1Nthaŵi imeneyo anthu a mitundu ina oyandikana nawo atamva kuti Ayuda adamanganso guwa lansembe, nakonzanso Nyumba ya Mulungu monga m'mene inaliri kale, adapsa mtima kwambiri.
2Adatsimikiza zoti aononge kotheratu anthu onse a fuko la Yakobe amene anali pakati pao. Motero adayambadi kupha anthuwo ndi kuŵaononga.
3Tsono Yudasi adayamba kumenya nkhondo ndi zidzukulu za Esau ku Idumeya ku dziko la Akrabatene, kumene anali atazinga Aisraele. Adaŵapambana, naŵagonjetsa ndi kuŵafunkhira chuma chao.
4Adakumbukiranso kuchimwa kwa ana a Baene, amene ankanyenga ndi kutchera msampha Aisraele, nkumaŵalalira pa njira.
5Adaŵatsekera m'malinga mwao, naŵazinga ndi zithando zankhondo, kufunitsitsa kuti aŵaonongeretu. Adatentha nsanja zao pamodzi ndi onse okhalamo.
6Pambuyo pake adaoloka kukathira nkhondo Aamoni. Kumeneko adapeza chigulu chankhondo champhamvu chotsogoleredwa ndi Timoteo.
7Adamenyana nawo kwambiri, naŵakantha ndi kuŵaononga kotheratu.
8Kenaka adalanda Yazere pamodzi ndi midzi yake yomwe, nabwerera ku Yudeya.
Kukonzekera nkhondo ku Galileya ndi ku Giliyadi9Anthu a mitundu ina okhala ku Giliyadi adasonkhana, kuti akamenye nkhondo ndi Aisraele a m'dziko mwao kuti aŵaononge. Aisraelewo adathaŵira ku linga la ku Datema.
10Kenaka adatumiza kalata kwa Yudasi ndi abale ake yonena kuti, “Anthu a mitundu ina otizungulira asonkhana kuti atiwononge.
11Akonzeka kuti adzalande linga limene tathaŵiramo, ndipo Timoteo ndiye mtsogoleri wao wankhondo.
12Ndiye inu bwerani msanga kudzatipulumutsa kuti angatiwononge, chifukwa ambiri mwa ife adafa.
13Abale athu onse okhala ku dera la Tobe iwonso adaphedwa, akazi ndi ana adaŵatenga kunka nawo ku ukapolo, ndipo chuma chaonso adaŵalanda. Kumeneko adapha anthu okwanira chikwi chimodzi.”
14Pamene Yudasi ankaŵerenga kalatayo, amithenga ena ochokera ku Galileya adafika, zovala zao zili zong'amba. Adanena kuti,
15“Anthu a ku Ptolemaisi, a ku Tiro ndi a ku Sidoni aphatikizana ndi anthu achilendo a ku Galileya kuti atiwononge.”
16Yudasi ndi anthu ake atamva mauthenga ameneŵa, adachita msonkhano waukulu, kuti amvane zoyenera kuchita kuti athandize abale ao ozunzidwa ndi kuthiridwa nkhondo ndi adani ao.
17Yudasi adauza mbale wake Simoni kuti, “Udzisankhire anthu, mukapulumutse abale anu okhala ku Galileya, ine ndi mbale wanga Yonatani tipita ku Giliyadi.”
18Ku Yudeyako adasiya Yosefe mwana wa Zakariya ndi Azariya mtsogoleri wa anthu, pamodzi ndi ankhondo otsala, kuti azilonda dzikolo.
19Adaŵalamula kuti, “Muziŵayang'anira anthu aŵa, koma musayambane nkhondo ndi akunja mpaka titabwera.”
20Simoni adampatsa anthu zikwi zitatu kuti apite nawo ku Galileya, Yudasi natenga anthu zikwi zisanu ndi zitatu kupita nawo ku Giliyadi.
Maulendo a ku Galileya ndi ku Giliyadi21Tsono Simoni adapita ku Galileya. Kumeneko adamenyana nkhondo ndi akunja ambiri naŵabalalitsa.
22Adaŵalondola mpaka ku chipata cha mzinda wa Ptolemaisi. Anthu akunja amene adaphedwa pa nkhondoyo anali okwanira 3,000, ndipo Ayuda adafunkha chuma chao.
23Adatenga Ayuda okhala ku Galileya ndi ku Aribata pamodzi ndi akazi ao ndi ana ao, ndi chuma chao chonse. Adabwera nawo ku Yudeya ali okondwa kwambiri.
