1 Yak. 4.13-16 Usamanyadira zamaŵa,
pakuti sudziŵa zimene zidzachitika pa tsikulo.
2Akutame ndi wina, osati pakamwa pako pomwe,
wosadziŵana naye akakutamanda, apo ndipo.
3Mwala ndi wolemera, ndipo mchenganso
ndi wolemera kwambiri,
koma makani a chitsiru ndi oposa zonsezo kulemera kwake.
4Mkwiyo umadzetsa nkhanza,
kupsa mtima kumachititsa zoopsa,
koma nsanje imabweretsa zoipa zopambana.
5Kudzudzula munthu poyera nkwabwino
kupambana kubisa chikondi chimene uli nacho.
6Amene amakukonda, ngakhale akupweteke,
chikondi chake chimakhalapobe,
mdani wako ngakhale akumpsompsone,
nkunyenga chabe kumeneko.
7Wokhuta amaipidwa ndi chisa cha uchi,
koma kwa munthu wanjala
ndi zoŵaŵa zomwe zimatsekemera.
8Munthu amene wasokera kutali ndi kwao,
ali ngati mbalame yosokera kutali ndi chisa chake.
9Mafuta ndi zonunkhira zimasangalatsa mtima,
koma kukoma kwa bwenzi kwagona pa malangizo ake.
10Usasiye bwenzi lako ndiponso bwenzi la atate ako.
Usachite kupita ku nyumba ya mbale wake,
ukakhala pa mavuto.
Mnzako wokhala naye pafupi
amaposa mbale wako wokhala kutali.
11Mwana wanga, ukhale ndi nzeru, ukondwetse mtima wanga,
kuti choncho ndithe kumuyankha amene amandinyoza.
12Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala,
koma wopusa amangopitirira ndipo amanong'oneza bondo.
13Munthu amene waperekera mlendo chikole,
umlande chovala chake,
chimenecho chikhale chigwiriro chako,
chifukwa chakuti waperekera chikole mlendo wosadziŵika.
14Wopatsa mnzake moni mofuula m'mamaŵa kwambiri,
adzamuyesa kuti akutemberera.
15Mkazi wolongolola ndi wotopetsa
ngati mvula ya mvumbi.
16Kuyesa kumletsa mkazi woteroyo
kuli ngati kuyesa kuletsa mphepo,
kapena kuyesa kufumbata mafuta m'manja.
Munthu sakhutitsidwa17Chitsulo amachinola nchitsulo chinzake,
chonchonso munthu amasulidwa ndi munthu mnzake.
18Amene amasamalira mkuyu adzadya zipatso zake,
chonchonso amene amasamalira mbuyake adzalandira ulemu.
19Monga momwe nkhope imaonekera m'madzi,
momwemonso mtima wa munthu umadziŵika ndi zochita zake.
20Manda sakhuta,
nawonso maso a munthu sakhuta.
21Siliva amasungunulira mu uvuni,
golide amasungunulira m'ng'anjo,
chonchonso munthu amayesedwa ndi mbiri yake.
22Chitsiru ngakhale uchisinje mu mtondo ndi munsi
pamodzi ndi chimanga,
kupusa kwake sikudzachoka konse.
23Uzidziŵe bwino nkhosa zako m'mene ziliri,
ndipo usamalire ziŵeto zako.
24Paja chuma sichikhala mpaka muyaya.
Kodi ufumu umakafika mpaka ku mibadwo yonse?
25Udzu ukatha, msipu nkuphuka,
ndipo atatuta udzu wakumapiri,
26anaankhosa adzakupatsa chovala, ndi ubweya wao,
ndipo pogulitsa mbuzi udzapeza chogulira munda.
27Udzakhala ndi mkaka wambiri wa mbuzi kuti uzidya,
iweyo ndi banja lako,
ndiponso ndi adzakazi ako omwe.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.