1“Ndithudi, ulipo mgodi wa siliva,
alipo malo oyengerapo golide.
2Chitsulo amachikumba pansi,
mkuŵa amachita kuusungunula ku miyala yamkuŵa.
3Anthu amaloŵa mu mdima atatenga nyale
namafunafuna miyalayo mpaka ku malire a mgodiwo,
akuyenda mu mdima wandiweyani.
4Amakumba njira zapansi mumgodimo,
kutali ndi kumene kumakhala anthu,
mpaka kuiŵalika ndi anthu onka nayenda,
amakhala ali lende pansipo, namazunguzika uku ndi uku.
5Nthaka imatulutsa chakudya,
koma kunsi kwake kumachita ngati kofwantchuka ndi moto.
6Miyala yamumgodimo ndi ya safiro,
mulinso fumbi la golide.
7“Njira ya mu mgodi imeneyi,
palibe mbalame yodya zinzake imene imaidziŵa,
kamtema yemwe sanaiwone.
8Zilombo zolusa sizinapondemo m'njiramo.
Mkango sunadzeremo m'menemo.
9“Anthu amaphwanya matanthwe olimba,
amagadabula mapiri kuyambira m'tsinde.
10Amasema mipita m'matanthwemo,
ndipo amatulutsamo miyala ya mtengo wapatali.
11Amaletsa mitsinje yapansipo kuti isayende,
motero amaonetsa poyera zinthu zobisika.
12 Mphu. 1.6; Bar. 3.15 “Koma nzeru zingapezeke kuti?
Luntha lingapezeke kuti?
13 Bar. 3.29-31 Anthu sadziŵa kufunika kwake kwa nzeruzo,
ndipo sizipezeka pa dziko lino lapansi.
14Phompho likuti, ‘Sizipezeka mwa ine muno,’
nyanja ikuti, ‘Mwa ine munonso ai.’
15Nzeru sangazipate ndi golide,
mtengo wake sangauyerekeze ndi siliva wambiri.
16Ngakhale golide wokoma kwambiri
wa ku Ofiri sangafike pa mtengo wa nzeruzo,
miyala ya onikisi kapena ya safiro
nayonso singafikepo.
17Golide ndi mwala wagalasi
sizingakwanire kuti agulire nzeru.
Nzeru sangazisinthanitse ndi
zokometsera za golide weniweni.
18Mtengo wake wa nzeru ndi woposa
miyala ya korali ndi krisitala,
umapambananso ndi miyala ya rubi yomwe.
Mtengo wake wa nzeru umapambana ndi ngale zomwe.
19Miyala ya topazi ya ku Etiopiya
sungaiyerekeze ndi nzeru,
ngakhale golide wabwino kwambiri sangafikepo pa nzeru.
20“Kodi tsono nzeru zimachokera kuti?
Nkuti kumene tingapeze luntha?
21Malo ake ndi obisika kwa zamoyo zonse,
ndi obisikanso kwa mbalame zamumlengalenga.
22Ngakhale malo a chiwonongeko
ndiponso imfa zimangoti,
‘Tidangomva mphekesera chabe ya zimenezo.’
23 Bar. 3.35-37 “Mulungu yekha ndiye amadziŵa
njira yake yopita kumeneko,
amadziŵa kumene nzeruzo zimakhala.
24Paja Iye amayang'ana mpaka
ku mathero a dziko lapansi,
amaona zonse zimene zili kunsi kwa thambo.
25Pamene Iye adapatsa mphepo mphamvu zake,
nayesa kuzama kwa nyanja,
26pamene adakhazika lamulo loti mvula izigwa,
nakonza njira za ching'aning'ani cha bingu,
27 Mphu. 1.9, 19 pamenepo mpamene adaona nzeruzo naziyesa mtengo wake,
ndipo adazikhazikitsa ndi kuzisanthula bwino lomwe.
28 Mas. 111.10; Miy. 1.7; 9.10 Choncho adauza munthu kuti,
‘Kuwopa Ambuye ndiye nzeru zimenezo,
kuthaŵa zoipa ndiye luntha limenelo.’ ”
Yobe
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.