1Ife amene tili ndi chikhulupiriro champhamvu, tiziŵalezera mtima anthu ofooka, osamangodzikondweretsa tokha.
2Aliyense mwa ife azikondweretsa mnzake, ndi kumchitira zabwino, kuti alimbikitse chikhulupiriro chake.
3Mas. 69.9 Pakuti Khristunso sankachita zinthu kungofuna kudzikondweretsa, koma ndi monga Malembo anenera kuti, “Chipongwe cha anthu okunyozani Inu chidafika pa Ine.”
41Am. 12.9; 2Am. 15.9Zonse zolembedwa m'Malembo kale, zidalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembowo amatilimbikitsa ndi kutithuzitsa mtima, kuti tizikhala ndi chiyembekezo.
5Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu,
6akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.
Uthenga Wabwino ndi wokhaliranso anthu a mitundu ina7Tsono muzilandirana monga momwe Khristu adakulandirirani inu, kuti Mulungu alemekezedwe.
8Chifukwa kunena zoona, Khristu adasanduka mtumiki wa Ayuda, kutsimikiza kuti Mulungu ndi wokhulupirika. Adatsimikiza kukhulupirikako pakuchita zimene Mulungu adaŵalonjeza makolo ao akale aja,
92Sam. 22.50; Mas. 18.49 ndiponso pakupatsa anthu amene sali Ayuda chifukwa cholemekezera Mulungu kaamba ka chifundo chake. Ndi monga Malembo anenera kuti,
“Nchifukwa chake ndidzakuyamikani
pakati pa anthu a mitundu ina,
ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”
10 Deut. 32.43 Akutinso,
“Inu anthu a mitundu ina,
kondwani pamodzi ndi anthu ake a Mulungu.”
11 Mas. 117.1 Ndiponso akuti,
“Inu nonse a mitundu ina, tamandani Ambuye,
anthu a mitundu yonse amtamande.”
12 Yes. 11.10 Nayenso mneneri Yesaya akuti,
“Mmodzi mwa zidzukulu za Yese adzabwera.
Iye adzadzambatuka kuti alamule anthu a mitundu ina,
ndipo iwo adzaika chikhulupiriro chao pa Iyeyo.”
13Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Chifukwa chiyani Paulo adaŵalembera mwamphamvu chotere14Abale anga, ine mwini wake sindikayika konse kuti ndinu anthu a kufuna kwabwino ndithu, ndinu anthu odziŵa zinthu, ndipo mumatha kulangizana.
15Komabe m'kalata ino zina ndakulemberani mopanda mantha konse, kuti ndikukumbutseni zimenezo. Ndalemba motere popeza kuti Mulungu adandikomera mtima
16pakundipatula kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu a mitundu ina. Adandipatsa ntchito yolalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu ngati wansembe, kuti anthuwo akhale ngati nsembe yokomera Iye ndi yoperekedwa mwa Mzimu Woyera.
17Tsono pokhala ndine wake wa Khristu Yesu, ndikunyadira ntchito imene ndikugwirira Mulungu.
18Sindidzalimba mtima kulankhula za kanthu kena ai, koma zokhazo zimene ndimachita kudzera mwa Khristu, kuti ndithandize anthu a mitundu ina kumvera. Zimenezi ndidazichita ndi mau anga ndi ntchito zanga,
19ndi zizindikiro ndi zozizwitsa zamphamvu zochitika ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Motero Uthenga Wabwino wonena za Khristu ndidaulalika kwathunthu ku Yerusalemu ndi ku dziko lozungulira mpaka ku Iliriko.
20Masiku onse ndinkayesetsa kulalika Uthenga Wabwino kumalo kokhako kumene dzina la Khristu linali lisanamvekebe. Ndinkaopa kumanga pa maziko amene munthu wina adaika.
21Yes. 52.15Paja Malembo akuti
“Anthu amene sadauzidwe za Iye, adzaona,
amene sadamve za Iye, adzamvetsa.”
Paulo aganiza zopita ku Roma22 Aro. 1.13 Pa chifukwa chimenechi ndidalephera kaŵirikaŵiri kufika kwanuko.
23Zaka zambiri ndakhala ndikulakalaka kuti ndifike kumeneko. Ndipo tsopano, popeza kuti ndatsiriza ntchito yanga ku mbali zakuno,
24ndikuyembekeza kudzakuwonani pamene ndidzadzera kwanuko popita ku Spaniya. Ndidzakondwera kukuchezerani masiku angapo, ndipo pambuyo pake ndifuna kuti mudzandithandize kupitiriza ulendo wanga.
251Ako. 16.1-4Koma tsopanoli ndikupita ku Yerusalemu kukapereka chithandizo kwa anthu a Mulungu kumeneko.
26Pakuti mipingo ya ku Masedoniya, ndi ya ku Akaiya idakoma mtima mpaka kupereka zothandiza osauka pakati pa anthu a Mulungu a ku Yerusalemu.
271Ako. 9.11Inde unali ufulu kuchita zimenezi, komanso unali udindo wao kuthandiza osaukawo. Ayuda adagaŵana madalitso ao achikhristu ndi anthu a mitundu ina, choncho iwowo ayeneranso kuthandiza Ayudawo pa zosoŵa zao za moyo wathupi.
28Tsono nditatsiriza ntchito yangayi, ndi kutula bwino lomwe kwa iwo zoperekazi, ndidzadzera kwanuko popita ku Spaniya.
29Ndikudziŵa kuti ndikadzabwera kumeneko, ndidzabwera ndi madalitso ochuluka a Khristu.
30Tsono ndikukupemphani abale, kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, ndiponso ndi chithandizo cha chikondi chimene Mzimu Woyera amapereka, kuti mugwirizane nane polimbikira kundipempherera kwa Mulungu.
31Mundipempherere kuti Mulungu anditchinjirize, ndisagwe m'manja mwa anthu osakhulupirira am'Yudeya. Mupempherenso kuti anthu a Mulungu a ku Yerusalemu azilandire ndi manja aŵiri zoperekazi zimene ndatumidwa kuti ndikaŵapatse.
32Choncho, Mulungu akalola, ndidzafika kwanuko ndili wokondwa, ndipo ndidzasanguluka pocheza nanu.
33Mulungu amene amapatsa mtendere akhale ndi inu nonse. Amen.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.