Yob. 25 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Apo Bilidadi wa ku Suki adayankha kuti,

2“Mulungu ali ndi ulamuliro wonse,

ndipo anthu onse ayenera kumuwopa.

Akusungitsa mtendere mu ufumu wake Kumwambamwambako.

3Kodi magulu ake ankhondo akumwamba ndi oŵerengeka?

Kodi kuŵala kwake sikuŵala paliponse?

4Kodi alipo munthu wosachimwa pamaso pa Mulungu?

Kodi munthu wobadwa mwa mkazi

angakhale bwanji wosapalamula?

5Ngati mwezi sutha kupereka kuŵala kwenikweni,

ndipo ngati nyenyezi sizitha kunyezemira pamaso pake,

6nanji tsono munthu amene ali ngati mphutsi chabe,

nanji mwana wa munthu amene ali ngati

nyongolotsi yam'dothi?”

Yobe

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help