24Pa nthaŵi imeneyo nayenso Yudasi Makabeo ndi mbale wake Yonatani adaoloka Yordani, nayenda masiku atatu m'chipululu.
25Adakumana ndi Anabate. Iwowo adaŵalandira mwaubwenzi, naŵafotokozera zonse zimene zidaachitikira abale ao okhala ku Giliyadi.
26Adati, “Ambiri mwa iwo adazingidwa ku Bozira, Bosora, Alema, Kasifo, Makedi ndi ku Karinaimu, mizinda yaikulu ndi yamalinga.
27Enanso adazingidwa ku mizinda ina ya ku Giliyadi. Ndipo adani ao adakonzeka kuti athire nkhondo mizindayo m'maŵa mwake, kuti ailande ndi kupha anthu onse am'menemo pa tsiku limodzi.”
28Yudasi ndi gulu lake lankhondo adadzera njira ya ku chipululu mpaka ku Bozira. Adamenya nkhondo nalanda mzindawo, ndipo adapha amuna onse. Atafunkha chuma chao, adautentha mzindawo.
29Adachoka kumeneko usiku, nayenda mpaka kukafika ku mzinda wamalinga wa Datema.
30M'maŵa kutacha, poyang'ana, adaona anthu ambirimbiri atanyamula makwerero ndi makina ankhondo, kuti alande mzindawo ndi kumenya nkhondo ndi Ayuda okhala m'katimo.
31Yudasi adaona kuti nkhondo yayambika kale, ndipo mumzindamo mukumveka phokoso, kulira kwa malipenga ndi kufuula kwa anthu.
32Choncho adauza anthu a gulu lake kuti, “Lero mumenye nkhondo chifukwa cha abale anu.”
33Tsono adagaŵa anthuwo m'magulu atatu, nasendera kwa adani cha kumbuyo kwao, akuliza malipenga ndi kupemphera mokweza mau.
34Ankhondo a Timoteo, atazindikira kuti ndi Yudasi Makabeo, adathaŵa, iyeyo nkuŵakantha ndithu. Motero anthu okwanira 8,000 adaphedwa pa nkhondoyo tsiku limenelo.
35Pochoka apo Yudasi adapita ku Alema, nakathiranso nkhondo kumeneko, nkulanda mzindawo. Adapha amuna onse, adafunkha chuma chao natentha mzinda wao.
36Kutha pamenepo adapitirira, nakalanda Kasifo, Makedi, Bosora ndi mizinda ina ya ku Giliyadi.
37Pambuyo pake Timoteo adasonkhanitsa gulu linanso lankhondo, namanga zithando zankhondo poyang'anana ndi Rafoni, patsidya pa mfuleni.
38Yudasi adatuma anthu kuti akazonde gululo, ndipo okazondawo adadzamuuza kuti, “Anthu a mitundu ina onse otizungulira aphatikizana ndi ankhondo a Timoteo, apanga chigulu chachikulu zedi.
39Adalembanso Arabu kuti aŵathandize pa nkhondoyo. Adamanga zithando zao zankhondo patsidya pa mfuleni, atakonzeka kuti amenyane nawe.” Pamenepo Yudasi adasendera kuti akumane nawo.
40Timoteo adauza atsogoleri ake ankhondo kuti, “Akayamba ndi Yudasi ndi anthu ake kuwoloka mfuleni, sititha kuŵaletsa, ndipo tipambana.
41Koma akaopa kuwoloka, ndipo akamanga zithando zao zankhondo patsidya pa mfuleni, tidzaoloka ndife kukakumana nawo, ndipo tidzampambana.”
42Yudasi atafika kumfuleniko, adaika akulu ankhondo m'mbali mwa mfuleni, naŵalamula kuti, “Musalole munthu ndi mmodzi yemwe kuti amange hema lake kuno, koma onse apite ku nkhondo.”
43Tsono adayamba ndiye kuwolokera kwa adani, anthu ake onse nkumutsata. Adaŵagonjetsa akunja aja, ndipo iwowo adataya zida zao nathaŵira ku malo opembedzerako mafano a ku Karinaimu.
44Koma Yudasi adalanda mzindawo, natentha nyumba ya mulungu wao ndi onse okhalamo. Choncho anthu a ku Karinaimu adagonja, osatha kumenyana naye Yudasi.
