Mas. 71 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero la munthu wokalamba.

1Ine ndimathaŵira kwa Inu Chauta.

Musandichititse manyazi.

2Koma mundilanditse ndi kundipulumutsa,

pakuti ndinu Mulungu wolungama.

Tcherani khutu kuti mundimve,

ndipo mundipulumutse.

3Mundikhalire thanthwe lothaŵirako,

ndiponso linga lolimba lopulumukirako.

Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.

4Landitseni Inu Mulungu wanga kwa anthu oipa,

landitseni ku mphamvu za anthu osalungama ndi ankhalwe.

5Inu Ambuye, ndinu amene ndimakukhulupirirani,

Inu Chauta, ndinu amene ndimakudalirani

kuyambira ubwana wanga.

6Inu mwakhala wondichirikiza

kuyambira pa nthaŵi imene ndidabadwa.

Inu ndinu amene mudanditulutsa m'mimba mwa mai wanga.

Ndimatamanda Inu nthaŵi zonse.

7Ndakhala chinthu chodabwitsa kwa anthu ambiri,

koma Inu ndinu wonditchinjiriza wamphamvu.

8Pakamwa panga pakutamanda Inu,

pakulalika ulemerero wanu tsiku lonse.

9Musanditaye nthaŵi ya ukalamba wanga,

musandisiye ndekha pamene mphamvu zanga zatha,

10Adani anga amandinena,

anthu olondalonda moyo wanga amapangana limodzi,

11namanena kuti, “Mulungu wamsiya yekha.

Mlondoleni, mumgwire,

pakuti palibe ndi mmodzi yemwe woti ampulumutse.”

12Inu Mulungu, musandikhalire kutali.

Inu Mulungu wanga, fulumirani kudzandithandiza.

13Anthu ondineneza achite manyazi ndipo aonongeke.

Anthu ofunafuna kundipweteka anyozedwe,

ndipo achite manyazi kotheratu.

14Koma ine ndidzakhulupirira Inu nthaŵi zonse,

ndipo ndidzapitirizabe kukutamandani.

15Pakamwa panga padzalankhula tsiku lonse

za ntchito zanu zolungama ndi za chipulumutso chanu,

popeza kuti sindidziŵa chiŵerengero chake.

16Ndidzabwera ndi uthenga

wofotokoza za ntchito zamphamvu za Chauta.

Ndidzatamanda chilungamo chanu chokha.

17Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga,

ndipo ndikulalikabe ntchito zanu zodabwitsa.

18Choncho Inu Mulungu, musandisiye ndekha

ngakhale pamene ndakalamba ndipo imvi zili mbu,

mpaka nditalalika mphamvu zanu

kwa mibadwo yonse yakutsogolo.

19Mphamvu zanu ndi kulungama kwanu,

zimafikira mpaka kumwambamwamba.

Pali yani wofanafana nanu, Inu Mulungu,

amene mwachita zazikulu?

20Mudzanditsitsimutsanso

Inu amene mwandiwonetsa mavuto ambiri oŵaŵa,

mudzanditulutsanso m'dzenje lozama la pansi pa nthaka.

21Inu mudzaonjezera ulemu wanga

ndipo mudzandisangalatsanso.

22Ndidzakutamandaninso ndi zeze, Inu Mulungu wanga,

chifukwa cha kukhulupirika kwanu.

Ndidzaimba nyimbo zoyamika Inu ndi pangwe,

Inu Woyera wa Israele.

23Pakamwa panga padzafuula ndi chimwemwe,

pamene ndikukuimbirani nyimbo zotamanda.

Nawonso mtima wanga umene mwauwombola,

udzaimba moyamika.

24Tsiku lonse ndidzasimba za kulungama kwanu,

pakuti amene ankafuna kundichita choipa,

aŵachititsa manyazi ndipo aŵanyazitsa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help