Ameneŵa ndiwo ana a Zadoki, ndipo ndi okhawo mwa zidzukulu za Levi amene angafike kufupi kudzatumikira Chauta.

Nyumba ya Mulungu

47“Tsono munthu uja adayesa bwalolo, linali lolingana m'litali ndi muufupi mwake, mamita 50 mbali iliyonse. Ndipo guwa linali kumaso kwa Nyumba ya Mulungu.

48Pambuyo pake adapita nane m'khonde lam'kati la Nyumba ya Mulunguyo. Adayesa mphuthu za khondelo zinali za mamita aŵiri ndi theka mbali zonse. Muufupi mwake mwa chipata munali mamita asanu ndi aŵiri. Zipupa za pambali pa chipata zinali za mita limodzi ndi theka mbali zonse.

49Khonde lam'kati m'litali mwake linali la mamita khumi, muufupi mwake mamita asanu ndi limodzi. Panali makwerero khumi, ndipo pambali pa mphuthu panali nsanamira ku mbali zonse.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help