45Pambuyo pake Yudasi adasonkhanitsa Aisraele onse a ku Giliyadi, kuti aŵabwezere onse ku Yudeya. Chinali chinamtindi cha anthu, otsika ndi otchuka omwe, pamodzi ndi akazi ao ndi ana ao. Onsewo anali atatenga katundu wao yense.
46Anthu ameneŵa Yudasi adafika nawo ku Efuroni. Umenewu unali mzinda waukulu wa linga lolimba, wa m'mbali mwa mseu. Sadathe kuulambalala chakumanja kapena chakumanzere, ankayenera kudzera pakati pake basi.
47Koma anthu amumzindamo adaŵatsekera njira nakundika miyala pa chipata. Yudasi adaŵatumizira mau amtendere.
48Adati, “Ife tikungofuna kudzeramo chabe m'dziko mwanumu, tikubwerera kwathu. Palibe amene akuvuteni, tingodutsa chabe.” Koma iwowo adakana ndithu kumtsekulira.
49Pamenepo Yudasi adalamula anthu akewo kuti amange mahema ao pomwe adaaimapo.
50Ankhondo ake adakonza mizere yao, ndipo Yudasi adalamula kuti authire nkhondo mzindawo. Adamenyana nkhondo usana ndi usiku, ndipo Mulungu adaupereka mzindawo m'manja mwao.
51Adapha amuna onse pankhondopo, nagumula mzindawo ndi kufunkha chuma chake chonse. Kenaka adadzera pakati pake akuponda pa mitembo ya adaniwo.
52Tsono adaoloka Yordani nakafika ku chigwa chachikulu choyang'anana ndi Betisane.
53Yudasi ankaŵafulumiza anthu okhala m'mbuyo ndi kuthandiza anthu ake njira yonse, mpaka adakafika ku dziko la Yudeya.
54Adakwera phiri la Ziyoni mosangalala ndi mokondwa, napereka nsembe zopsereza, chifukwa onsewo anali atabwerera bwino, osataya ndi mmodzi yemwe mwa abale ao.
55Nthaŵi imene Yudasi ndi Yonatani anali ku dziko la Giliyadi, ndipo Simoni mbale wao anali ku Galileya mbali ya ku Ptolemaisi,
56Yosefe, mwana wa Zakariya, ndipo Azariya mtsogoleri wa ankhondo, adaamva za zazikulu zimene anzao aja adaazichita pomenya nkhondo zao.
57Tsono iwo adati, “Ifenso tiyeni tibukitse mbiri yathu, tiyeni tikamenye nkhondo ndi anthu a mitundu ina otizungulira.”
58Motero adatenga magulu ao ankhondo, napita kukamenya nkhondo ku Yaminiya.
59Tsono Gorjiyasi adatuluka mumzindamo ndi anthu ake napita kuti akakumane nawo.
60Yosefe ndi Azariya adagonjetsedwa, ndipo adani adaŵathamangitsa mpaka ku malire a Yudeya. Tsiku limenelo adaphedwa Aisraele okwanira zikwi ziŵiri.
61Choncho Aisraele adathyoledwa kwambiri chifukwa iwo sadamvere Yudasi ndi abale ake, naganiza kuti iwonso adzakhoza kuchita zazikulu zotchukitsa mbiri yao.
62Koma sanali a mtundu wa anthu amene Mulungu adaaŵapatsa mphamvu ya kupulumutsa Aisraele.
Apambana ku Idumeya ndi ku Filistiya63Yudasi ndi abale ake anali ndi ulemerero waukulu pakati pa Aisraele onse ndiponso pakati pa anthu a mitundu ina amene adaamva maina ao.
64Anthu ankadzasonkhana kwa iwo kuti aŵatamande.
65Pambuyo pake Yudasi ndi abale ake adapita kukamenya nkhondo ndi zidzukulu za Esau, m'dziko lakumwera. Adagonjetsa Hebroni ndi midzi yake, nagumula malinga ake, nkutentha nsanja zankhondo zokhala kumeneko.
66Pambuyo pake adanyamuka kumeneko kupita ku dziko la Afilisti, nakabzola ku Marisa.
67Pa tsiku limenelo ansembe ena adaphedwa ku nkhondo, chifukwa adaafuna kuwonetsa chamuna chao, nadziponya mopanda nzeru pakati pa nkhondo.
68Tsono Yudasi adapita ku Azoto ku dziko la Afilisti. Adagwetsa maguwa ao natentha mafano a milungu yao. Kenaka atafunkha chuma cha m'mizinda yao, adabwerera ku dziko la Yudeya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.