Miy. 24 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Usamachitira nsanje anthu ochimwa,

kapena kumalakalaka kuti uzimvana nawo,

2chifukwa mitima yao imalingalira zandeu,

ndipo pakamwa pao pamalankhula zoutsa mavuto.

3Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru,

ndipo imakhazikika ndi anthu a mtima wodziŵa zinthu.

4Wodziŵa zinthu angathe kudzaza zipinda zake

ndi chuma chokondweretsa ndi cha mtengo wapatali.

5Munthu wanzeru ndi wamphamvu

kupambana munthu wa nyonga zambiri,

munthu wophunzira amaposa munthu wamphamvu.

6Pafunika malangizo abwino kuti ukamenye nkhondo.

Aphungu akachuluka, kupambana kuli pomwepo.

7Nzeru ndi yapatali kwambiri kwa munthu wopusa,

alibe chonena pa bwalo lamilandu.

8Amene amakonzekera kuchita choipa,

adzatchedwa mvundulamadzi.

9Kukonzekera zopusa nkuchimwa,

munthu wonyoza amanyansa anthu.

10Ukataya mtima pamene upeza zovuta,

ndiye kuti mphamvu zako ndi zochepa.

11Uŵapulumutse amene akutengedwa kuti akaphedwe.

Uŵalanditse amene akuyenda movutikira

popita kukaŵapha.

12Ukanena kuti, “Ife sitidazidziŵe zimenezi,”

kodi iye amene amayesa mtima, zimenezi saziwona?

Kodi amene amayang'anira moyo wako sazidziŵa?

Kodi sadzambwezera munthu potsata ntchito zake?

13Mwana wanga, uzidya uchi poti ndi wabwino,

madzi a m'chisa cha njuchi ndi ozuna ukaŵalaŵa.

14Udziŵe kuti nzeru ndi yoteronso mumtima mwako.

Ukaipeza, zinthu zidzakuyendera bwino m'tsogolo,

ndipo chikhulupiriro chako sichidzakhala chachabe.

15Nyumba ya munthu wabwino usaichite zachifwamba

ngati munthu woipa mtima,

usachite nayo nkhondo nyumba yake.

16Munthu wabwino amagwa kasanunkaŵiri,

koma amadzukirira ndithu,

m'menemo anthu oipa tsoka limaŵagwera chonse.

17Usamakondwerera kugwa kwa mdani wako,

mtima wako usamasangalala iyeyo akaphunthwa.

18Ukatero Chauta adzaziwona zimenezo nadzaipidwa nazo,

kenaka adzaleka kumkwiyira mdani wakoyo.

19Usamavutika chifukwa cha anthu ochita zoipa,

usachite nawo nsanje anthu oipa.

20Pajatu munthu woipa

zinthu sizidzamuyendera bwino m'tsogolo,

moyo wa anthu oipa adzauzima ngati nyale.

21Mwana wanga, uziwopa Chauta ndiponso mfumu,

usagwirizane ndi anthu okonda kuŵachitira mwano.

22Ameneŵa amatha kugwetsa tsoka mwadzidzidzi,

ndani angadziŵe kuwopsa kwa chiwonongeko

chochokera kwa aŵiriŵa?

Malangizo enanso a anthu anzeru

23Enanso ndi aŵa malangizo a anthu anzeru:

Kukondera pozenga milandu si chinthu chabwino.

24Amene amauza munthu woipa kuti, “Ndiwe wosalakwa,”

anthu adzamtemberera,

ndipo mitundu ya anthu idzaipidwa naye.

25Koma aweruzi amene amalanga anthu oipa adzapeza bwino,

ndipo adzakhala ndi madalitso ambiri.

26Munthu woyankha zoona

ndiye amaonetsa chibwenzi chenicheni.

27Ukonzeretu ntchito zako zonse makamaka zakumunda,

pambuyo pake mpamene ungayambe kumanga nyumba.

28Usakhale mboni yotsutsa mnzako popanda chifukwa,

pakamwa pako pasamanena zonama.

29Usamanena kuti, “Ndidzamchitira

monga momwe iye wandichitira ine,

ndidzamlipsira chifukwa cha zomwe iye

wandichitira ine.”

30Ndinkayenda m'mbali mwa munda wa munthu waulesi,

m'mbali mwa munda wamphesa wa munthu wopanda nzeru.

31M'minda monsemo munali mutamera minga yokhayokha,

m'nthaka imeneyo munali mutamera khwisa,

ndipo mpanda wake wamiyala unali utagwa.

32Tsono nditaona, ndidayamba kuganizirapo pa zimenezo,

nditayang'ana, ndidatolapo phunziro ili:

33 Miy. 6.10, 11 Ukati, “Taimani ndigoneko pang'ono,”

kapena “Ndiwodzereko chabe,”

kapena “Ndingopumulako pang'ono,”

34umphaŵi udzakufikira monga mbala,

kusauka kudzakupeza ngati mbala yachifwamba.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help